bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Deuteronomy 22
Deuteronomy 22
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 23 →
1
Mukapenya ng'ombe kapena nkhosa ya mbale wako zilikusokera musamazilekerera, muzimbwezera mbale wanu ndithu.
2
Ndipo ngati mbale wanu sakhala pafupi ndi inu, kapena mukapanda kumdziwa, mubwere nayo kwanu kunyumba yanu, kuti ikhale kwanu, kufikira mbale wanu akaifuna, ndipo wambwezera iyo.
3
Mutero nayenso bulu wake; mutero nachonso chovala chake, mutero nachonso chotayika chilichonse cha mbale wanu, chakumtayikira mukachipeza ndi inu; musamazilekerera.
4
Mukapenya bulu kapena ng'ombe ya mbale wanu, zitagwa m'njira, musamazilekerera; mumthandize ndithu kuziutsanso.
5
Mkazi asavale chovala cha mwamuna, kapena mwamuna asavale chovala cha mkazi; pakuti aliyense wakuchita izi Yehova Mulungu wanu anyansidwa naye.
6
Mukachipeza chisa cha mbalame panjira, mumtengo kapena panthaka pansi, muli ana kapena mazira, ndi make alikuumatira ana kapena mazira, musamatenga make pamodzi ndi ana;
7
muloletu make amuke, koma mudzitengere ana; kuti chikukomereni, ndi kuti masiku anu achuluke.
8
Pamene mumanga nyumba yatsopano, muzimanga kampanda pa tsindwi lake, kuti ungatengere nyumba yanu mwazi, akagwako munthu.
9
Musamabzala mbeu zosiyana m'munda wanu wamphesa, kuti zingaipsidwe mbeu zonse udazibzala, ndi zipatso za munda wamphesa zomwe.
10
Musamalima ndi bulu ndi ng'ombe zikoke pamodzi.
11
Musamavala nsalu yosokonezeka yaubweya pamodzi ndi thonje.
12
Mudzipangire mphonje pangodya zinai za chofunda chanu chimene mudzifunda nacho.
13
Munthu akatenga mkazi, nalowana naye, namuda,
14
namneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kumveketsa dzina loipa, ndi kuti, Ndinamtenga mkazi uyu, koma polowana naye sindinapeza zizindikiro zakuti ndiye namwali ndithu;
15
pamenepo atate wa namwaliyo ndi mai wake azitenga ndi kutuluka nazo zizindikiro za unamwali wake wa namwaliyo, kunka nazo kwa akulu a mudzi kuchipata;
16
ndipo atate wa namwaliyo azinena kwa akulu, Ndinampatsa munthuyu mwana wanga wamkazi akhale mkazi wake, koma amuda;
17
ndipo, taonani, wamneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kuti, Sindinapeza zizindikiro za unamwali wake m'mwana wako wamkazi; koma si izi zizindikiro za unamwali wa mwana wanga wamkazi. Ndipo azifunyulula chovalacho pamaso pa akulu a mudziwo.
18
Pamenepo akulu a mudziwo azitenga munthuyu ndi kumkwapula;
19
ndi kumlipitsa masekeli makumi okhaokha khumi a siliva, ndi kuipereka kwa atate wa namwaliyo, popeza anamveketsa dzina loipa namwali wa Israele, ndipo azikhala mkazi wake, sakhoza kumchotsa masiku ake onse.
20
Koma chikakhala choona ichi, kuti zizindikiro zakuti ndiye namwali zidamsowa namwaliyo;
21
pamenepo azimtulutsa namwaliyo ku khomo la nyumba ya atate wake, ndipo amuna a mudzi wake azimponya miyala kuti afe; popeza anachita chopusa m'Israele, kuchita chigololo m'nyumba ya atate wake; chotero uzichotsa choipacho pakati panu.
22
Akampeza munthu alikugona ndi mkazi wokwatibwa ndi mwamuna; afe onse awiri, mwamuna wakugona ndi mkazi, ndi mkazi yemwe; chotero muzichotsa choipacho mwa Israele.
23
Pakakhala namwali, wosadziwa mwamuna, wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, ndipo anampeza m'mudzi mwamuna, nagona naye;
24
muziwatulutsa onse awiri kunka nao ku chipata cha mudzi uwo, ndi kuwaponya miyala kuti afe; namwaliyo popeza sanafuule angakhale anali m'mudzi; ndi mwamuna popeza anachepetsa mkazi wa mnansi wake; chotero muzichotsa choipacho pakati panu.
25
Koma mwamuna akapeza namwali wopalidwa bwenzi kuthengo, namgwira mwamunayo, nagona naye; pamenepo afe mwamuna yekha wogona naye;
26
koma namwaliyo musamamchitira kanthu; namwaliyo alibe tchimo loyenera imfa; pakuti mlandu uwu ukunga munthu waukira mnzake namupha;
27
pakuti anampeza kuthengo; namwali wopalidwa bwenziyo anafuula, koma panalibe wompulumutsa.
28
Munthu akapeza namwali wosadziwa mwamuna, ndiye wosapalidwa ubwenzi, nakamgwira nagona naye, napezedwa iwo,
29
pamenepo mwamuna amene anagona naye azipatsa atate wake wa namwaliyo masekeli makumi asanu a siliva, ndipo azikhala mkazi wake; popeza anamchepetsa; sakhoza kumchotsa masiku ake onse.
30
Munthu asatenge mkazi wa atate wake, kapena kuvula atate wake.
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 23 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34