bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Corinthians 16
1 Corinthians 16
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
1
Kunena za zopereka zothandizira akhristu a ku Yerusalemu, inunso muchite monga momwe ndidalongosolera m'mipingo ya ku Galatiya.
2
Pa tsiku loyamba la sabata, aliyense mwa inu azipatulapo kanthu, potsata momwe wapezera. Zimene wapatulazo azisunge kunyumba, kuti pasakakhalenso kusonkhasonkha ine ndikabwera.
3
Tsono ndikadzafika, ndidzaŵapatsa makalata anthu amene mungaŵasankhe, ndipo ndidzaŵatuma kuti akapereke mphatso yanuyo ku Yerusalemu.
4
Koma ngati nkofunika kuti inenso ndipite, tidzapitira limodzi.
5
Ndidzafika kwanuko nditadutsa dziko la Masedoniya, pakuti ndingodzerako ku Masedoniyako.
6
Koma kapena kwanuko ndidzakhala kanthaŵi, kapenanso nyengo yonse yachisanu. Ndifuna kuti pambuyo pake mudzandithandize kupitiriza ulendo wanga kulikonse kumene ndingapite.
7
Ulendo umenewo sindifuna kungokuwonani chidule modutsa chabe, koma ndikuyembekeza kukhala nanu kanthaŵi ndithu, Ambuye akalola.
8
Koma ndikhala ku Efeso kuno mpaka chikondwerero cha Pentekoste.
9
Pakuti pano mwai ulipo woti nkuchita zazikulu, ndiponsotu adani alipo ambiri.
10
Ngati Timoteo afika kwanuko, samalani kuti pasakhale kanthu komdetsa nkhaŵa pakati panu, pakuti iyenso akugwira ntchito ya Ambuye, monga ine.
11
Tsono wina aliyense asamnyoze, koma mumthandize kupitiriza ulendo wake mwamtendere kubwerera kuli ine kuno. Paja ndikumuyembekeza pamodzi ndi abale ena.
12
Kunena za mbale wathu, Apolo, ndamuumiriza kolimba kuti pamodzi ndi abale ena abwere kwanuko kudzakuwonani, koma iye sadafune kupita tsopano. Akadzapeza mpata wabwino, adzabwera.
13
Khalani maso, khalani okhazikika m'chikhulupiriro chanu, chitani chamuna, khalani amphamvu.
14
Zonse zimene muchita, muzichite mwachikondi.
15
Abale, mukudziŵa kuti Stefanasi ndi a m'banja mwake ndiwo adayambirira kuloŵa chikhristu m'dziko la Akaiya. Ndipo akhala akudzipereka kutumikira anthu a Mulungu.
16
Tsono ndikukupemphani kuti inunso muziŵamvera anthu otere, ndiponso aliyense wogwira ntchito ndi kutumikira modzipereka pamodzi nawo.
17
Ndakondwa kuti Stefanasi, Fortunato ndi Akaiko afika, pakuti ngakhale inu simuli nane, iwo achita ngati kuloŵa m'malo wanu.
18
Adandisangulutsa ine monga adasangulutsanso inu. Anthu otere muziŵalemekeza.
19
Mipingo ya ku dziko la Asiya ikuti moni. Akwila ndi Prisika, pamodzi ndi mpingo umene umasonkhana m'nyumba mwao, akuti moni kwa inu nonse, akhristu anzao.
20
Abale onse akuti moni. Mupatsane moni mwa chikondi chenicheni.
21
Ineyo Paulo, ndikuchita kulemba ndekha mau aŵa akuti “Moni.”
22
Ngati munthu sakonda Ambuye, akhale wotembereredwa. Maranatha! Ambuye athu, bwerani!
23
Ambuye Yesu akudalitseni.
24
Chikondi changa chikhale pa inu nonse, mwa Khristu Yesu.
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16