bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Corinthians 7
1 Corinthians 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 8 →
1
Tsopano ndiyankhe zimene mudandifunsa m'kalata yanu. Nkwabwino kuti munthu asakwatire,
2
koma kuwopa dama, mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wakewake, ndipo mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wakewake.
3
Mwamuna azipereka kwa mkazi wake zomuyenerera zokhudza banja ngati mkazi wake, momwemonso mkazi azipereka kwa mwamuna wake zomuyenerera zokhudza banja ngati mwamuna wake.
4
Mkazi thupi lake si lokhalira iye yekha ai, ndi lokhaliranso ndi mwamuna wake yemwe. Momwemonso mwamuna thupi lake si lokhalira iye yekha ai, ndi lokhaliranso ndi mkazi wake yemwe.
5
Musamakanane, koma pokhapokha mutavomerezana kutero pa kanthaŵi kuti mudzipereke ku mapemphero. Pambuyo pake mukhalenso pamodzi, kuwopa kuti Satana angakuyeseni chifukwa cha kulephera kudzigwira.
6
Pamene ndikunena zimenezi, sindikuchita mokulamulani ai, koma mokulolani chabe.
7
Kwenikweni ndikadakonda kuti anthu onse akhale ngati ine, koma Mulungu adapatsa munthu aliyense mphatso yakeyake, wina mphatso yakuti, winanso yakuti.
8
Kwa amene sali pa banja, ndiponso kwa azimai amasiye, mau anga ndi aŵa: Nkwabwino kuti iwo akhalebe paokha choncho ngati ineyo.
9
Koma ngati sangathe kudziletsa, aloŵe m'banja, pakuti nkwabwino kuloŵa m'banja kupambana kupsa ndi moto wa zilakolako.
10
Kwa anthu am'banja lamulo langa, limenetu kwenikweni ndi lochokera kwa Ambuye, ndi ili: Mkazi asalekane ndi mwamuna wake.
11
Koma ngati amuleka, akhale wosakwatiwanso, kapena ayanjane nayenso mwamuna wakeyo. Chimodzimodzinso mwamuna asasudzule mkazi wake.
12
Kwa ena mau anga, osati a Ambuye ai, ndi aŵa: Ngati mkhristu ali ndi mkazi wachikunja, ndipo mkaziyo avomera kukhala naye, mwamunayo asathetse ukwatiwo.
13
Momwemonso ngati mkhristu wamkazi ali ndi mwamuna wachikunja, ndipo mwamunayo avomera kukhala naye, mkaziyo asathetse ukwatiwo.
14
Pakuti mwamuna wachikunja uja amadalitsidwa chifukwa cha mkazi wakeyo. Nayenso mkazi wachikunja uja amadalitsidwa chifukwa cha mwamuna wakeyo. Pakadapanda apo, bwenzi ana anu atakhala akunja, koma monga zilirimu, ndi ana a Mulungu.
15
Koma ngati wakunja uja afuna kuleka mkhristu, amuleke. Zikatero, ndiye kuti mkhristu wamwamunayo kapena wamkaziyo ali ndi ufulu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale ndi moyo wamtendere.
16
Kodi iwe, mkazi wachikhristu, ungadziŵe bwanji ngati udzampulumutsa mwamuna wako? Kapenanso iwe, mwamuna wachikhristu, ungadziŵe bwanji ngati udzapulumutsa mkazi wako?
17
Aliyense atsate moyo umene Ambuye adamkonzera, moyo umene Mulungu adamuitanira. Ndizo zimene ndimaŵalamula anthu onse amumpingo.
18
Ngati wina Mulungu adamuitana ali woumbalidwa, asavutike nkubisa kuumbala kwakeko. Chimodzimodzi ngati wina adamuitana ali wosaumbalidwa, asaumbalidwe.
19
Kuumbala si kanthu ai, kusaumbala si kanthunso. Kanthu nkutsata malamulo a Mulungu.
20
Aliyense angokhala monga momwe analiri pamene Mulungu adamuitana.
21
Kodi unali kapolo pamene Mulungu adakuitana? Usavutike nazo. Komanso ngati upeza mwai woti ulandire ufulu, uugwiritse ntchito mwaiwo.
22
Pakuti munthu amene anali kapolo pamene Ambuye adamuitana, ameneyo ndi mfulu ya Ambuye. Momwemonso amene anali mfulu pamene Ambuye adamuitana, ameneyo ndi kapolo wa Khristu.
23
Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono musasanduke akapolo a anthu.
24
Abale, aliyense angokhala pamaso pa Mulungu monga momwe analiri pamene Mulunguyo adamuitana.
25
Kunena za amene sali pa banja, ndilibe lamulo lochokera kwa Ambuye. Koma ndikuuzani maganizo anga, ngati munthu amene Ambuye adandichitira chifundo kuti ndikhale wokhulupirika.
26
Chifukwa cha masautso a nthaŵi ino, ndiyesa nkwabwino kuti munthu akhale monga momwe aliri.
27
Kodi ndiwe wapabanja? Usayese kuthetsa banja lako. Kodi ndiwe wopanda banja? Usayese kupeza banja.
28
Komabe ngati ukwatira, sukuchimwa ai. Ndipo ngati namwali akwatiwa, sakuchimwa ai. Komabe oloŵa m'banja adzakumana ndi zovuta m'moyo wao, ndipo pano ndingofuna kukupewetsani zovutazo.
29
Chimene ndikukuuzani, abale, nchakuti nthaŵi yachepa. Kuyambira tsopano anthu okwatira akhale monga ngati sadakwatire.
30
Amene akulira, akhale monga ngati sakulira, amene akukondwa, akhale monga ngati sakukondwa, amene akugula zinthu, akhale monga ngati sali nazo zinthuzo.
31
Ndipo amene akugwiritsa ntchito zinthu zapansipano, zisaŵagwire mtima zinthuzo. Pakuti dziko lino lapansi, monga liliri tsopanomu, likupita.
32
Ndidakakonda kuti pasakhale zokudetsani nkhaŵa. Munthu wosakwatira amangotekeseka ndi za Ambuye, kuganiza za m'mene angakondweretsere Ambuye.
33
Koma munthu wokwatira amatekeseka ndi zapansipano, kuganiza za m'mene angakondweretsere mkazi wake.
34
Motero amagwira njakata. Mkazi wosakwatiwa, kapenanso namwali, amangotekeseka ndi za Ambuye, kuti adzipereke kwa Ambuye m'thupi ndi mumzimu momwe. Koma mkazi wokwatiwa amatekeseka ndi zapansipano, kuganiza za m'mene angakondweretsere mwamuna wake.
35
Ndikunenatu zimenezi kufuna kuti ndikuthandizeni, osati kuti ndikuletseni ufulu wanu ai. Makamaka ndifuna kuti muzichita zonse moyenera, ndipo kuti muzidzipereka kwathunthu potumikira Ambuye.
36
Koma ngati wina akuganiza kuti akumlakwira namwali wake amene adamtomera, ndipo ngati namwaliyo unamwali wake ukupitirira, tsono munthuyo nkuganiza kuti ayenera kumkwatira, angathe kuchita zimenezo, si kuchimwa ai.
37
Komabe ngati wina, mwaufulu wake, popanda womukakamiza, watsimikiza kwenikweni kuti samkwatira namwali adamtomerayo, nayenso wachita bwino.
38
Ndiye kuti, munthu wokwatira namwali amene adamtomera, akuchita bwino, koma woleka osamkwatira, akuchita bwino koposa.
39
Mkazi amamangika ndi lamulo la ukwati, nthaŵi yonse pamene mwamuna wake ali moyo. Koma mwamuna wake akamwalira, ali ndi ufulu kukwatiwa ndi mwamuna amene iye afuna, malinga ukwatiwo ukhale wachikhristu.
40
Koma m'mene ndikuganizira ine, adzakhala wokondwa koposa ngati akhala wosakwatiwanso. Ndipo ndikuyesa inenso ndili naye Mzimu wa Mulungu.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16