bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ecclesiastes 4
Ecclesiastes 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 5 →
1
Ndidaonanso kuzunza kulikonse kochitika pansi pano. Ndipo ndidaona ozunzidwa akulira misozi, koma panalibe ndi mmodzi yemwe woti aŵatonthoze. Panalibe oŵatonthoza chifukwa ozunzawo anali ndi mphamvu.
2
Ndinkaganiza kuti akufa aja amene adapita kale ndi amwai kwambiri kupambana amene akadali ndi moyo.
3
Koma wopambana onsewo ndi amene sadabadwe nkomwe, ndipo ntchito zoipa zimene zimachitika pansi pano sadaziwone.
4
Tsono ndidazindikira kuti ntchito zonse zolemetsa ndiponso ntchito zonse zaluso zimachitika chifukwa choti wina akuchitira nsanje mnzake. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.
5
Paja akuti chitsiru chimangoti manja khodobala, nkumasoŵa chakudya mpaka kumafa ndi njala.
6
Komabe nkwabwino kukhala ndi moyo wabata wodzaza dzanja limodzi, kupambana kutekeseka ndi ntchito zolemetsa zodzaza manja aŵiri, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungozivuta chabe.
7
Ndidazindikira chinanso chopanda phindu pansi pano:
8
Panali munthu amene anali yekha, wopanda mwana kapena mbale, komabe ntchito yake yolemetsa sinkatha. Maso ake sankakhutitsidwa nacho chuma chake. Motero sankadzifunsa konse kuti, “Kodi ntchito yolemetsa ndikuigwirayi ndiponso mavuto a kudzimana zokondweretsaŵa, ndikuchitira yani?” Zimenezi nzopanda phindu ndiponso nzosakondweretsa.
9
Kukhala aŵiri nkwabwino koposa kukhala wekha, chifukwa ntchito ya anthu aŵiri ili ndi phindu lopambana.
10
Aŵiriwo akagwa, wina adzautsa mnzake. Koma tsoka amene ali yekha: akagwa, ndiye kuti zavuta, chifukwa palibe wina womuutsa.
11
Ndiponso aŵiri akagona pamodzi amafunditsana. Koma nanga mmodzi angathe kudzifunditsa bwanji?
12
Nkotheka kuti munthu apambane mnzake amene ali yekha, koma pakakhala aŵiri, iwoŵa adzalimbana naye. Chingwe cha nkhosi zitatu sichidukirapo.
13
Mnyamata wosauka ndi wanzeru ali bwino kupambana mfumu yokalamba ndi yopusa, imene siikumvanso malangizo.
14
Mnyamatayo atha kukhala kuti adachita kuchokera ku ndende kudzaloŵa ufumu, kapenanso kuti adabadwa mmphaŵi m'dziko mwake momwemo.
15
Ndinkaganiza za anthu onse amene amakhala pansi pano, ndipo ndidazindikira kuti pakati paopo panali mnyamata uja amene anali wodzatenga malo a mfumu.
16
Mfumu ikhoza kulamulira anthu osaŵerengeka, komabe itamwalira, palibe aliyense amene adzayamikire zomwe mfumuyo idachita. Ndithudi, zimenezinso nzopandapake, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12