bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Deuteronomy 12
Deuteronomy 12
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 13 →
1
Awa ndi malemba ndi maweruzo, muziwasamalirawa kuwachita m'dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu anakupatsani likhale lanulanu, masiku onse akukhala ndi moyo inu pa dziko lapansi.
2
Muononge konse malo onse, amitundu amene mudzawalanda anatumikirako milungu yao, pa mapiri aatali, ndi pa zitunda, ndi pansi pa mitengo yonse yabiriwiri;
3
nimugumule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kutentha zifanizo zao, ndi kulikha mafano osema a milungu yao; ndipo muononge dzina lao lichoke m'malomo.
4
Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu.
5
Koma kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha mwa mafuko anu onse kuikapo dzina lake, ndiko ku chokhalamo chake, muzifunako, ndi kufikako;
6
ndi kubwera nazo kumeneko nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, ndi magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza ya dzanja lanu, ndi zowinda zanu, ndi nsembe zanu zaufulu, ndi zoyamba kubadwa za ng'ombe zanu, ndi za nkhosa ndi mbuzi zanu;
7
ndipo kumeneko muzidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kukondwera nazo zonse mudazigwira ndi dzanja lanu, inu ndi a pa banja lanu, m'mene Yehova Mulungu wanu anakudalitsani.
8
Musamadzichita monga mwa zonse tizichita kuno lero, yense kuchita chilichonse chiyenera m'maso mwake;
9
pakuti mpaka lero simunafikira mpumulo ndi cholowa, zimene Yehova Mulungu wanu adzakupatsani.
10
Koma mudzaoloka Yordani, ndi kukhala m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akulandiritsani; ndipo adzakupumulitsani akulekeni adani anu onse pozungulirapo, ndipo mudzakhala mokhazikika.
11
Pamenepo padzakhala malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake, kumeneko muzibwera nazo zonse ndikuuzanizi; nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza dzanja lanu, ndi zowinda zanu zosankhika zimene muzilonjezera Yehova.
12
Ndipo mudzakondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi antchito anu amuna, ndi antchito anu akazi, ndi Mlevi ali m'midzi mwanu, popeza alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi inu.
13
Dzichenjerani nokha, musamapereka nsembe zanu zopsereza pamalo ponse upaona:
14
koma pamalo pamene Yehova adzasankha, mwa limodzi la mafuko anu, pamenepo muzipereka nsembe zanu zopsereza, ndi pamenepo muzichita zonse ndikuuzani.
15
Koma monga mwa chikhumbu chonse cha moyo wanu muiphe ndi kudya nyama m'midzi yanu yonse, monga mwa mdalitso wa Yehova Mulungu wanu anakupatsani; odetsa ndi oyera adyeko, monga yamphoyo ndi yangondo.
16
Mwazi wao wokha musamadya; muziuthira panthaka ngati madzi.
17
Simukhoza kudya m'mudzi mwanu limodzi la magawo khumi la tirigu wanu, kapena la vinyo wanu, kapena la mafuta anu, kapena oyamba kubadwa a ng'ombe zanu kapena la nkhosa ndi mbuzi zanu, kapena zowinda zanu zilizonse muzilonjeza kapena nsembe zanu zaufulu, kapena nsembe yokweza ya m'dzanja lanu;
18
koma muzizidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha, inu, ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi antchito anu amuna, ndi antchito anu akazi, ndi Mlevi ali m'mudzi mwanu; nimukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'zonse mudazigwira ndi dzanja lanu.
19
Dzichenjerani nokha, musataye Mlevi masiku onse akukhala inu m'dziko mwanu.
20
Akadzakuza malire a dziko lanu Yehova Mulungu wanu, monga ananena ndi inu, ndipo mukadzati, Ndidye nyama, popeza moyo wanga ukhumba kudya nyama; mudye nyama monga umo monse ukhumba moyo wanu.
21
Malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kuikako dzina lake akakutanimphirani, muziphako ng'ombe zanu ndi nkhosa ndi mbuzi zanu zimene Yehova anakupatsani, monga ndinakuuzani, ndi kuzidya m'mudzi mwanu, monga umo monse ukhumba moyo wanu.
22
Koma monga umo amadya mphoyo ndi ngondo momwemo uzizidya; odetsa ndi oyera adyeko chimodzimodzi.
23
Koma mulimbikepo ndi kusadya mwaziwo; popeza mwazi ndiwo moyo, nimusamadya moyo pamodzi ndi nyama yake.
24
Musamadya uwu; muuthire pansi ngati madzi.
25
Musamadya uwu; kuti chikukomereni inu, ndi ana anu akudza m'mbuyo mwanu, pakuchita inu zoyenera pamaso pa Yehova.
26
Zopatulika zanu zokha zimene muli nazo, ndi zowinda zanu, muzitenge, ndi kupita nazo ku malo amene Yehova adzasankha;
27
ndipo mupereke nsembe zanu zopsereza, nyama zao ndi mwazi wao, pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu; ndipo athire mwazi wa nsembe zanu zophera pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu, koma nyama yake muidye.
28
Samalirani ndi kumvera mau awa onse ndikuuzaniwa, kuti chikukomereni inu, ndi ana anu akudza m'mbuyo mwanu nthawi zonse, pochita inu zokoma ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.
29
Pamene Yehova Mulungu wanu akadzadulatu amitundu pamaso panu, kumene mulowako kuwalandira, ndipo mutawalandira, ndi kukhala m'dziko lao,
30
dzichenjerani nokha mungakodwe ndi kuwatsata, ataonongeka pamaso panu; ndi kuti mungafunsire milungu yao, ndi kuti, Amitundu awa atumikira milungu yao bwanji? Ndichite momwemo inenso.
31
Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu; pakuti zilizonse zinyansira Yehova, zimene azida Iye, iwowa anazichitira milungu yao; pakuti angakhale ana ao amuna ndi ana ao akazi awatentha m'moto, nsembe ya milungu yao.
32
Chilichonse ndikuuzani, muchisamalire kuchichita; musamaonjezako, kapena kuchepsako.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34