bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Deuteronomy 14
Deuteronomy 14
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 15 →
1
Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu; musamadzicheka, kapena kumeta tsitsi pakati pa maso chifukwa cha akufa.
2
Popeza ndinu mtundu wa anthu opatulikira Yehova Mulungu wanu, ndipo Yehova anakusankhani mukhale mtundu wa anthu wa pa wokha wa Iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu okhala pankhope pa dziko lapansi.
3
Musamadya chonyansa chilichonse.
4
Nyamazi muyenera kumadya ndi izi: ng'ombe, nkhosa, ndi mbuzi,
5
ngondo, ndi nswala ndi mphoyo, ndi mphalapala, ndi ngoma, ndi nyumbu, ndi mbalale.
6
Ndipo nyama iliyonse yogawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, nibzikula, imeneyo muyenera kudya.
7
Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika chiboda: ngamira, ndi kalulu, ndi mbira, popeza zibzikula, koma zosagawanika chiboda, muziyese zodetsa;
8
ndi nkhumba, popeza igawanika chiboda koma yosabzikula, muiyese yodetsa; musamadya nyama yao, musamakhudza mitembo yao.
9
Mwa zonse zili m'madzi muyenera kumadya izi: zilizonse zili nazo zipsepse ndi mamba, zimenezi muyenera kumadya;
10
koma zilizonse zopanda zipsepse kapena mamba musamadya; muziyese zonyansa.
11
Mbalame zosadetsa zonse muyenera kumadya.
12
Koma izi ndi zimene simuyenera kumadya: mphungu, ndi nkhwazi, ndi chikambi,
13
ndi kamtema, ndi mphamba, ndi muimba monga mwa mtundu wake;
14
ndi khungubwi aliyense monga mwa mtundu wake;
15
ndi nthiwatiwa, ndi chipudo, ndi kakowa, ndi kabawi monga mwa mtundu wake;
16
ndi nkhutukutu, ndi manchichi, ndi tsekwe;
17
ndi vuwo, ndi dembo, ndi nswankhono;
18
ndi indwa, ndi chimeza, monga mwa mtundu wake, ndi sadzu, ndi mleme.
19
Ndipo zokwawa zonse zakuuluka muziyesa zonyansa; musamazidya.
20
Mbalame zonse zosadetsa muyenera kumadya.
21
Musamadya chinthu chilichonse chitafa chokha; muzipereka icho kwa mlendo ali m'mudzi mwanu, achidye ndiye; kapena uchigulitse kwa mlendo; popeza ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu. Musamaphika mwanawambuzi mu mkaka wa make.
22
Muzipereka ndithu limodzi la magawo khumi la zipatso zonse za mbeu zanu, zofuma kumunda, chaka ndi chaka.
23
Ndipo muzidye pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo m'mene asankhamo Iye, kukhalitsamo dzina lake; limodzi la magawo khumi la tirigu wanu, la vinyo wanu, ndi la mafuta anu, ndi oyamba kubadwa a ng'ombe zanu ndi a nkhosa ndi mbuzi zanu; kuti muphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu masiku onse.
24
Ndipo ikakutalikirani njira kotero kuti simukhoza kulinyamula, popeza malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha, kuikapo dzina lake, akutanimphirani; atakudalitsani Yehova Mulungu wanu;
25
pamenepo mulisinthe ndalama, ndi kumanga ndalama ikhale m'dzanja mwanu, ndi kupita ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha;
26
ndipo mugule ndi ndalamazo chilichonse moyo wanu ukhumba, ng'ombe kapena nkhosa, kapena vinyo, kapena chakumwa cholimba, kapena chilichonse moyo wanu ukufunsani; nimudye pomwepo pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kukondwera, inu ndi a pabanja panu.
27
Koma Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, musamamtaya, popeza alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi inu.
28
Pakutha pake pa zaka zitatu muzitulutsa magawo onse a magawo khumi a zipatso zanu za chaka icho, ndi kuwalinditsa m'mudzi mwanu;
29
ndipo abwere Mlevi, popeza alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi inu, ndi mlendo, ndi ana amasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala m'mudzi mwanu, nadye nakhute; kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni mu ntchito zonse za dzanja lanu muzichitazi.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34