bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Corinthians 4
1 Corinthians 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 5 →
1
Muzitiwona ngati antchito a Khristu, ngati akapitao osamala zinsinsi za Mulungu.
2
Chofunika chachikulu pa akapitao otere nchakuti akhale okhulupirika.
3
Kunena za ine ndekha, ndilibe nazo kanthu ngati ndiweruzidwa ndi inu, kapenanso ndi bwalo lina lililonse la anthu. Ndiponsotu ngakhale mwiniwakene sindidziweruza ndekha ai.
4
Ndilibe kanthu konditsutsa mumtima mwanga, komabe ngakhale chimenechi si chitsimikizo chakuti ndine wolungama. Ondiweruza ndi Ambuye basi.
5
Motero musaweruziretu munthu aliyense, Ambuye asanabwere. Iwo ndiwo adzaunika pa zonse zobisika mu mdima, ndipo adzaulula maganizo a m'mitima mwa anthu. Pamenepo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko chomuyenerera.
6
Abale, zimene ndanenazi nzokhudza ine ndi Apolo. Ndifuna kuti zimenezi zikuphunzitseni tanthauzo la mau aja akuti, “Musapitirire zimene Malembo akunena.” Nchifukwa chake musamanyadira wina, ndi kupeputsa mnzake.
7
Nanga adakusiyanitsa ndi anthu ena ndani? Kaya uli ndi chiyaninso chimene sudachite kuchilandira? Tsono ngati udachita kuzilandira, ukunyadiranji ngati kuti sudangozilandira chabe?
8
Ndiye kuti muli nazo kale zonse zimene mumasoŵa! Ndiye kuti mwalemera kale! Ndiye kuti mwasanduka mafumu popanda ife! Ndikadakondwera mukadakhaladi mafumu, kuti ifenso tikhale mafumu pamodzi nanu.
9
Ndikuwona kuti atumwife Mulungu adatipatsa malo a kuthungo kwenikweni, ngati anthu oti akukaphedwa. Ndithu tasanduka ngati chinthu chochiwonetsa kwa zolengedwa zonse, osati anthu okha ai, komanso ndi angelo omwe.
10
Ife ndife opusa chifukwa cha Khristu, koma inu ndinu anzeru mwa Khristu. Ife ndife ofooka, koma inu ndinu amphamvu. Inu mumalandira ulemu, koma ife timanyozedwa.
11
Mpaka tsopano lino timamva njala ndi ludzu, ndipo ndife ausiŵa. Anthu akutimenya, ndipo tilibe pokhala penipeni.
12
Tikugwira ntchito kolimba ndi manja athu kuti tidzisunge. Anthu akamatichita chipongwe, timapempha kuti Mulungu aŵadalitse. Anthu akamatizunza, timangopirira.
13
Anthu akamatilalatira, timangoŵayankha moleza. Tasanduka onyozeka, ngati zinyatsi za dziko lapansi, ndipo mpaka tsopano anthu onse akutiyesa zinyalala.
14
Ndikukulemberani zonsezi, osati kuti ndikuchititseni manyazi, koma kuti ndikulangizeni, chifukwa ndinu ana anga okondedwa.
15
Ngakhale mutakhala nawo aphunzitsi ambirimbiri m'moyo wanu wachikhristu, simukhala ndi atate ambiri ai. Pajatu m'moyo wanu wachikhristu ine ndidachita ngati kukubalani pakukulalikirani Uthenga Wabwino.
16
Ndikukupemphani tsono kuti muzinditsanzira.
17
Nchifukwa chake ndakutumizirani Timoteo, mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye. Iyeyu adzakukumbutsani za mayendedwe anga achikhristu, amene sasiyana ndi zimene ndimaphunzitsa ponseponse m'mipingo yonse.
18
Ena mwayamba kudzitukumula, monga ngati sindidzabwerako kwanu.
19
Koma Ambuye akalola, ndidzabwera kwanuko posachedwa. Pamenepo ndidzadziŵa zimene odzitukumulawo angathe kuchita, osati zimene amangonena chabe.
20
Pakuti mu Ufumu wa Mulungu chachikulu si mau chabe, koma ntchito.
21
Nanga mukufuna chiyani? Mukufuna kuti ndidzabwere kwanuko ndi mkwapulo, kapena ndi mtima wachikondi ndi wofatsa?
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16