bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ecclesiastes 2
Ecclesiastes 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 3 →
1
Nthaŵi zina mumtima mwangamu ndinkati, “Ah! Tsopano ndiyesepo zokondweretsa, ndidzisangalatse.” Koma ai, zimenezinso zinali zopanda phindu.
2
Kukakhala kuseka, ndidati, “Imene ija ndi misala.” Chikakhala chisangalatso, ndidati, “Phindu lake nchiyani?”
3
Potsata nzeruzo ndidaayesa kudzisangalatsa ndi vinyo, koma umenewo unali uchitsiru. Ndinkati mwina kapena njira yotere nkukhala yopambana, imene anthu amatsata pofuna kusangalala pa masiku oŵerengeka a moyo wao.
4
Ndidaachita ntchito zazikulu. Ndidaamanga nyumba zambiri, ndi kudziwokera mipesa.
5
Ndidaalima madimba ndi minda ya mitengo. Ndidaabzalamo mitengo yazipatso ya mitundu yonse.
6
Ndidaakumbanso maiŵe oti madzi ake azithirira minda ya mitengo yobzala ija.
7
Ndidaagula akapolo ndi adzakazi, ndinalinso ndi akapolo obadwira m'nyumba mwanga momwe. Ndinali ndi ng'ombe ndi nkhosa kupambana aliyense amene adalamulirapo ku Yerusalemu kale.
8
Ndidaadzikundikiranso siliva ndi golide ndiponso chuma chochokera kwa mafumu amene ndinkaŵalamulira. Ndinali ndi ondiimbira nyimbo, amuna ndi akazi omwe. Ndinalinso ndi akazi aang'ono ochuluka, aja amasangalatsa mitima ya amunaŵa.
9
Ndidaasanduka munthu wotchuka, nkudzapambana onse amene ankalamulira ku Yerusalemu kale, monsemo nzeru osandichoka.
10
Chilichonse chimene maso anga ankachilakalaka, ndidaachitenga. Mtima wanga sindidaumane zokondweretsazo, pakuti mtima wangawo unkakondwa ndi ntchito zanga zonse zolemetsa. Zimenezi zinali mphotho ya ntchito zanga zolemetsazo.
11
Tsono ndidayamba kulingalira zonse zimene ndidazichita, ntchito zolemetsa zonse zimene ndidazigwira, nkuwona kuti zonsezo zinali zopanda phindu. Kunali kungodzivuta chabe. Ndithu panalibe choti nkupindulapo pa dziko lapansi.
12
Pamenepo ndidayesanso kulingalira kuti kwenikweni nzeru nchiyani, misala nchiyani, uchitsiru nchiyani. Kodi munthu wodzaloŵa ufumu tsopanoyo angapose bwanji mnzake adapita uja? Nzokhazokhazo zomwe ameneyo adazichita kale.
13
Ndidaona kuti inde nzeru nzopambana uchitsiru, monga momwe kuŵala kumapambanira mdima.
14
Inde munthu wanzeru amayenda maso ali patsogolo, pamene chitsiru chimayenda m'chimbulimbuli. Komabe ndidazindikira kuti zomwe zagwera winayo, mnzakeyonso zimamgwera zomwezo.
15
Ndiye ine ndidayamba kulingalira kuti, “Kani zimene zimagwera chitsiru nanenso zidzandigwera zomwezo! Nanga tsono ineyo nzeru zambiri chotere nzanji?” Pamenepo ndidaona kuti zimenezinso nzopanda phindu!
16
Pakuti munthu wanzeru, pamodzi ndi chitsiru chomwe, onsewo sakumbukika nthaŵi yaitali, pokhala kuti pa masiku akutsogolo, onsewo adzaiŵalika. M'mene chimafera chitsiru ndi m'menenso amafera munthu wanzeru.
17
Motero moyo wanga ndidaipidwa nawo, chifukwa chakuti zonse zochitika pansi pano zimandimvetsa chisoni. Ndithudi, zonsezo nzopandapake, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.
18
Ntchito zanga zonse zolemetsa zimene ndidazigwira pansi pano zidandiipira, chifukwa ndiyenera kuzisiyira amene adzabwere pambuyo panga.
19
Tsono ndani amadziŵa kuti munthu ameneyo adzakhala wanzeru kapena chitsiru? Komabe munthuyo adzakhala womalamulira zonse zimene ndidazichita pansi pano mwa nzeru zanga. Zimenezinso nzopanda phindu.
20
Motero ndidayamba kutaya mtima chifukwa cha ntchito zonse zimene ndidazigwira movutikira pansi pano.
21
Paja nthaŵi zina munthu amene wagwira ntchito zolemetsa mwaluntha, mwanzeru ndi mwaluso, zonsezo ayenera kuzisiyira munthu amene sadakhetserepo konse thukuta, kuti akondwere nazo. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo nzoipa kwambiri.
22
Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zonse zolemetsa ndi zodetsa nkhaŵa zimene amazichita pansi pano?
23
Masiku ake onse amakhala achisoni, ntchito yake imakhala yovuta. Ndi usiku womwe mtima wake supumula. Zimenezinso nzopanda phindu.
24
Kwa munthu palibe chabwino china choposa kudya, kumwa ndi kukondwerera ntchito zake. Ngakhale zimenezi ndazindikira kuti nzochokera kwa Mulungu.
25
Nanga popanda Iye ndani angathe kudya, ndani angathe kusangalala?
26
Pajatu munthu wokondweretsa Mulungu, Mulunguyo amamsandutsa waluntha, wanzeru ndi wosangalala. Koma wochimwa amampatsa ntchito yokunkha ndi younjika zinthu, kenaka zonsezo nkuzipatsa munthu wokondwetsa Mulungu. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12