bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Corinthians 3
1 Corinthians 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 4 →
1
Tsono ine, abale, sindidathe kulankhula nanu monga momwe ndimalankhulira ndi anthu amene ali ndi Mzimu Woyera. Koma ndidaayenera kulankhula nanu ngati anthu odalira zapansipano, kapenanso ngati ana akhanda m'moyo wanu wachikhristu.
2
Ndidakumwetsani mkaka, osakupatsani chakudya cholimba, chifukwa simukadatha kuchidya. Ngakhalenso tsopano simungathe kuchidya,
3
popeza kuti mukudalirabe zapansipano. Pakati panu pali kaduka ndi kukangana. Nanga zimenezi sizikutsimikiza kuti mukudalirabe zapansipano, ndipo kuti mumachita monga momwe amachitira anthu odalira zapansipanozo?
4
Mumangoti ali apa, “Ine ndine wa Paulo,” ali apa, “Ine ndine wa Apolo.” Kodi mukamatero simukuchita ngati anthu odalira zapansipano?
5
Kodi Apolo nchiyani? Paulonso nchiyani? Ndi atumiki chabe a Mulungu, amene adakufikitsani ku chikhulupiriro. Aliyense adangogwira ntchito imene Mulungu adampatsa.
6
Ineyo ndidabzala mbeu, Apolo nkuzithirira, koma amene adazimeretsa ndi Mulungu.
7
Motero wobzala kapenanso wothirira sali kanthu, koma Mulungu yekha amene amameretsa, ndiye ali kanthu.
8
Tsono wobzala sasiyana ndi wothirira, ndipo aliyense adzalandira mphotho yake molingana ndi ntchito imene adaigwira.
9
Komabe ife ndife okhaokha ogwira ntchito ya Mulungu, inuyo ndinu munda wa Mulungu, ndinunso nyumba ya Mulungu.
10
Popeza kuti Mulungu adachita kundituma, ndidakhazika maziko monga mmsiri waluso, ndipo wina akumanga pa mazikowo. Koma aliyense azichenjera pomanga.
11
Pajatu palibe maziko enanso amene wina aliyense angathe kukhazika osiyana ndi maziko amene alipo kale. Mazikowo ndi Yesu Khristu.
12
Pa mazikoŵa munthu angathe kumangapo ndi golide, siliva, miyala yamtengowapali, mitengo, udzu kapena mapesi.
13
Koma ntchito za munthu aliyense zidzaonekera poyera, pamene tsiku la chiweruzo lidzaziwonetsa. Pakuti tsikulo lidzafika ndi moto, ndipo motowo ndi umene udzayesa ntchito za munthu aliyense.
14
Zimene munthu adamanga pamazikopo zikadzakhalapobe, mwiniwakeyo adzalandira mphotho.
15
Koma zikadzanyeka ndi moto, sadzalandira mphotho. Inde mwiniwakeyo adzapulumukabe, koma monga ngati munthu amene wangopulumuka m'moto.
16
Kodi inu simudziŵa kuti ndinu nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu?
17
Ngati wina aliyense aononga nyumba ya Mulunguyo, Mulungu nayenso adzamuwononga ameneyo. Pakuti nyumba ya Mulungu ndi yopatulika, ndipo nyumbayo ndinu amene.
18
Tsono musadzinyenge. Ngati wina mwa inu adziyesa wanzeru, kunena za nzeru za masiku ano, ameneyo ayambe wakhala ngati wopusa, kuti asanduke wanzeru.
19
Zoonadi nzeru za anthu odalira zapansipano, nzopusa pamaso pa Mulungu. Pajatu Malembo akuti, “Mulungu amakola anthu anzeru m'kuchenjera kwao.”
20
Penanso Malembo akuti, “Ambuye amaŵadziŵa maganizo a anthu anzeru kuti ndi achabe.”
21
Nchifukwa chake pasakhale wina aliyense wonyadira anthu chabe. Zinthu zonse nzanu:
22
Paulo, Apolo ndi Kefa, dziko lapansi, moyo ndi imfa, zimene zilipo ndi zimene zilikudza. Koma ngakhale zonsezi nzanu,
23
inu ndinu ake a Khristu, ndipo Khristu ndi wake wa Mulungu.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16