bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Deuteronomy 23
Deuteronomy 23
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 24 →
1
Munthu wophwetekwa, wophwanyika kapena wofulika, asalowe m'msonkhano wa Yehova.
2
Mwana wa m'chigololo asalowe m'msonkhano wa Yehova, ngakhale mbadwo wake wakhumi usalowe m'msonkhano wa Yehova.
3
Mwamoni kapena Mmowabu asalowe m'msonkhano wa Yehova; ngakhale mbadwo wao wakhumi usalowe m'msonkhano wa Yehova, ku nthawi zonse;
4
popeza sanakumana nanu ndi mkate ndi madzi m'njira muja munatuluka m'Ejipito; popezanso anakulembererani Balamu mwana wa Beori wa ku Petori wa Mesopotamiya, kuti akutemberereni.
5
Ndipo Yehova Mulungu wanu sanafune kumvera Balamu; koma Yehova Mulungu wanu anakusandulizirani tembererolo likhale mdalitso, popeza Yehova Mulungu wanu anakukondani.
6
Musawafunira mtendere, kapena chowakomera masiku anu onse ku nthawi zonse.
7
Musamanyansidwa naye Mwedomu, popeza ndiye mbale wanu; musamanyansidwa naye Mwejipito, popeza munali alendo m'dziko lake.
8
Ana obadwa nao a mbadwo wachitatu alowe m'msonkhano wa Yehova.
9
Nkhondo yanu ikatuluka pa adani anu, mudzisunge kusachita choipa chilichonse.
10
Pakakhala munthu pakati pa inu, ndiye wosayera chifukwa chochitika usiku, azituluka kunja kwa chigono, asalowe pakati pa chigono;
11
koma kudzali pofika madzulo, asambe m'madzi; ndipo litalowa dzuwa alowe pakati pa chigono.
12
Mukhale nao malo kunja kwa chigono kumene muzimukako kuthengo;
13
nimukhale nacho chokumbira mwa zida zanu; ndipo kudzali, pakukhala inu pansi kuthengo mukumbe nacho, ndi kutembenuka ndi kufotsera chakutulukacho;
14
popeza Yehova Mulungu wanu ayenda pakati pa chigono chanu kukupulumutsani ndi kupereka adani anu pamaso panu; chifukwa chake chigono chanu chikhale chopatulika; kuti angaone kanthu kodetsa mwa inu, ndi kukupotolokerani.
15
Musamapereka kwa mbuye wake kapolo wopulumuka kwa mbuye wake kuthawira kwa inu;
16
akhale nanu, pakati panu, ku malo asankhako iye m'mudzi mwanu mwina momkonda; musamamsautsa.
17
Pasakhale mkazi wachigololo pakati pa ana akazi a Israele, kapena wachigololo pakati pa ana amuna a Israele.
18
Musamabwera nayo mphotho ya wachigololo, kapena mtengo wake wa galu kulowa nazo m'nyumba ya Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha chowinda chilichonse; pakuti onse awiriwa Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.
19
Musamakongoletsa mbale wanu mopindulitsa; phindu la ndalama, phindu la chakudya, phindu la kanthu kalikonse kokongoletsa.
20
Mukongoletse mlendo mopindulitsa; koma mbale wanu musamamkongoletsa mopindulitsa, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni mwa zonse muzigwira ndi dzanja lanu, m'dziko limene mulowamo kulilandira.
21
Mukawindira Yehova Mulungu wanu chowinda, musamachedwa kuchichita; popeza Yehova Mulungu wanu adzakufunsani za ichi ndithu ndipo mukadachimwako.
22
Koma mukapanda kulonjeza chowinda, mulibe kuchimwa.
23
Chotuluka pa milomo yanu muchisamalire ndi kuchichita; monga munalonjezera Yehova Mulungu wanu, chopereka chaufulu munachilonjeza pakamwa panu.
24
Mukalowa m'munda wamphesa wa mnansi wanu, mudyeko mphesa ndi kukhuta nazo monga mufuna eni; koma musaika kanthu m'chotengera chanu.
25
Mukalowa m'tirigu wosasenga wa mnansi wanu, mubudule ngala ndi dzanja lanu, koma musasengako ndi chisenga tirigu wachilili wa mnansi wanu.
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 24 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34