bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ecclesiastes 7
Ecclesiastes 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 8 →
1
Mbiri yabwino ndi yopambana mafuta onunkhira bwino amtengowapatali. Tsiku lomwalira ndi lopambana tsiku lobadwa.
2
Kuli bwino kupita ku nyumba yamaliro kupambana kupita ku nyumba yamadyerero. Pakuti imfa ndiye mathero ake a anthu onse, tsono amoyo azisinkhasinkha bwino zimenezi.
3
Chisoni nchabwino kupambana chimwemwe, chifukwa ngakhale nkhope ikhale yakugwa, mtima umathabe kutolapo nzeru.
4
Mtima wa munthu wanzeru umalingalira kaŵirikaŵiri za imfa. Koma mtima wa munthu wopusa umalingalira za chimwemwe.
5
Kuli bwino kuti munthu azimva kudzudzula kwa anthu anzeru, kupambana kumvera nyimbo zotamanda za zitsiru.
6
Kuseka kwa zitsiru kuli ngati kuthetheka kwa moto kunsi kwa mbiya. Zimenezinso nzachabechabe.
7
Ndithudi kuzunza ena kumamsandutsa munthu wanzeru kuti akhale wopusa, ndipo kulandira chiphuphu kumaononga mtima.
8
Mathero ake a chinthu ndi abwino kupambana chiyambi chake. Mtima wopirira ndi wopambana mtima wodzikuza.
9
Usamafulumira kukwiya, pakuti mkwiyo umakhalira zitsiru.
10
Usamafunsa kuti, “Chifukwa chiyani masiku amakedzana anali abwino kupambana masiku ano?” Limeneli si funso lanzeru.
11
Nzeru nzabwino ngati choloŵa chomwe, zimapindulitsa wamoyo aliyense pansi pano.
12
Chitetezo cha nzeru chili ngati chitetezo cha ndalama. Koma kudziŵa zinthu kukuposerapo, chifukwa nzeru zimasunga moyo wa amene ali nazo.
13
Taganizira ntchito ya Mulungu. Ndani angathe kuwongola chinthu chimene Iye adachipanga chokhota?
14
Uzikondwa mwai ukakufikira, ndipo tsoka likakugwera uzilingalirapo bwino pamenepo. Udziŵe kuti ndi Mulungu yemwe amene amatumiza mwai ndi tsoka. Amatero kuti munthu asadziŵiretu zimene zidzachitike m'tsogolo.
15
Pa moyo wanga wopandapakewu, ndaona zinthu ziŵiri izi: mwina anthu abwino amaonongeka, zabwino chichitirecho, mwinanso anthu oipa amakhala ndi moyo nthaŵi yaitali, zoipa chichitirecho.
16
Ndiye usachite kunkitsa nako kulungama, kapena kunkitsa nazo nzeru. Nanga ufere ziti?
17
Usachite kunyanyanso kuipa, usanyanye nawonso uchitsiru. Nanga uferenji nthaŵi yako isanakwane?
18
Nkwabwino kuti utsate njira imodzi, komanso osataya njira inayo. Munthu woopa Mulungu adzapeza phindu ndi ziŵiri zonsezo.
19
Nzeru zimapatsa munthu mphamvu zoposa zimene angampatse atsogoleri khumi amumzinda.
20
Ndithudi, pa dziko lapansi palibe munthu amene amachita zabwino zokhazokha osachimwa konse.
21
Usamasamala zonse zokamba anthu, mwinamwina udzamva wantchito wako akukutukwana.
22
Mumtima mwako ukudziŵa kuti iweyonso udatukwanapo anthu ena.
23
Zonsezi ndidaziyesa ndi nzeru zanga. Ndinkati, “Ndidzakhala wanzeru.” Koma nzeruzo zinali nane kutali.
24
Zimene zilipo zili kutali ndipo nzozama, kuzamatu kwambiri. Ndani angathe kuzidziŵa?
25
Motero ndidaikapo mtima kwambiri kuti ndidziŵe, ndifufuze ndi kumafunafuna nzeru ndi m'mene zinthu zimakhalira. Ndidafunanso kumvetsa kuipa kwake kwa uchitsiru ndiponso kupusa kwake kwa msala.
26
Ndidapeza china choŵaŵa kupambana imfa. Chinthucho ndi mkazi amene ali ngati msampha, amene mtima wake uli ngati ukonde, ndipo manja ake ali ngati maunyolo. Munthu wokondweretsa Mulungu amamthaŵa mkaziyo, koma wochimwa amalolera kukhala kapolo wake.
27
Zimenezitu nzimene ndidazipeza pakusonkhanitsa izi ndi izi, kuti ndidziŵe m'mene zinthu zimakhalira.
28
Ndizo zimene mtima wanga unkazifunafuna kaŵirikaŵiri, koma osazipeza. Ndidapeza mwamuna mmodzi yekha wolungama pakati pa anthu 1,000, koma mkazi wolungama sindidampezepo ndi mmodzi yemwe pakati pa anthu onsewo.
29
Ndidapeza chokhachi chakuti Mulungu pomulenga munthu, adampatsa mtima wolungama, koma anthu amatsata njira zaozao zambirimbiri.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12