bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ecclesiastes 5
Ecclesiastes 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 6 →
1
Uzisamala mayendedwe ako ukamapita ku Nyumba ya Mulungu. Kuli bwino kupita kumeneko kukaphunzirako, kupambana kukangopereka nsembe chabe ngati anthu opusa, amene sadziŵa kuti akuchita zoipa.
2
Usamafulumira kulankhula, ndipo usamalumbira msanga kwa Mulungu mumtima mwako. Paja Mulungu ali Kumwamba, iwe uli pansi pano, tsono usamachulukitsa mau ai.
3
Kuchuluka kwa mavuto mu mtima kumabweretsa maloto oipa, ndipo kuchuluka kwa mau kumadzetsa uchitsiru.
4
Ukalumbira chinthu kwa Mulungu, usachedwe kuchichita, chifukwa Mulungu sakondwera nazo zitsiru. Zimene wazilumbira, uzichitedi.
5
Kuli bwino kusalumbira kanthu kwa Mulungu, kupambana kuti ulumbire koma osachita.
6
Pakamwa pako pasakuchimwitse, kuti choncho usayenerenso kukauza wansembe wa Mulungu kuti, “Ai, ndinkangonena!” Chifukwa chiyani ufuna kuputa Mulungu? Kodi ukufuna kuti aononge zimene wazigwirira ntchito?
7
Maloto akachuluka pamachulukanso zokamba zachabechabe. Koma iwe uzilemekeza Mulungu.
8
Ukamaona anthu osauka akuzunzika m'dziko, ndiponso anthu ena akupsinja anzao ndi kuŵalanda ufulu wao mwankhanza, usadabwe nazo zimenezo. Paja woyang'anira wokulapo ali naye wina wamkulu kwambiri amene amamuyang'anira. Ndipo palinso akuluakulu enanso oyang'anira iwowo.
9
Alimi onse amatengako dzinthu dzam'minda, koma ndi mfumu yokha imene imaona phindu lake la mindayo.
10
Anthu okonda ndalama sakhutitsidwa nazo ndalamazo. Chimodzimodzinso anthu okonda chuma, sakhutitsidwa nalo phindu. Zimenezinso nzachabechabe.
11
Chuma chikachuluka, odya nawo chumacho amachulukanso. Nanga mwini wake amapindulapo chiyani? Si kumangoziyang'ana basi?
12
Wantchito amagona tulo tabwino, ngakhale adye pang'ono kapena kudya kwambiri. Koma wolemera, chuma sichimgonetsa tulo.
13
Pansi pano pali choipa china chomvetsa chisoni kwambiri chimene ndachiwona: Chuma chopweteka mwiniwake yemwe.
14
Ndiye chuma chimenecho chikamwazika moipa, munthuyo nkukhala ndi ana, amachita kusoŵa choŵapatsa ana akewo.
15
Monga momwe munthu adabadwira m'mimba mwa mai wake opanda kanthu, chonchonso adzapita maliseche. Pa zonse zimene adakhetsera thukuta, palibe nchimodzi chomwe chimene adzatenge m'manja mwake.
16
Chimenechinso nchoipa chomvetsa chisoni kwambiri: kuti munthu adzapita monga momwe adabwerera. Nanga phindu lake nchiyani, popeza kuti iyeyo adagwira pachabe ntchito yolemetsa?
17
Masiku ake onse moyo wake unali wodzaza ndi mdima ndi chisoni, unali moyo wa mavuto, matenda ndi nkhaŵa.
18
Tsono chimene ndimachiwona kuti nchabwino ndi choyenera ndi ichi: kumadya, kumamwa, ndi kumakondwerera ntchito zonse zolemetsa zimene munthu umagwira pansi pano, pa masiku oŵerengeka a moyo wako amene Mulungu wakupatsa. Nchokhachi chimene ungati nchako, choyenera kulandira.
19
Mwina Mulungu amamlemeretsa munthu pakumpatsa chuma ndi zabwino zina, namlola kuti akondwerere zonsezo. Munthuyo azilandire zimenezo ndi kumakondwerera ntchito zake zonse zolemetsa. Imeneyi ndi mphatso yochokeradi kwa Mulungu.
20
Munthu wotereyu sadzaganizako kwenikweni za kuchepa kwa masiku a moyo wake, chifukwa chakuti Mulungu wamdzaza ndi chimwemwe mu mtima.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12