bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Jeremiah 32
Jeremiah 32
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 33 →
1
Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova chaka chakhumi cha Zedekiya mfumu ya Yuda, chimene chinali chaka chakhumi ndi chisanu ndi chitatu cha Nebukadinezara.
2
Nthawi yomweyo nkhondo ya mfumu ya Babiloni inamangira Yerusalemu misasa; ndipo Yeremiya mneneri anatsekeredwa m'bwalo la kaidi, linali kunyumba ya mfumu ya Yuda.
3
Pakuti Zedekiya mfumu ya Yuda inamtsekera iye, nati, Chifukwa chanji ulinkunenera, kuti, Yehova atero, Taonani, ndidzapereka mudzi uwu m'dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo iye adzaulanda,
4
ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda sadzapulumuka m'dzanja la Ababiloni, koma adzaperekedwadi m'dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo adzanena ndi iye pakamwa ndi pakamwa, ndipo adzaonana maso ndi maso;
5
ndipo adzatsogolera Zedekiya kunka ku Babiloni, ndipo adzakhala komwe kufikira ndidzamzonda, ati Yehova: ngakhale mudzamenyana ndi Ababiloni, simudzapindula konse?
6
Ndipo Yeremiya anati, Mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,
7
Taonani, Hanamele mwana wa Salumu mbale wa atate wako adzadza kwa iwe, kuti, Ugule munda wanga uli ku Anatoti; pakuti mphamvu yakuombola ndi yako kuugula.
8
Ndipo Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga anadza kwa ine m'bwalo la kaidi monga mwa mau a Yehova, nati kwa ine, Gulatu munda wanga, wa ku Anatoti, m'dziko la Benjamini; pakuti mphamvu yakulowa ndi yakuombola ndi yako; udzigulire wekha. Pamenepo ndinadziwa kuti awa ndi mau a Yehova.
9
Ndipo ndinagula mundawo wa ku Anatoti kwa Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga, ndimyesera ndalama, masekeli khumi ndi asanu ndi awiri a siliva.
10
Ndipo ndinalemba chikalatacho, ndichisindikiza, ndiitana mboni zambiri, ndiyesa ndalama m'miyeso.
11
Ndipo ndinatenga kalata wogulira, wina wosindikizidwa, monga mwa lamulo ndi mwambo, ndi wina wovundukuka;
12
ndipo ndinapereka kalata wogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, mwana wa Maseiya, pamaso pa Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga, ndi pamaso pa mboni zimene zinalemba pa kalata wogulirayo, pamaso pa Ayuda onse okhala m'bwalo la kaidi.
13
Ndipo ndinauza Baruki pamaso pao, kuti,
14
Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero; Tenga akalata awa, kalata uyu wogulira, wosindikizidwa, ndi kalata uyu wovundukuka, nuwaike m'mbiya yadothi; kuti akhale masiku ambiri.
15
Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Nyumba ndi minda ndi minda yamphesa idzagulidwanso m'dziko muno.
16
Ndipo nditapereka kalata wogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, ndinapemphera kwa Yehova, kuti,
17
Ha! Yehova Mulungu, taonani, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi mphamvu yanu yaikulu ndi mkono wanu wotambasuka; palibe chokanika Inu;
18
amene muchitira chifundo anthu zikwi; nimubwezera mphulupulu ya atate m'chifukwa cha ana ao a pambuyo pao, dzina lake ndi Mulungu wamkulu, wamphamvu, Yehova wa makamu;
19
wamkulu m'upo, wamphamvu m'ntchito; maso anu ali otsegukira njira zonse za ana a anthu; kuti mupatse yense monga mwa chipatso cha machitidwe ake;
20
amene munaika zizindikiro ndi zodabwitsa m'dziko la Ejipito, mpaka lero lomwe, m'Israele ndi mwa anthu ena; nimunadzitengera mbiri, monga lero lomwe;
21
ndipo munatulutsa anthu anu Israele m'dziko la Ejipito ndi zizindikiro, ndi zodabwitsa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mantha ambiri;
22
ndipo munawapatsa iwo dziko ili, limene munalumbirira makolo ao kuti mudzawapatsa, dziko moyenda mkaka ndi uchi;
23
ndipo analowa, nakhalamo; koma sanamvere mau anu, sanayende m'chilamulo chanu; sanachite kanthu ka zonse zimene munawauza achite; chifukwa chake mwafikitsa pa iwo choipa chonsechi;
24
taonani mitumbira, yafika kumudzi kuugwira, ndipo mudzi uperekedwa m'dzanja la Ababiloni olimbana nao, chifukwa cha lupanga, ndi chifukwa cha njala, ndi chifukwa cha chaola; ndipo chimene munachinena chaoneka; ndipo, taonani, muchiona.
25
Ndipo Inu Yehova Mulungu mwati kwa ine, Udzigulire munda ndi ndalama, nuitane mboni; koma mudzi waperekedwa m'manja a Ababiloni.
26
Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, kuti,
27
Taona, Ine ndine Yehova, Mulungu wa anthu onse; kodi kuli kanthu kondilaka Ine?
28
Chifukwa chake Yehova atero: Taona, ndidzapereka mudziwu m'dzanja la Ababiloni, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzaulanda,
29
ndipo Ababiloni, olimbana ndi mudzi uwu, adzafika nadzayatsa mudziwu, nadzautentha, pamodzi ndi nyumba, zimene anafukizira Baala, pa machitidwe ao, ndi kutsanulirira milungu ina nsembe zothira, kuti autse mkwiyo wanga.
30
Pakuti ana a Israele ndi ana a Yuda anachita zoipa zokhazokha pamaso panga chiyambire ubwana wao, pakuti ana a Israele anandiputa Ine kokhakokha ndi ntchito ya manja ao, ati Yehova.
31
Pakuti mudzi uwu unali woutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga kuyambira tsiku lija anaumanga mpaka lero, kuti ndiuchotse pamaso panga;
32
chifukwa cha zoipa zonse za ana a Israele ndi za ana a Yuda, zimene anandiputa nazo Ine, iwowo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, aneneri ao, ndi anthu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu.
33
Ndipo anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope, ngakhale ndinawaphunzitsa, kuuka m'mamawa ndi kuwaphunzitsa, koma sanamvere kulangizidwa.
34
Koma anaika zonyansa zao m'nyumba yotchedwa dzina langa, kuti aidetse.
35
Ndipo anamanga misanje ya Baala, ili m'chigwa cha mwana wake wa Hinomu, kuti apitirize kumoto ana ao aamuna ndi aakazi chifukwa cha Moleki; chimene sindinauza, chimene sichinalowa m'mtima mwanga, kuti achite chonyansa ichi, chochimwitsa Yuda.
36
Chifukwa chake tsopano atero Yehova, Mulungu wa Israele, za mudzi umene, munena inu, waperekedwa m'dzanja la mfumu ya Babiloni ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola:
37
Taonani, ndidzawasokolotsa m'maiko monse, kumene ndinawapirikitsira ndi mkwiyo wanga, ndi m'kupsa mtima kwanga, ndi mu ukali waukulu, ndipo ndidzawabwezeranso kumalo kuno, ndipo ndidzawakhazikitsa mokhulupirika,
38
ndipo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao;
39
ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi ndi njira imodzi, kuti andiope Ine masiku onse; kuwachitira zabwino, ndi ana ao pambuyo pao;
40
ndipo ndidzapangana nao pangano lamuyaya, kuti sindidzawachokera kuleka kuwachitira zabwino; koma ndidzalonga kuopsa kwanga m'mitima yao, kuti asandichokere.
41
Inde, ndidzasekerera iwo kuwachitira zabwino, ndipo ndidzawaoka ndithu m'dziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse.
42
Pakuti atero Yehova: Monga ndatengera anthu awa choipa chonsechi, chomwecho ndidzatengera iwo zabwino zonse ndawalonjeza.
43
Ndipo minda idzagulidwa m'dziko lino, limene muti, Ndilo bwinja, lopanda munthu kapena nyama; loperekedwa m'dzanja la Ababiloni.
44
Anthu adzagula minda ndi ndalama, adzalembera akalata ogulira, adzawasindikiza, adzaitana mboni, m'dziko la Benjamini, ndi m'malo ozungulira Yerusalemu, ndi m'midzi ya Yuda, ndi m'midzi ya kumtunda, ndi m'midzi ya kuchidikha, ndi m'midzi ya kumwera; pakuti ndidzabweza undende wao, ati Yehova.
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 33 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52