bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Deuteronomy 2
Deuteronomy 2
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 3 →
1
Pamenepo tinabwerera, ndi kuyenda kunka kuchipululu, kutsata njira ya Nyanja Yofiira, monga Yehova adanena ndi ine; ndipo tinapaza phiri la Seiri masiku ambiri.
2
Ndipo Yehova ananena ndi ine, ndi kuti,
3
Yakwanira nthawi yakupaza inu phiri ili; tembenukani kunka kumpoto.
4
Ndipo uuze anthu, ndi kuti, Mukapite kubzola malire a abale anu, ana a Esau okhala m'Seiri; ndipo adzakuopani; muchenjere ndithu;
5
musalimbana nao; popeza sindikupatsakoni dziko lao, pangakhale popondapo phazi lanu ai; pakuti ndapatsa Esau phiri la Seiri likhale lakelake.
6
Mugulane nao chakudya ndi ndalama, kuti mudye; mugulane naonso madzi kuti mumwe.
7
Pakuti Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mu ntchito zonse za manja anu; anadziwa kuyenda kwanu m'chipululu ichi chachikulu; zaka izi makumi anai Yehova Mulungu wanu anakhala ndi inu; simunasowa kanthu.
8
Potero tinapitirira abale athu, ana a Esau okhala m'Seiri, njira ya chidikha, ku Elati ndi ku Eziyoni-Gebere. Pamenepo tinatembenuka ndi kudzera njira ya chipululu cha Mowabu.
9
Ndipo Yehova anati kwa ine, Usavuta Mowabu, kapena kuutsana naye nkhondo; popeza sindidzakupatsako dziko lake likhale lakolako; pakuti ndinapatsa ana a Loti Ari likhale laolao.
10
(Aemimu anakhalamo kale, ndiwo anthu akulu, ndi ambiri, ndi ataliatali, ngati Aanaki.
11
Anawayesa iwonso Arefaimu, monga Aanaki; koma Amowabu awatcha Aemimu.
12
Ndipo Ahori anakhala m'Seiri kale, koma ana a Esau analanda dziko lao, nawaononga pamaso pao, nakhala m'malo mwao; monga Israele anachitira dziko lakelake, limene Yehova anampatsa).
13
Ukani tsopano, olokani mtsinje wa Zeredi. Ndipo tinaoloka mtsinje wa Zeredi.
14
Ndipo masiku amene tinayenda kuchokera ku Kadesi-Baranea, kufikira tidaoloka mtsinje wa Zeredi, ndiwo zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu; kufikira utatha mbadwo wonse wa amuna ankhondo m'chigono, monga Yehova adawalumbirira.
15
Komanso dzanja la Yehova linatsutsana nao, kuwaononga m'chigono, kufikira adawatha.
16
Ndipo kunali, atatha kufa amuna onse ankhondo mwa anthu,
17
Yehova ananena ndi ine, ndi kuti,
18
Lero lomwe utumphe malire a Mowabu, ndiwo Ari.
19
Ndipo pamene uyandikiza popenyana ndi ana a Amoni, usawavuta, kapena kuutsana nao; popeza sindidzakupatsako dziko la ana a Amoni likhale lakolako; popeza ndinapatsa ana a Loti ili likhale laolao.
20
(Ilinso aliyesa dziko la Arefaimu; Arefaimu anakhalamo kale; koma Aamoni awatcha Azamzumimu;
21
ndiwo anthu akulu, ndi ambiri, ndi atalitali, monga Aanaki; koma Yehova anawaononga pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m'malo mwao;
22
monga Iye anachitira ana a Esau, akukhala m'Seiri, pamene anaononga Ahori pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m'malo mwao kufikira lero lomwe.
23
Kunena za Aavimu akukhala m'midzi kufikira ku Gaza, Akafitori, akufuma ku Kafitori, anawaononga, nakhala m'malo mwao).
24
Uka, yenda ulendo wako, ndi kuoloka mtsinje wa Arinoni; taonani, ndapereka Sihoni mfumu ya Hesiboni, Mwamori, ndi dziko lake m'dzanja lako; yamba kulilandira, ndi kuutsana naye nkhondo.
25
Tsiku lino ndiyamba kuopsetsa nawe ndi kuchititsa mantha nawe anthu a pansi pa thambo lonse, amene adzamva mbiri yako, nadzanjenjemera, nadzawawidwa chifukwa cha iwe.
26
Ndipo ndinatuma amithenga ochokera ku chipululu cha Kedemoti kwa Sihoni mfumu ya Hesiboni ndi mau a mtendere, ndi kuti,
27
Ndipitire m'dziko mwako; ndidzatsata mseu, osapatuka ine ku dzanja lamanja kapena kulamanzere,
28
Undigulitse chakudya ndi ndalama, kuti ndidye; ndi kundipatsa madzi kwa ndalama, kuti ndimwe; chokhachi ndipitire choyenda pansi;
29
monga anandichitira ana a Esau akukhala m'Seiri, ndi Amowabu akukhala m'Ari; kufikira nditaoloka Yordani kulowa dziko limene Yehova Mulungu wathu atipatsa.
30
Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilole kupitira kwao; popeza Yehova Mulungu wanu anaumitsa mzimu wake, nalimbitsa mtima wake, kuti ampereke m'dzanja lanu, monga lero lino.
31
Ndipo Yehova anati kwa ine, Taona, ndayamba kupereka Sihoni ndi dziko lake pamaso pako; yamba kulandira dziko lake likhale lakolako.
32
Pamenepo Sihoni anatuluka kukomana nafe, iye ndi anthu ake onse, kugwirana nafe nkhondo ku Yahazi.
33
Ndipo Yehova Mulungu wathu anampereka iye pamaso pathu; ndipo tinamkantha, iye ndi ana ake amuna ndi anthu ake onse.
34
Ndipo muja tinalanda midzi yake yonse; ndipo tinaononga konse midzi yonse, amuna ndi akazi ndi ana; sitinasiyapo ndi mmodzi yense.
35
Zoweta zokha tinadzifunkhira, pamodzi ndi zofunkha za midzi tidailanda.
36
Kuyambira ku Aroere, ndiko kumphepete kwa mtsinje wa Arinoni, ndi kumudzi wokhala kumtsinje kufikira ku Giliyadi, kunalibe mudzi wakutitalikira malinga ake; Yehova Mulungu wathu anapereka yonse pamaso pathu.
37
Ku dziko la ana a Amoni lokha simunayandikiza; dera lonse la mtsinje wa Yaboki, ndi midzi ya kumapiri, ndi kwina kulikonse Yehova Mulungu wathu anatiletsa.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
Recommended Reading
Commentary
Deuteronomy Commentaries
→
Devotional
Deuteronomy Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Lopatulika) Study Bible
→