bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ecclesiastes 1
Ecclesiastes 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 2 →
1
Naŵa mau a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya ku Yerusalemu:
2
Zonse nzopanda phindu, akutero Mlaliki. Zonse nzachabechabe! Ndithudi zonse nzopandapake.
3
Kodi munthu amapindulanji ndi ntchito zonse zolemetsa zimene amazigwira pansi pano?
4
Mbadwo wina ukutha, wina ukudza, koma dziko lapansi limakhalapobe losasinthika.
5
Dzuŵa limatuluka, nkukaloŵa, ndipo limapita mwamsanga kumene linatulukira.
6
Mphepo imaombera chakumwera, nkudzakhotera chakumpoto. Imaomba mozungulirazungulira, pozungulirapo nkudzabwereranso komwe yachokera.
7
Mitsinje yonse imakathira ku nyanja, koma nyanjayo osadzaza. Kumene madzi adachokera amabwereranso komweko.
8
Zinthu zonse nzolemetsa, kulemera kwake nkosasimbika. Maso sakhuta nkupenya, makutunso sakhuta nkumva.
9
Zomwe zidaalipo kale ndizo zidzakhaleponso. Zomwe zidaachitika kale ndizo zidzachitikenso. Ndiye kuti chatsopano palibiretu pansi pano.
10
Kodi chilipo chinthu chimene wina anganene kuti, “Ichi ndiye nchatsopano?” Iyai, chidaalipo kale, ifenso kukadalibe nkomwe.
11
Zakale sizikumbukika, ngakhale zinthu zimene zidzachitike pambuyo pake sizidzakumbukikanso ndi amene adzabwere m'tsogolo mwake.
12
Ine Mlalikine ndidakhalapo mfumu yolamulira Israele ku Yerusalemu.
13
Ndidaaika mtima wanga pa kufunitsitsa kumvetsa bwino zonse zochitika pansi pano. Imeneyi ndi ntchito yolemetsa kwambiri imene Mulungu adatipatsa anthufe.
14
Zonse zochitika pansi pano ndaziwona. Zonsezo nzopandapake, ndipo kuzifunafuna nkungodzivuta chabe.
15
Chimene chidakhota sichingathe kuwongokanso, chimene palibe sichingathe kuŵerengedwa.
16
Mumtima mwangamu ndinkati, “Ndatola nzeru zambiri, kupambana onse amene ankalamulira ku Yerusalemu kale. Ndaphunzira zambiri zaluntha ndi zanzeru.”
17
Ndidaayesetsa kumvetsa kuti nzeru nchiyani, misala nchiyani, uchitsiru nchiyani. Koma ndidazindikira kuti kuterokonso kunali kungodzivuta chabe.
18
Paja nzeru zambiri zimadzetsa chisoni chambiri, munthu akamaonjezera nzeru, ndiye kuti akuwonjezeranso chisoni.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12