bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Corinthians 15
1 Corinthians 15
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 16 →
1
Abale, ndifuna kukukumbutsani Uthenga Wabwino umene ndidakulalikirani. Mudaulandira, ndipo mudakhazikitsapo chikhulupiriro chanu molimba.
2
Mulungu adzakupulumutsani ndi Uthenga Wabwinowu, ngati musunga bwino mau ake monga ndidakulalikirani. Popanda kutero, bwenzi mutangokhulupirira pachabe.
3
Pajatu mau aakulu amene ndidakupatsani ndi omwewo amene inenso ndidalandira. Mauwo ndi akuti Khristu adafera machimo athu, monga Malembo anenera.
4
Adaikidwa m'manda, mkucha wake adauka, monga Malembo anenera.
5
Motero adaonekera Kefa, kenaka atumwi khumi ndi aŵiri aja.
6
Pambuyo pake adaonekera abale opitirira mazana asanu pa nthaŵi imodzi. Ambiri mwa iwowo akalipo, ena adamwalira.
7
Ndipo adaonekera Yakobe, kenaka atumwi onse.
8
Potsiriza, pambuyo pa onse adandiwonekeranso ineyo, ngakhale ndili ngati mpolo chabe.
9
Inetu ndine wamng'onong'onodi mwa atumwi onse. Sindine woyenera konse kuti ndizitchedwa mtumwi, pakuti ndinkazunza Mpingo wa Mulungu.
10
Koma chifukwa chakuti Mulungu adandikomera mtima, ndili monga ndilirimu. Ndipo kukoma mtima kwakeko sikunali kopanda phindu, popeza kuti ndidagwira ntchito koposa atumwi ena onse. Komabe si ndine ndidaigwira, koma mphamvu za Mulungu zimene zikundilimbikitsa.
11
Motero kaya ndi ineyo kaya ndi iwowo, zimene timalalika ndi zomwezo, zimene mudakhulupirira ndi zomwezonso.
12
Tsono popeza kuti chimene timalalika ndi chakuti Khristu adauka kwa akufa, bwanji ena mwa inu akunena kuti, “Anthu akufa sadzaukanso?”
13
Ngati akufa sadzauka, ndiye kuti Khristunso sadauke.
14
Tsono ngati Khristu sadauke, kulalika kwathu nkwachabe, ndipo chikhulupiriro chanu nchachabenso.
15
Ngati zili choncho, ndiye kuti ndife mboni zonama, tikuchita umboni wonama m'dzina la Mulungu, ponena kuti Mulungu adaukitsa Khristu. Ngati nzoonadi kuti akufa sauka, ndiye kuti Mulungu sadamuukitse Khristuyo.
16
Pakuti ngati akufa sauka, Khristunso sadauke.
17
Ndipotu ngati Khristu sadauke, chikhulupiriro chanu nchopanda pake, ndipo mukadali m'machimo anu.
18
Pamenepo nawonso amene adamwalira ali okhulupirira Khristu, adatayika ndithu.
19
Ngati taika chikhulupiriro chathu mwa Khristu chifukwa cha moyo uno wokha, ndiye kuti ndife omvetsa chisoni koposa anthu ena onse.
20
Koma ai, Khristu adauka ndithu kwa akufa. Pakati pa onse amene adafa, ndiye woyamba kuuka.
21
Pakuti monga imfa idadza pansi pano kudzera mwa munthu wina, momwemonso kuuka kwa akufa kudadza kudzera mwa munthu wina.
22
Monga anthu onse amamwalira chifukwa ndi ana a Adamu, momwemonso anthu onse adzauka chifukwa cholumikizana ndi Khristu.
23
Koma aliyense adzauka pa nthaŵi yake: woyambirira ndi Khristu, ndipo pambuyo pake, pamene Khristuyo adzabwera, nawonso amene ali ake adzauka.
24
Pamenepo chimalizo chidzafika. Khristu atathetsa ufumu wonse, ulamuliro wonse, ndi mphamvu zonse, adzapereka ufumu uja kwa Mulungu Atate.
25
Paja Khristu ayenera kulamulira mpaka atagonjetsa adani ake onse.
26
Mdani wotsiriza kumthetsa mphamvu, ndiye imfa.
27
Malembotu akuti, “Mulungu adamgonjetsera zinthu zonse.” Koma nchodziŵikiratu kuti pamene akuti “zinthu zonse,” sakuphatikizapo ndi Mulungu yemwe, amene adagonjetsera Khristu zinthu zonse.
28
Koma pamene zonse zidzakhala zitagonjera Khristu, pamenepo Mwana wa Mulungu nayenso adzagonjera Mulungu, amene adamgonjetsera zinthu zonse. Adzachita zimenezi kuti Mulungu akhale wolamulira aliyense kwathunthu.
29
Ngati Yesu sadauke kwa akufa, nanga amafunanji anthu amene amabatizidwa m'malo mwa amene adafa? Ngati akufa sauka konse, nanga chifukwa chiyani anthu amabatizidwa m'malo mwao?
30
Nanga pamenepo ifenso timakhaliranji m'zoopsa nthaŵi zonse?
31
Abale anga, imfa ndimayenda nayo tsiku ndi tsiku. Ndikunenetsa zimenezi chifukwa ndimakunyadirani mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
32
Nanga pamene ndidalimbana ndi zilombo ku Efeso, ndidapindulapo chiyani, ngati ndinkatsata maganizo a anthu chabe? Ndiyetu ngati akufa sauka, tizingochita monga amanenera kuti, “Tiyeni tizidya ndi kumwa, pakuti maŵa tikufa.”
33
Musadzinyenge. “Paja kuyanjana ndi anthu ochimwa kumaononga khalidwe.”
34
Mudzidzimuke mumtima mwanu, ndipo muleke kuchimwa. Ena mwa inu sadziŵa Mulungu konse. Ndikukuuzani zimenezi kuti muchite manyazi.
35
Koma kapena wina nkufunsa kuti, “Kodi akufa adzauka bwanji? Kodi adzakhala ndi thupi lotani?”
36
Ati kupusa ati! Mbeu imene umafesa, siingamere ndi kukhala moyo itapanda kufa.
37
Ndipo chimene ufesa, si mmera umene udzatuluka ai, koma ndi njere chabe, kaya ndi ya tirigu, kapena ya mtundu wina uliwonse.
38
Koma Mulungu amaisandutsa mmera monga momwe Iye akufunira, mbeu iliyonse mmera wakutiwakuti.
39
Mnofu sukhala wa mtundu umodzi. Pali mnofu wina wa anthu, wina wa nyama, wina wa mbalame, ndi wina wa nsomba.
40
Palinso zolengedwa zakuthambo, ndi zina zapansipano. Koma ulemerero wa zakuthambo ndi wosiyana ndi ulemerero wa zapansipano.
41
Dzuŵa lili ndi kuŵala kwake, mwezi uli ndi kuŵala kwake kosiyana ndi kwa dzuŵa kuja, nyenyezinso zili ndi kuŵala kwake kosiyana ndi kwa zina zija. Ngakhale nyenyezizo zimasiyananso kuŵala kwake.
42
Zidzateronso pamene akufa adzauka. Thupi loikidwa m'nthaka ngati mbeu yofesa, limaola, koma likadzauka, lidzakhala losaola.
43
Thupi loikidwa m'manda, ndi lonyozeka ndi lofooka, koma likadzauka lidzakhala lokongola ndi lamphamvu.
44
Thupi loikidwa m'manda, ndi lamnofu chabe, koma likadzauka, lidzakhala lauzimu. Ngati pali thupi lamnofu, palinso thupi lauzimu.
45
Paja Malembo akuti, “Munthu woyamba uja, Adamu, adachita kusanduka chinthu chamnofu chokhala ndi moyo.” Koma Adamu wotsiriza adakhala chinthu chauzimu chopatsa moyo.
46
Loyamba si thupi lauzimu ai. Loyamba ndi lamnofu, pambuyo pake lauzimu.
47
Adamu woyamba uja anali wochokera ku dothi, anali wapansipano. Koma Khristu, Adamu wachiŵiri uja, anali wochokera Kumwamba.
48
Anthu onse apansipano ali ngati Adamu wopangidwa ndi dothi uja. Ndipo onse amene ali a Kumwamba, ali ngati Khristu wa Kumwamba.
49
Monga takhala ofanafana ndi Adamu, munthu wopangidwa ndi dothi uja, momwemonso tidzakhala ofanafana ndi Khristu, munthu wa Kumwamba.
50
Abale, chimene ndikunena nchakuti munthu ndi thupi lake lamnofuli sangathe kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu, ndipo zimene zimaola, sizingathe kuloŵa kumene zinthu siziwola.
51
Mvetsetsani, ndikuuzeni chinsinsi. Sikuti tonse tidzamwalira, komabe tonse tidzasandulika.
52
Zidzachitika mwadzidzidzi, pa kamphindi ngati kuphethira kwa diso, pamene lipenga lotsiriza lidzalira. Likadzaliratu lipengalo, akufa adzauka ndi matupi amene sangaole, ndipo ife tidzasandulika.
53
Pakuti thupi lotha kuwolali liyenera kusanduka losatha kuwola, ndipo thupi lotha kufali liyenera kusanduka losatha kufa.
54
Tsono thupi lotha kuwolali likadzasanduka losatha kuwola, ndipo thupi lotha kufali likadzasanduka losatha kufa, pamenepo zidzachitikadi zimene Malembo adanena kuti, “Imfa yagonjetsedwa kwathunthu.”
55
“Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti? Iwe imfa, ululu wako uli kuti?”
56
Ululu wake wa imfa ndi uchimo, ndipo chimene chimapatsa uchimo mphamvu, ndi Malamulo.
57
Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
58
Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16