bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Deuteronomy 15
Deuteronomy 15
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 16 →
1
Pakutha pake pa zaka zisanu ndi ziwiri pakhale chilekerero.
2
Chilekererocho ndichi: okongoletsa onse alekerere chokongoletsa mnansi wake; asachifunse kwa mnansi wake, kapena mbale wake; popeza analalikira chilekerero cha Yehova.
3
Muyenera kuchifunsa kwa mlendo; koma chanu chilichonse chili ndi mbale wanu, dzanja lanu lichilekerere;
4
ndiko kuti pasakhale waumphawi mwa inu; pakuti Yehova adzakudalitsani kwambiri m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanuchanu;
5
chokhachi mumvere chimverere mau a Yehova Mulungu wanu, kuti musamalire kuchita malamulo awa onse amene ndikuuzani lero lino.
6
Popeza Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani, monga ananena nanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha; nimudzachita ufumu pa amitundu ambiri, koma iwo sadzachita ufumu pa inu.
7
Akakhala ndi inu munthu waumphawi, ndiye wina wa abale anu, m'umodzi wa midzi yanu, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, musakhakala mtima wanu, kapena kuumitsa dzanja lanu kukaniza mbale wanu waumphawi;
8
koma muzimtansira dzanja lanu ndithu ndi kumkongoletsa ndithu zofikira kusowa kwake, monga umo amasowa.
9
Dzichenjerani, mungakhale mau opanda pake mumtima mwanu, ndi kuti, Chayandika chaka chachisanu ndi chiwiri, chaka cha chilekerero; ndipo diso lanu lingaipire mbale wanu waumphawi, osampatsa kanthu; ndipo iye angalirire inu kwa Yehova; ndipo mwa inu mungakhale tchimo.
10
Muzimpatsa ndithu, osawawa mtima wanu pompatsa; popeza, chifukwa cha ichi Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mu ntchito zanu zonse, ndi m'zonse muikapo dzanja lanu.
11
Popeza waumphawi salekana m'dziko, chifukwa chake ndikuuzani ndi kuti, Dzanja lanu mulitansire ndithu mbale wanu, ndi ozunzika anu, ndi aumphawi anu, a m'dziko mwanu.
12
Mukagula mbale wanu, Muhebri wamwamuna kapena Muhebri wamkazi, ndipo adzakutumikira zaka zisanu ndi chimodzi; koma chaka chachisanu ndi chiwiri umlole achoke kwanu waufulu.
13
Ndipo pomlola iwe achoke kwanu waufulu, musamamlola achoke wopanda kanthu;
14
mumlemeze nazo za nkhosa ndi mbuzi zanu, ndi za popondera mphesa, ndi za mosungira vinyo; monga Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mumninkhe uyu.
15
Ndipo mukumbukire kuti munali akapolo m'dziko la Ejipito, ndipo Yehova Mulungu wanu anakuombolani; chifukwa chake ndikuuzani ichi lero lino.
16
Ndipo kudzakhala, akanena ndi inu, Sindituluka kuchoka kwanu; popeza akonda inu ndi nyumba yanu, popeza kumkomera kwanu;
17
pamenepo muzitenga lisungulo, ndi kulipisa m'khutu mwake, kulikanikiza ndi chitseko, ndipo adzakhala kapolo wanu kosalekeza. Muzichitanso momwemo ndi adzakazi anu.
18
Musamayesa nchosautsa, pomlola akuchokereni waufulu; popeza anakugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi monga wolipidwa wakulandira chowirikiza; potero Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m'zonse muzichita.
19
Zazimuna zonse zoyamba kubadwa, zobadwa mwa ng'ombe zanu ndi mwa nkhosa ndi mbuzi zanu, muzizipatulira Yehova Mulungu wanu; musamagwiritsa ntchito yoyamba kubadwa mwa ng'ombe zanu, kapena kusenga yoyamba kubadwa ya nkhosa kapena mbuzi zanu.
20
Muzidye chaka ndi chaka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo amene Yehova adzasankha, inu ndi a m'banja mwanu.
21
Koma ikakhala nacho chilema, yotsimphina, kapena yakhungu, chilema chilichonse choipa, musamaiphera nsembe Yehova Mulungu wanu.
22
Muidye m'mudzi mwanu; odetsa ndi oyera aidye chimodzimodzi, monga mphoyo ndi nswala.
23
Mwazi wake wokha musamadya; muuthire pansi ngati madzi.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34