bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Corinthians 1
1 Corinthians 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 2 →
1
Ndine, Paulo, amene mwa kufuna kwa Mulungu ndidaitanidwa kuti ndikhale mtumwi wa Khristu Yesu. Ndili pamodzi ndi mbale wathu, Sostene.
2
Tikulembera mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto. Mulungu adakupatulani mwa Khristu Yesu, ndipo adakuitanani kuti mukhale anthu akeake, pamodzi ndi anthu onse amene ponseponse amatama dzina la Ambuye Yesu Khristu mopemba. Iye ndiye Mbuye wathu ndi Mbuye waonso.
3
Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.
4
Nthaŵi zonse ndimayamika Mulungu wanga chifukwa cha inu, popeza kuti adakukomerani mtima mwa Khristu Yesu.
5
Zoonadi mwa Khristu mwakhala anthu olemera pa zonse, makamaka pa kulankhula ndi pa kudziŵa zinthu,
6
popeza kuti mau ochitira Khristu umboni akhazikika mwa inu.
7
Nchifukwa chake palibe mphatso yauzimu imene yakupereŵerani, pamene mukudikira kubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu.
8
Iye adzakulimbitsani mpaka chimalizo, kuti mudzakhale opanda cholakwa pa tsiku la Ambuye athu Yesu Khristu.
9
Mulungu ndi wokhulupirika, ndipo Iye ndiye amene adakuitanani kuti mukhale a mtima umodzi ndi Mwana wake Yesu Khristu Ambuye athu.
10
Abale, ndikukupemphani m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu, kuti muzivomerezana pa zimene munena. Pasakhale kupatulana pakati panu, koma muzimvana kwenikweni pokhala a mtima umodzi ndi a maganizo amodzi.
11
Pakuti ena a m'banja la Koloe andifotokozera kuti pali kukangana pakati panu, abale anga.
12
Chimene ndikufuna kunena nchakuti aliyense mwa inu akungonena zakezake. Wina akuti, “Ine ndine wa Paulo,” winanso akuti, “Ine ndine wa Apolo,” wina akuti, “Ine ndine wa Kefa,” winanso akuti, “Ine ndine wa Khristu.”
13
Kodi Khristu wagaŵika? Kodi adakuferani pa mtanda ndi Paulo? Kodi mudabatizidwa m'dzina la Paulo?
14
Ndimayamika Mulungu kuti pakati panupo sindidabatize wina aliyense, kupatula Krispo ndi Gayo basi.
15
Motero palibe amene anganene kuti adabatizidwa m'dzina langa.
16
Inde ndidabatizanso Stefanasi ndi a m'banja mwake, koma sindikumbukira kuti pali winanso amene ndidamubatiza.
17
Paja Khristu adandituma, osati kuti ndizibatiza ai, koma kuti ndizilalika Uthenga Wabwino. Ndipo ndiyenera kumaulalika mosagwiritsa ntchito luso lake la ulaliki, kuwopa kuti mtanda wa Khristu ungatheretu mphamvu.
18
Mau onena za imfa ya Khristu pa mtanda ndi chinthu chopusa kwa anthu amene akutayika, koma kwa ife amene tili pa njira ya chipulumutso, mauwo ndi mphamvu ya Mulungu.
19
Paja Malembo akuti, “Ndidzaononga nzeru za anthu anzeru, ndidzathetsa kuchenjera kwa anthu ochenjera.”
20
Nanga ali kuti anthu anzeru? Ali kuti aphunzitsi a Malamulo a Mose? Ali kuti anthu onyadira nzeru zamakono zapansipano? Monga Mulungu sadaonetse kuti kudalira nzeru zapansipano nkopusa?
21
Pakuti mwa nzeru zake Mulungu adakonzeratu kuti anthuwo asamdziŵe ndi nzeru zao. Koma kudamkomera Mulungu kupulumutsa anthu okhulupirira ndi mau opusa amene timalalika.
22
Ayuda amafuna kuwona zozizwitsa, pamene Agriki amafunafuna nzeru.
23
Koma ife timalalika Khristu amene adapachikidwa pa mtanda. Kwa Ayuda mau ameneŵa ndi okhumudwitsa, pamene kwa anthu a mitundu ina mauŵa ndi opusa.
24
Koma amene Mulungu adaŵaitana, kaya ndi Ayuda kaya ndi Agriki, onsewo amazindikira kuti Khristu ndi mphamvu ya Mulungu ndiponso nzeru ya Mulungu.
25
Pajatu chimene chimaoneka ngati kupusa kwa Mulungu, nchanzeru kupambana nzeru za anthu. Ndipo chimene chimaoneka ngati kufooka kwa Mulungu, nchamphamvu kupambana mphamvu za anthu.
26
Abale, taganizani m'mene munaliri pamene Mulungu adakuitanani. Pakati panu panalibe ambiri amene anthu ankaŵayesa anzeru. Panalibenso ambiri amphamvu, kapena obadwa m'mabanja omveka.
27
Koma Mulungu adasankha zimene anthu amaziyesa zopusa, kuti Iye anyazitse nazo anthu anzeru. Adasankhanso zimene anthu amaziyesa zofooka, kuti Iye anyazitse nazo anthu amphamvu.
28
Ndipo zimene anthu amaziyesa zachabe, zonyozeka ndi zosakhala zenizeni, Mulungu adazisankha kuti athetse mphamvu zinthu zimene iwowo amayesa kuti ndiye zenizeni.
29
Mulungu adachita zimenezi kuti pasakhale wina aliyense woti nkumadzitukumula pamaso pake.
30
Mulungu ndiye adakulunzanitsani ndi Khristu Yesu, ndipo adamsandutsa kuti akhale nzeru yathu. Chifukwa cha Yesu, timapezeka olungama pamaso pa Mulungu. Ndi Yesuyo amene amatisandutsa anthu akeake a Mulungu, ndiye amatipulumutsa.
31
Nchifukwa chake, monga Malembo anenera, “Wofuna kunyada, anyadire Ambuye.”
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16