bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ecclesiastes 6
Ecclesiastes 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 7 →
1
Choipa china chimene ndachiwona pansi pano, chimene chimaŵaŵa anthu zedi, ndi ichi:
2
Mulungu kukulemeretsa, kukupatsa chuma ndi ulemu, osasoŵa kanthu kalikonse kamene ukukalakalaka, koma tsono osakupatsa mwai woti udyerere zinthuzo, wodyerera nkukhala munthu wachilendo. Zimenezi nzothetsa nzeru, ndipo ndi vuto lokhumudwitsa kwambiri.
3
Munthu ngakhale abale ana zana limodzi, nkukhala ndi moyo zaka zambiri, ngakhale zaka zakezo zichuluke chotani, ngati sakondwerera zinthu zabwino za pa moyo wake, potsiriza osalandira maliro aulemu, ndithu ine ndikuti munthuyo ngakhale mtayo womwe umpambana kwambiri.
4
Mtayo umangopita pachabe nkuloŵa mu mdima, ndipo umakaiŵalika mumdimamo.
5
Ngakhale mtayowo sudaone dzuŵa kapena kudziŵa kanthu kalikonse, komabe umapumula kupambana munthu wa moyo wautali uja,
6
ngakhale akadakhala ndi moyo zaka zikwi ziŵiri, koma osaona zabwino. Kodi nanga onsewo suja amapita ku malo amodzimodzi?
7
Munthu amagwira ntchito zolemetsa kuti apeze chakudya, komabe satha kukhutira kotheratu.
8
Nanga munthu wanzeru ali ndi chiyani chimene amapambana nacho chitsiru? Kodi mmphaŵi amene amangodziŵa kukhala bwino pamaso pa anzake, ndiye kuti wapindulapo chiyani?
9
Kuli bwino kumangopenya zinthu ndi maso kupambana kumazilakalaka chamumtima. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.
10
Chilichonse chimene chilipo adachitchula kale dzina. Za m'mene munthu aliri nzodziŵika, nchomveka kuti sangathe kutsutsana ndi amene ali wamphamvu kupambana iyeyo.
11
Mau akachuluka, zopandapake zimachulukanso. Nanga munthu apindulapo chiyani?
12
Ndani amadziŵa zomkomera munthu kwenikweni pa nthaŵi yochepa imene munthuyo ali ndi moyo? Moyo wake ndi wa masiku ochepa, ndi wopandapake, umangopitirira ngati mthunzi. Ndani angathe kumufotokozera munthuyo zimene zidzachitike pansi pano iyeyo atafa?
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12