bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Deuteronomy 19
Deuteronomy 19
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 20 →
1
Pamene Yehova Mulungu wanu ataononga amitundu, amene Yehova Mulungu wanu akupatsani dziko lao, ndipo mutalilandira lanulanu, ndi kukhala m'midzi mwao, ndi m'nyumba zao;
2
pamenepo mudzipatulire midzi itatu pakati pa dziko lanu, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanulanu.
3
Mudzikonzere njira, ndi kugawa malire a dziko lanu, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanulanu, patatu; kuti wakupha munthu athawireko.
4
Ndipo mlandu wa munthu wakupha mnzake wakuthawirako nakhala ndi moyo ndiwo: wakupha mnzake osati dala, osamuda kale lonse;
5
monga ngati munthu analowa kunkhalango ndi mnzake kutema mitengo, ndi dzanja lake liyendetsa nkhwangwa kutema mtengo, ndi nkhwangwa iguluka m'mpinimo, nikomana ndi mnzake, nafa nayo; athawire ku wina wa midzi iyi, kuti akhale ndi moyo;
6
kuti wolipsa mwazi angalondole wakupha mnzake, pokhala mtima wake watentha, nampeza, popeza njira njaitali, namkantha kuti wafa; angakhale sanapalamule imfa, poona sanamude kale lonse.
7
Chifukwa chake ndikuuzani ndi kuti, Mudzipatulire midzi itatu.
8
Ndipo Yehova Mulungu wanu akakulitsa malire anu, monga analumbirira makolo anu, ndi kukupatsani dziko lonse limene ananena kwa makolo anu kuwapatsa ili;
9
ukadzasunga lamulo ili lonse kulichita, limene ndikuuzani lero lino, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zake masiku onse; pamenepo mudzionjezere midzi itatu ina pamodzi ndi itatu iyi;
10
kuti angakhetse mwazi wosachimwa pakati pa dziko lanu, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu, pangakhale mwazi pa inu.
11
Koma munthu akamuda mnzake, namlalira, ndi kumuukira ndi kumkantha moyo wake, kuti wafa; nakathawira ku wina wa midzi iyi;
12
pamenepo akulu a mudzi wake atumize ndi kumtengako ndi kumpereka m'manja mwa wolipsa mwazi, kuti afe.
13
Diso lanu lisamchitire chifundo, koma muchotse mwazi wosachimwa m'Israele, kuti chikukomereni.
14
Musamasendeza malire a mnansi wanu, amene adawaika iwo a kale lomwe, m'cholowa chanu mudzalandirachi, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanulanu.
15
Mboni imodzi isamaukira munthu pa mphulupulu iliyonse, kapena tchimo lililonse adalichimwa; pakamwa pa mboni ziwiri, kapena pakamwa pa mboni zitatu mlandu utsimikizike.
16
Mboni yachiwawa ikaukira munthu kumneneza ndi kuti analakwa;
17
pamenepo anthu onse awiri, pakati pao pali makaniwo, aziima pamaso pa Yehova, pamaso pa ansembe ndi oweruza okhala m'masiku awa;
18
ndipo oweruza afunsitse bwino; ndipo taonani, mboniyo ikakhala mboni yonama, yomnamizira mbale wake;
19
mumchitire monga iye anayesa kumchitira mbale wake; motero muchotse choipacho pakati panu.
20
Ndipo otsalawo adzamva, nadzaopa, ndi kusachitanso monga choipacho pakati panu.
21
Ndipo diso lanu lisachite chifundo, moyo kulipa moyo, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi.
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 20 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34