bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ecclesiastes 10
Ecclesiastes 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 11 →
1
Ntchentche zakufa zimaika fungo loipa m'mafuta onunkhira bwino. Choncho kupusa kwapang'ono kumatha kuwononga nzeru ndi ulemu.
2
Mtima wa munthu wanzeru umamtsogolera bwino, koma mtima wa munthu wopusa umamsokeza.
3
Chitsiru ngakhale chikamayenda mu mseu, zochita zake nzopanda nzeru ndithu, ndipo aliyense amachizindikira kuti nchitsirudi.
4
Wolamula akakukwiyira, usachoke pa ntchito yako, pakuti kufatsa kumakonza ngakhale zolakwa zazikulu.
5
Pansi pano pali choipa china chimene ndachiwona, choipa chake ndi cholakwa chimene amachichita wolamula.
6
Opusa amaŵapatsa ntchito zapamwamba, olemera nkumaŵapatsa ntchito zotsika.
7
Ndaona akapolo akuyenda pa akavalo, m'menemo akalonga akuyenda pansi ngati akapolo.
8
Amene amakumba dzenje adzagwamo yekha. Amene amaboola khoma njoka idzamuluma.
9
Amene amakumba miyala, itha kumpweteka miyalayo. Amene amaŵaza nkhuni, atha kudzipweteka nazo.
10
Nkhwangwa ikakhala yobuntha, nkupandanso kuinola, imalira mphamvu zambiri potema. Koma nzeru zimathandiza munthu kuti athedi kudula kanthu.
11
Nkopanda phindu kudziŵa kuseŵeretsa njoka ngati njokayo yakuluma kale.
12
Mau a pakamwa pa munthu wanzeru amakondweretsa, koma pakamwa pa chitsiru mpoononga.
13
Chitsiru chimayamba ndi mau opusa, potsiriza zolankhula zake zimangokhala zamisala basi.
14
Chitsiru chimangochulutsa mau. Kodi ndani angadziŵe zimene zidzachitike kutsogolo? Ndani angathe kumuuza munthu zimene zidzachitike iye atafa?
15
Chitsiru chimagwira ntchito modzitopetsa, koma njira yopita ku mzinda sichiidziŵa.
16
Tsoka kwa iwe dziko, ngati mfumu yako ikali mwana, ndipo nduna zako zimachezera madyerero usiku wonse.
17
Koma ndiwe wodala iwe dziko, ngati mfumu yako ndi mwana wa mfulu. Ndiwe wodala ngati nduna zako zimachita phwando pa nthaŵi yabwino, kuti zikhale zamphamvu, osati kuti ziledzere.
18
Denga limaloshoka, mwini wake akakhala waulesi, ndipo nyumba imadontha, mwiniwake akakhala nthyamba.
19
Phwando ndi lokondwetsa anthu, ndipo vinyo ndi wosangalatsa moyo. Komatu zonsezo nzolira ndalama.
20
Ngakhale mumtima mwako usamainyoza mfumu. Ngakhale m'chipinda mwako momwe usamatukwana wolemera. Mwina kambalame kamumlengalenga kapena kachilombo kena kouluka nkukumvera, kenaka nkukaulula zonse kwa amene umaŵanenawo.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12