bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Jeremiah 29
Jeremiah 29
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 30 →
1
Amenewa ndi mau a kalata uja anatumiza Yeremiya mneneri kuchokera ku Yerusalemu kunka kwa akulu otsala a m'nsinga, ndi kwa ansembe, ndi kwa aneneri, ndi kwa anthu onse, amene Nebukadinezara anawatenga ndende ku Yerusalemu kunka ku Babiloni;
2
anatero atachoka ku Yerusalemu Yekoniya mfumu ndi amake a mfumu ndi adindo ndi akulu a Yuda ndi a ku Yerusalemu, ndi amisiri, ndi achipala,
3
anatumiza kalatayo m'dzanja la Elasa mwana wake wa Safani, ndi Gemariya mwana wake wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya Yuda anawatuma ku Babiloni kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, kuti,
4
Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, kwa am'nsinga onse, amene ndinawatenga ndende ku Yerusalemu kunka nao ku Babiloni:
5
Mangani nyumba, khalani m'menemo; limani minda, idyani zipatso zake;
6
tengani akazi, balani ana aamuna ndi aakazi; kwatitsani ana anu amuna, patsani ananu akazi kwa amuna, kuti abale ana aamuna ndi aakazi; kuti mubalane pamenepo musachepe.
7
Nimufune mtendere wa mudzi umene ndinakutengerani am'nsinga, nimuwapempherere kwa Yehova; pakuti mwa mtendere wake inunso mudzakhala ndi mtendere.
8
Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Aneneri anu ndi akuombeza anu amene akhala pakati panu, asakunyengeni inu, musamvere maloto anu amene mulotetsa.
9
Pakuti anenera kwa inu zonama m'dzina langa; sindinatuma iwo, ati Yehova.
10
Pakuti Yehova atero, kuti, Zitapita zaka makumi asanu ndi awiri pa Babiloni, ndidzakuyang'anirani inu, ndipo ndidzakuchitirani inu mau anga abwino, ndi kubwezera inu kumalo kuno.
11
Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.
12
Pamenepo mudzandiitana Ine, ndipo mudzanka ndi kupemphera kwa Ine, ndipo ndidzakumverani inu.
13
Ndipo mudzandifuna Ine, ndi kundipeza, pamene mundifuna ndi mtima wanu wonse.
14
Ndipo ndidzapezedwa ndi inu, ati Yehova, ndidzabwezanso undende wanu, ndipo ndidzasonkhanitsa inu kwa mitundu yonse, ndi kumalo konse kumene ndinakupirikitsirani inu, ati Yehova; ndipo ndidzakubwezeraninso kumalo kumene ndinakutengani inu andende.
15
Pakuti mwati, Yehova watiutsira ife aneneri m'Babiloni.
16
Pakuti Yehova atero za mfumu imene ikhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi za anthu onse amene akhala m'mudzi uno, abale anu amene sanatulukire pamodzi ndi inu kundende;
17
Yehova wa makamu atero: Taonani, ndidzatuma pa iwo lupanga, ndi njala, ndi chaola, ndipo ndidzayesa iwo onga nkhuyu zoola, zosadyeka, pokhala nzoipa.
18
Ndipo ndidzatsata iwe ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola, ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko la pansi, akhale chitemberero, ndi chodabwitsa, ndi chotsonyetsa, ndi chitonzo, kwa mitundu yonse kumene ndinawapirikitsirako;
19
chifukwa sanamvere mau anga, ati Yehova, amene ndinawatumizira ndi atumiki anga aneneri, ndi kuuka mamawa ndi kuwatuma, koma munakana kumva, ati Yehova.
20
Pamenepo tamvani inu mau a Yehova, inu nonse a m'ndende, amene ndachotsa m'Yerusalemu kunka ku Babiloni.
21
Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, za Ahabu mwana wake wa Koliya, ndi za Zedekiya mwana wake wa Maaseiya, amene anenera zonama m'dzina langa: Taonani, Ndidzawapereka m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni; ndipo iye adzawapha pamaso panu;
22
ndipo am'nsinga onse a Yuda amene ali m'Babiloni adzatemberera pali iwo, kuti, Yehova akuchitire iwe monga Zedekiya ndi Ahabu, amene mfumu ya ku Babiloni inaocha m'moto;
23
chifukwa anachita zopusa m'Israele, nachita chigololo ndi akazi a anansi ao, nanena mau onama m'dzina langa, amene ndinawauza kuti asanene; Ine ndine wodziwa, ndi mboni, ati Yehova.
24
Ndipo za Semaya Mnehelamu uzinena, kuti,
25
Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, kuti, Chifukwa watumiza akalata m'dzina lako iwe mwini kwa anthu onse amene akhala ku Yerusalemu, ndi kwa Zefaniya mwana wake wa Maaseiya wansembe, ndi kwa ansembe onse, kuti,
26
Yehova anakuyesa iwe wansembe m'malo mwa Yehoyada wansembe, kuti iwe ndi anzako mudzakhale akapitao m'nyumba ya Yehova, oyang'anira munthu yense wamisala, wodziyesa mneneri, kuti umuike iye m'zigologolo ndi m'goli.
27
Ndipo tsopano, walekeranji kumdzudzula Yeremiya wa ku Anatoti, amene amadziyesa mneneri wanu,
28
popeza watitumizira mau ku Babiloni, akuti, Undende udzakhalitsa; mangani nyumba, khalani m'menemo; limani minda, idyani zipatso zao?
29
Ndipo Zefaniya wansembe anawerenga kalata amene m'makutu a Yeremiya mneneri.
30
Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, akuti,
31
Uwatumizire mau am'nsinga onse, akuti, Atero Yehova za Semaya Mnehelamu: Chifukwa Semaya wanenera kwa inu, koma Ine sindinamtuma, ndipo anakukhulupiritsani zonama;
32
chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndidzalanga Semaya Mnehelamu, ndi mbeu zake; sadzakhala ndi munthu wakukhala mwa anthu awa, sadzaona zabwino ndidzachitira anthu anga, ati Yehova: chifukwa wanena zopikisana ndi Yehova.
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 30 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52