bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Jeremiah 20
Jeremiah 20
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 21 →
1
Ndipo Pasuri mwana wake wa Imeri wansembe, amene anali kapitao wamkulu m'nyumba ya Yehova, anamva Yeremiya alikunenera zimenezi.
2
Ndipo Pasuri anampanda Yeremiya mneneriyo, namuika matangadza amene anali m'chipata cha kumtunda cha Benjamini, chimene chinali kunyumba ya Yehova.
3
Ndipo panali m'mawa mwake, kuti Pasuri anatulutsa Yeremiya m'matangadzamo. Ndipo Yeremiya anati kwa iye, Yehova sanatche dzina lako Pasuri, koma Magorimisabibu.
4
Pakuti Yehova atero, Taonani, ndidzakuyesa iwe choopsa cha kwa iwe mwini, ndi kwa abwenzi ako onse; ndipo iwo adzagwa ndi lupanga la adani ao, ndipo maso ako adzaona; ndipo ndidzapereka Ayuda onse m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzawatengera iwo am'nsinga ku Babiloni, nadzawapha ndi lupanga.
5
Ndiponso ndidzapereka chuma chonse cha mudzi uwu, ndi zaphindu zake zonse, ndi zinthu zake zonse za mtengo wake, inde, zolemera zonse za mafumu a Yuda ndidzapereka m'manja mwa adani ao, amene adzazifunkha, nadzazitenga kunka nazo ku Babiloni.
6
Ndipo iwe, Pasuri, ndi onse okhala m'nyumba mwako mudzanka kundende; ndipo udzafika ku Babiloni, ndi pamenepo udzafa, ndi pamenepo udzaikidwa, iwe, ndi mabwenzi ako onse, amene unawanenera mabodza.
7
Yehova, mwandikopa ine, ndipo ndinakopedwa; muli ndi mphamvu koposa ine, ndipo mwalakika; ine ndikhala choseketsa dzuwa lonse, onse andiseka.
8
Pakuti paliponse ndinena, ndifuula; ndifuula, Chiwawa ndi chofunkha; pakuti mau a Yehova ayesedwa kwa ine chitonzo, ndi choseketsa, dzuwa lonse.
9
Ndipo ngati nditi, Sindidzamtchula Iye, sindidzanenanso m'dzina lake, pamenepo m'mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m'mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.
10
Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzamlaka iye, ndipo tidzambwezera chilango.
11
Koma Yehova ali ndi ine ngati wamphamvu ndi woopsa; chifukwa chake ondisautsa adzaphunthwa, sadzandilala; adzakhala ndi manyazi ambiri, chifukwa sanachite chanzeru, ngakhale ndi kunyazitsa kwamuyaya kumene sikudzaiwalika.
12
Koma, Inu Yehova wa makamu, amene muyesa olungama, amene muona impso ndi mtima, mundionetse ine kubwezera chilango kwanu pa iwo; pakuti kwa inu ndaululira mlandu wanga.
13
Muimbire Yehova, mulemekeze Yehova; pakuti walanditsa moyo wa aumphawi m'dzanja la ochita zoipa.
14
Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa; lisadalitsike tsiku limene amai wanga anandibala ine.
15
Atembereredwe munthu amene anatengera mau kwa atate wanga, kuti, Mwana wamwamuna anakubadwira iwe; ndi kumsekeretsatu iye.
16
Munthuyo akhale ngati midzi imene Yehova anapasula, osalekerera; amve mfuu mamawa, ndi mkuwo pausana;
17
chifukwa sanandiphe ine m'mimba; kuti mai wanga akhale manda anga, ndi mimba yake yaikulu nthawi zonse.
18
Chifukwa chanji ndinatuluka m'mimba kuti ndione kutopa ndi kulira, kuti masiku anga athe ndi manyazi?
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52