bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ecclesiastes 8
Ecclesiastes 8
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 9 →
1
Ndani angafanefane ndi munthu wanzeru? Ndani angadziŵe kutanthauza zinthu? Munthu nzeru zake zimampatsa chimwemwe, ndipo ukali umachoka pankhope pake.
2
Uzimvera lamulo la mfumu, ndipo chifukwa cha lumbiro lako kwa Mulungu usade nkhaŵa.
3
Zinthu zikapanda kuikondweretsa mfumu, uchoke pamaso pake mwamsanga, pakuti imachita chilichonse chimene chikuikomera.
4
Pajatu mau a mfumu ndi opambana. Ndani angafunse kuti, “Kodi mukuchita chiyani?”
5
Womvera malamulo ake sadzaona vuto lililonse. Munthu wanzeru amadziŵa nthaŵi yake ndi njira yake yochitira zonse.
6
Kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake ndi kachitidwe kake, ngakhale kuti mavuto ake a munthu amamupsinja kwambiri.
7
Palibe amene amadziŵa zimene zilikudza. Palibe amene angafotokozere zakutsogolo.
8
Monga munthu alibe mphamvu zolamulira mpweya wa moyo, chonchonso alibe mphamvu zolamulira tsiku la kufa kwake. Nkhondo sithaŵika, tsono anthu ochita zoipa, kuipa kwaoko sikudzaŵapulumutsa.
9
Zonsezi ndidaziwona pamene ndinkalingalira mumtima mwanga zonse zimene zimachitika pansi pano. Nthaŵi zonse pali ena amene amalamulira anzao mwankhanza.
10
Pambuyo pake ndidaona oipa akuikidwa m'manda. Iwowo kale ankaloŵa ndi kumatuluka m'malo oyera, ndipo mumzindamo anthu ankaŵatamanda m'mene ankachita zinthu zoterezi. Zimenezinso nzachabechabe.
11
Oweruza akamachedwetsa chilango cha anthu opalamula, anthu ena amalimba mtima nkumafuna kuti ayambe kuchita zoipa nawonso.
12
Ngakhale kuti wochimwa amati akachita zoipa kambirimbiri, amakhalabe moyo nthaŵi yaitali, komabe ndikudziŵa kuti omvera Mulungu ndiwo amene zinthu zidzaŵayendere bwino, poti ndi amene amamlemekeza.
13
Koma oipawo zinthu sizidzaŵayendera bwino, ndipo moyo wao udzakhala wosakhalitsa ngati mthunzi, poti samvera Mulungu.
14
Pali chinthu china chachabechabe chimene chimachitika pansi pano. Chinthucho ndi ichi: mwina anthu abwino amalangidwa ngati ochita zoipa, pamene oipa amalandira zabwino ngati kuti ndi anthu abwino. Ndikuti zimenezinso nzachabechabe.
15
Nchifukwa chake ndikuti munthu azikondwerera moyo, pakuti munthu alibe chinthu chinanso chabwino pansi pano choposa kudya, kumwa ndi kumadzikondweretsa. Akamatero, munthuyo adzakhala ndi chimwemwe pa ntchito yake masiku onse a moyo wake, amene Mulungu wampatsa pansi pano.
16
Ndinkaikapo mtima kuti ndidziŵe nzeru ndi kumvetsa ntchito zimene zikuchitika pansi pano, osapeza tulo usana ndi usiku.
17
Ndipo ndidaona ntchito zonse za Mulungu. Palibe munthu amene angathe kuzitulukira zonse zimene zimachitika pansi pano. Ngakhale munthu ayesetse chotani kuzimvetsa, sadzafikapo. Ngakhale munthu wanzeru anene kuti akudziŵa zinthu, nkosatheka kuti azitulukire.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12