bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Jeremiah 2
Jeremiah 2
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 3 →
1
Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, nati,
2
Pita nufuule m'makutu a Yerusalemu, kuti, Yehova atero, Ndikumbukira za iwe kukoma mtima kwa ubwana wako, chikondi cha matomedwe ako; muja unanditsata m'chipululu m'dziko losabzalamo.
3
Israele anali wopatulikira Yehova, zipatso zoundukula za zopindula zake; onse amene adzamudya iye adzayesedwa opalamula; choipa chidzawagwera, ati Yehova.
4
Tamvani mau a Yehova, iwe nyumba ya Yakobo, ndi inu mabanja onse a nyumba ya Israele;
5
atero Yehova, Atate anu apeza chosalungama chanji mwa Ine, kuti andichokera kunka kutali, natsata zachabe, nasanduka achabe?
6
Osati Ali kuti Yehova amene anatikweza kuchokera kudziko la Ejipito, natitsogolera m'chipululu, m'dziko loti see ndi la maenje, m'dziko la chilala ndi la mthunzi wa imfa, m'dziko losapitanso anthu, losamangamo anthu?
7
Ndipo ndinakulowetsani m'dziko la minda, kuti mudye zipatso zake, ndi zabwino zake; koma pamene munalowa, munaipitsa dziko langa, ndi kuyesa cholandira changa chonyansa.
8
Ansembe sanati, Ali kuti Yehova? Ndi iwo amene agwira malamulo sandidziwa Ine; ndi abusa omwe anandilakwira Ine, ndi aneneri ananenera mwa Baala, natsata zinthu zosapindula.
9
Chifukwa chake ndidzatsutsananso nanu, ati Yehova, ndi ana a ana anu ndidzatsutsana nao.
10
Pakuti pitani ku zisumbu za Kitimu nimuone; tumizani ku Kedara nimulingalire bwino; nimuone ngati chinalipo chotere.
11
Kodi mtundu wa anthu unasintha milungu yao, imene siili milungu? Koma anthu anga anasintha ulemerero wao ndi chosapindula.
12
Muzizwe pamenepo, miyamba inu, muope kwambiri, mukhale ouma, ati Yehova.
13
Pakuti anthu anga anachita zoipa ziwiri; anandisiya Ine kasupe wa madzi amoyo, nadziboolera zitsime, zitsime zong'aluka, zosakhalamo madzi.
14
Kodi Israele ndi mtumiki? Kodi ndiye kapolo wobadwa m'nyumba? Afunkhidwa bwanji?
15
Ana a mikango anambangulira iye, nakweza mau; anapasula dziko lake, midzi yake yatenthedwa, mulibenso wokhalamo.
16
Ananso a Nofi ndi a Tapanesi, anaswa pakati pamtu pako.
17
Kodi sunadzichitira ichi iwe wekha popeza unasiya Yehova Mulungu wako, pamene anatsogolera iwe panjira?
18
Tsopano uli nacho chiyani m'njira ya ku Ejipito, kumwa madzi a Sihori? Uli nacho chiyani m'njira ya ku Asiriya, kumwa madzi a m'mtsinje?
19
Choipa chako dzidzakulanga iwe, mabwerero ako adzakudzudzula iwe; dziwa, nuone, kuti ichi ndi choipa ndi chowawa, kuti wasiya Yehova Mulungu wako, ndi kuti kundiopa Ine sikuli mwa iwe, ati Yehova Mulungu wa makamu.
20
Pakuti kale lomwe ndinathyola goli lako, ndi kudula zomangira zako; ndipo unati, Sindidzakutumikirani, pakuti pa zitunda zonse zazitali, ndi patsinde pa mitengo yonse yaiwisi unawerama, ndi kuchita dama.
21
Ndipo Ine ndinakuoka mpesa wangwiro, mbeu yoona; kodi bwanji wandisandukira Ine mbeu yopanda pake, ya mpesa wachilendo?
22
Pakuti ngakhale usamba ndi soda, ndi kudzitengera sopo wambiri, mphulupulu zako zidziwika pamaso panga, ati Yehova Mulungu.
23
Bwanji uti, Sindinaipitsidwa, sindinatsata Abaala? Ona njira yako m'chigwa, dziwa chimene wachichita; ndiwe ngamira yothamanga yoyenda m'njira zake;
24
mbidzi yozolowera m'chipululu, yopumira mphepo pakufuna pake; pokomana nayo ndani adzaibweza? Onse amene aifuna sadzadzilemetsa; adzaipeza m'mwezi wake.
25
Kaniza phazi lako lisakhale losavala nsapato, ndi m'mero mwako musakhale ndi ludzu; koma unati, Palibe chiyembekezo, iai; pakuti ndakonda alendo, ndipo ndidzatsata pambuyo pao.
26
Monga mbala ili ndi manyazi pamene igwidwa, chomwecho nyumba ya Israele ili ndi manyazi; iwo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, ndi aneneri ao;
27
amene ati kwa mtengo, Iwe ndiwe atate wanga; ndi kwa mwala, Wandibala; pakuti anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope yao; koma m'nthawi ya kuvutidwa kwao adzati, Ukani, tipulumutseni.
28
Koma ili kuti milungu yako imene wadzipangira? Iuke, ikupulumutse iwe m'nthawi ya kuvutidwa kwako; pakuti milungu yako ilingana ndi kuchuluka kwa midzi yako, Yuda iwe.
29
Chifukwa chanji mudzatsutsana ndi Ine nonse? Mwandilakwira Ine, ati Yehova.
30
Ndapanda ana anu mwachabe; sanamvere kulanga; lupanga lanu ladya aneneri anu, monga mkango wakuononga.
31
Mbadwo inu, taonani mau a Yehova. Kodi ndakhala kwa Israele chipululu? Kapena dziko la mdima woti bii? Chifukwa ninji ati anthu anga, Tamasuka sitidzabweranso konse kwa Inu?
32
Kodi angathe namwali kuiwala zokometsera zake, kapena mkwitibwi zovala zake? Koma anthu anga andiiwala Ine masiku osawerengeka.
33
Kodi sukonzadi njira yako kufunafuna chilakolako? Chifukwa chake waphunzitsa akazi oipa njira zako.
34
Ndiponso m'nsalu zako wapezeka mwazi wa miyoyo ya aumphawi osachimwa; sunawapeza pakuboola, koma ponsepo.
35
Koma unati, Ndili wosachimwa ndithu; mkwiyo wake wachoka pa ine. Taona, ndidzakuweruza iwe, chifukwa uti, Sindinachimwa.
36
Bwanji uyendayenda kwambiri ndi kusintha njira yako? Udzachitanso manyazi ndi Ejipito monga unachita manyazi ndi Asiriya.
37
Koma udzatuluka kwa iyenso, manja ako pamtu pako; pakuti Yehova wakana zokhulupirira zako, ndipo sudzapindula m'menemo.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52