bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Deuteronomy 11
Deuteronomy 11
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 12 →
1
Chifukwa chake muzikonda Yehova Mulungu wanu, ndi kusunga chilangizo chake, ndi malemba ake, ndi maweruzo ake, ndi malamulo ake, masiku onse.
2
Ndipo dziwani lero lino; pakuti sindinena ndi ana anu osadziwa, ndi osapenya kulanga kwa Yehova Mulungu wanu, ukulu wake, dzanja lake lamphamvu, ndi mkono wake wotambasuka,
3
ndi zizindikiro zake, ndi ntchito zake, adazichitira Farao mfumu ya Aejipito, ndi dziko lake lonse pakati pa Ejipito;
4
ndi chochitira Iye nkhondo ya Ejipito, akavalo ao, ndi agaleta ao; kuti anawamiza m'madzi a Nyanja Yofiira, muja anakutsatani m'mbuyo, ndi kuti Yehova anawaononga kufikira lero lino;
5
ndi chimene anakuchitirani m'chipululu, kufikira munadza kumalo kuno;
6
ndi chimene anachitira Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, mwana wa Rubeni; muja nthaka inatsegula pakamwa pake, ndi kuwameza iwo, ndi mabanja ao, ndi mahema ao, ndi za moyo zonse zakuwatsata pakati pa Israele wonse.
7
Koma maso anu anapenya ntchito yonse yaikulu ya Yehova anaichita.
8
Potero muzisunga malamulo onsewa ndikuuzani lero lino, kuti mukhale amphamvu, ndi kulowa ndi kulandira dziko, limene mumkako kulilandira;
9
ndi kuti masiku anu achuluke m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, kuti adzawapatsa iwo ndi mbeu zao, dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.
10
Pakuti dziko limene mumkako kulilandira ndi losanga dziko la Ejipito lija mudatulukako, kumene kuja munafesa mbeu zanu, ndi kuzithirira ndi phazi lanu, monga munda watherere;
11
koma dziko limene mumkako kulilandira ndilo dziko la mapiri ndi zigwa; limamwa madzi a mvula ya kumwamba;
12
ndilo dziko loti Yehova Mulungu wanu alisamalira, maso a Yehova Mulungu wanu akhalapo chikhalire, kuyambira chaka mpaka kutsiriza chaka.
13
Ndipo kudzakhala mukasamalira chisamalire malamulo anga amene ndikuuzani lero lino, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kumtumikira ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse,
14
ndidzapatsa mvula ya dziko lanu m'nyengo yake, ya chizimalupsa ndi ya masika, kuti mutute tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu.
15
Ndipo ndidzapatsa msipu wa zoweta zanu podyetsa panu; mudzadyanso nimudzakhuta.
16
Dzichenjerani nokha, angachete mitima yanu, nimungapatuke, ndi kutumikira milungu ina, ndi kuipembedza;
17
ndi kuti Mulungu angapse mtima pa inu, nangatseke kumwamba, kuti isowe mvula, ndi kuti nthaka isapereke zipatso zake; ndi kuti mungaonongeke msanga m'dziko lokomali Yehova akupatsani.
18
Chifukwa chake muzisunga mau anga awa mumtima mwanu ndi m'moyo mwanu; ndi kuwamanga ngati chizindikiro pamanja panu; ndipo zikhale zapamphumi pakati pa maso anu.
19
Ndipo muziwaphunzitsa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala inu pansi m'nyumba mwanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pakuuka inu pomwe.
20
Ndipo muziwalembera pa mphuthu za nyumba zanu, ndi pa zipata zanu;
21
kuti masiku anu ndi masiku a ana anu achuluke m'dziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu kuti adzawapatsali, monga masiku a thambo lili pamwamba pa dziko.
22
Pakuti mukasunga chisungire malamulo awa onse amene ndikuuzani kuwachita; kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake zonse, ndi kummamatira;
23
Yehova adzapirikitsa amitundu awa onse pamaso panu, ndipo mudzalanda amitundu akulu ndi amphamvu oposa inu.
24
Pamalo ponse padzapondapo phazi lanu ndi panu, kuyambira chipululu ndi Lebanoni, kuyambira pa mtsinjewo, mtsinje wa Yufurate, kufikira nyanja ya m'tsogolo, ndiwo malire anu.
25
Palibe munthu adzaima pamaso panu; Yehova Mulungu wanu adzanjenjemeretsa ndi kuopsa dziko lonse mudzapondapo, chifukwa cha inu, monga anenana ndi inu.
26
Taonani, ndilikuika pamaso panu lero dalitso ndi temberero;
27
dalitso, ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikuuzani lero lino;
28
koma temberero, ngati simudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kupatuka m'njira ndikuuzani lero lino, kutsata milungu ina imene simunaidziwa.
29
Ndipo kudzakhala, atakulowetsani Yehova Mulungu wanu m'dziko limene mumkako kulilandira, munene mdalitso pa phiri la Gerizimu, ndi temberero pa phiri la Ebala.
30
Sakhala kodi tsidya lija la Yordani, m'tseri mwake mwa njira yake yolowa dzuwa, m'dziko la Akanani, akukhala m'chidikha, pandunji pake pa Giligala, pafupi pa mathundu a More?
31
Pakuti mulinkuoloka Yordani kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani; ndipo mudzachilandira cholowa chanu, ndi kukhalamo.
32
Potero samalirani kuchita malemba ndi maweruzo onse ndiwaika pamaso panu lero lino.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34