bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Deuteronomy 18
Deuteronomy 18
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 19 →
1
Ansembe Alevi, fuko lonse la Levi, alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi Israele; azizidya nsembe zamoto za Yehova, ndi cholowa chake.
2
Alibe cholowa pakati pa abale ao; Yehova mwini wake ndiye cholowa chao, monga ananena nao.
3
Ndipo zoyenera ansembe, awapatse anthu akuphera nsembe ndizo: ingakhale ng'ombe kapena nkhosa azipatsa wansembe mwendo wamwamba, ndi ya m'masaya ndi chifu.
4
Zipatso zoyamba za tirigu wanu, za vinyo wanu, ndi za mafuta anu ndi ubweya woyamba kuusenga, muwapatse izi.
5
Popeza Yehova Mulungu wanu anawasankha mwa mafuko anu onse, aimirire natumikire m'dzina la Yehova, iwo ndi ana ao amuna kosalekeza.
6
Ndipo Mlevi akachokera kumudzi wanu wina m'Israele monse, kumene akhalako, nakadza ndi chifuniro chonse cha moyo wake ku malo amene Yehova adzasankha;
7
pamenepo azitumikira m'dzina la Yehova Mulungu wake, monga amachita abale ake onse Alevi akuimirirako pamaso pa Yehova.
8
Chakudya chao chizifanana, osawerengapo zolowa zake zogulitsa.
9
Mutakalowa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, musamaphunzira kuchita monga mwa zonyansa za amitundu aja.
10
Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi ku moto wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga.
11
Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa.
12
Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye; ndipo chifukwa cha zonyansa izi Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu.
13
Mukhale angwiro ndi Yehova Mulungu wanu.
14
Pakuti amitundu awa amene mudzawalandira, amamvera iwo akuyesa mitambo, ndi a ula; koma inu, Yehova Mulungu wanu sakulolani kuchita chotero.
15
Yehova Mulungu wanu adzakuukitsirani mneneri wa pakati panu, wa abale anu, wonga ine; muzimvera iye;
16
monga mwa zonse munafunsa Yehova Mulungu wanu m'Horebu, tsiku lakusonkhana lija, ndi kuti, Tisamvenso mau a Yehova Mulungu wathu, ndipo tisaonenso moto waukulu uwu, kuti tingafe.
17
Ndipo Yehova anati kwa ine, Chokoma ananenachi.
18
Ndidzawaukitsira mneneri wa pakati pa abale ao, wonga iwe; ndipo ndidzampatsa mau anga m'kamwa mwake, ndipo adzanena nao zonse ndimuuzazi.
19
Ndipo kudzakhala kuti munthu wosamvera mau anga amene amanena m'dzina langa, ndidzamfunsa.
20
Koma mneneri wakuchita modzikuza ndi kunena mau m'dzina langa, amene sindinamlamulira anene, kapena kunena m'dzina la milungu ina, mneneri ameneyo afe.
21
Ndipo mukati m'mtima mwanu, Tidzazindikira bwanji mau amene Yehova sananene?
22
Mneneri akanena m'dzina la Yehova, koma mau adanenawa sachitika, nisafika, ndiwo mau Yehova sanawanene; mneneriyo ananena modzikuza, musamuope iye.
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34