bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Corinthians 9
1 Corinthians 9
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 10 →
1
Kodi sindine mfulu? Kodi sindine mtumwi? Kodi suja ine ndidamuwona Yesu Ambuye athu? Kodi suja inu ndinu zipatso za ntchito yanga yogwirira Ambuye?
2
Ngakhaletu ena sandiyesa mtumwi, koma kwa inu ndine mtumwi ndithu, pakuti moyo wanu wachikhristu ndi umboni wakuti ndinedi mtumwi.
3
Zimene ndimaŵayankha ofufuza za ine ndi izi:
4
Kodi si koyenerera kwa ife kumalandira chakudya ndi chakumwa?
5
Kodi si koyenerera kwa ife kuti ŵaakazi azitsagana nafe pa maulendo athu, monga zikuchitikira ndi atumwi ena ngakhalenso abale a Ambuye ndiponso Kefa.
6
Kodi ine ndi Barnabasi, ndife tokha oyenera kugwira ntchito zamanja kuti tizidzipezera tokha zotisoŵa.
7
Kodi alipo msilikali womadzipezera yekha zofunika zonse? Kodi alipo munthu wobzala mpesa, koma osadyako zipatso zake? Kodi alipo munthu wokhala ndi ziŵeto, koma osamwako mkaka wake?
8
Kodi zimene ndikunenazi ndi nzeru za anthu chabe? Suja Malamulo a Mose amanena zomwezi?
9
Paja timaŵerenga m'Malamulowo kuti, “Usaimange pakamwa ng'ombe pamene ikupuntha tirigu.” Kodi pamene adanena zimenezi, Mulungu adangosamala za ng'ombe zokha?
10
Kodi sankanena zimenezi makamaka chifukwa cha ife? Adazilembadi chifukwa cha ife, pakuti wolima ndiponso wopuntha, onsewo amagwira ntchito yao ndi chiyembekezo chakuti nawonso adzalandirako kanthu pa zokolola.
11
Ngati ife tidafesa zabwino zauzimu pakati panu, nanga tilekerenji kulandira kwa inu zotisoŵa m'moyo wathu wathupi?
12
Ngati ena adziyesa kuti ndi oyenera kulandira zimenezi kwa inu, nanga ife sindiye oyenera koposa iwowo kuzilandira? Komabe kuyenera kumeneku sitidakugwiritse ntchito ai. Makamaka tidapirira zonse, kuwopa kuti tingachedwetse anthu mwa njira iliyonse kulandira Uthenga Wabwino wonena za Khristu.
13
Kodi simudziŵa kuti otumikira m'Nyumba ya Mulungu, amadya chakudya cha m'Nyumbamo, ndipo kuti opereka nsembe pa guwa lansembe, amalandira nao zansembezo?
14
Momwemonso Ambuye adalamula kuti olalika Uthenga Wabwino, azilandira zoŵasunga pakulalika Uthengawo.
15
Koma ineyo sindinkagwiritsa ntchito konse lamulo limeneli. Ndiponso sindikulemba kalatayi chifukwa chofuna kuligwiritsa ntchito kumene. Kwenikweni ndikadakonda kuti ndife, kupambana kuti wina andichotsere chifukwa chimene ndimanyadira.
16
Komabe pamene ndikulalika Uthenga Wabwino, apo pokha palibe ponyadira ai, popeza kuti ndi Ambuye amene adachita kundilamula zimenezo. Tsoka kwa ine ngati sindiulalika Uthenga Wabwinowo.
17
Ngatitu ndikugwira ntchitoyi mofuna ine ndekha, ndiye kuti ndilandirapo mphotho. Koma ngati ndiigwira mosafuna ine ndekha, ndiye kuti ntchitoyo ndi udindo umene Ambuye adandipatsa.
18
Pamenepo tsono mphotho yanga ndi yotani? Mphotho yanga ndi yakuti ndikamalalika Uthenga Wabwino, ndizingoulalika mwaulere, osafuna kulandirapo malipiro aja amene ndikadayenera kulandira polalika Uthenga Wabwinowo.
19
Ndine mfulu, osati kapolo wa munthu wina aliyense ai, komabe ndidadzisandutsa kapolo wa anthu onse, kuti ndikope anthu ambiri.
20
Kwa Ayuda ndidakhala ngati Myuda, kuti ndiŵakope. Ngakhale ineyo sindilamulidwa ndi Malamulo a Mose, komabe kwa Ayuda amene ali olamulidwa ndi Malamulowo, ndidakhala ngati iwo omwe, kuti ndiŵakope.
21
Kwa amene alibe Malamulo a Mose, ndidakhala ngati iwo omwe, kuti ndiŵakope. Sindiye kuti ndilibe Malamulo a Mulungu ai, popeza kuti ndili nawo malamulo a Khristu.
22
Kwa amene ali ndi chikhulupiriro chofooka, ndidakhala ngati wa chikhulupiriro chofooka, kuti ndiŵakope ofookawo. Kwa anthu onse ndidakhala ngati iwo omwe, kuti ngati nkotheka ndikope ena mwa iwo.
23
Zonsezi ndimazichita chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti inenso ndilandire nao madalitso a Uthengawo.
24
Monga inu simudziŵa kuti pa mpikisano wa liŵiro onse amathamanga, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphotho? Tsono kuthamanga kwanu kukhale kwakuti nkukalandira mphothoyo.
25
Aliyense wothamanga pa mpikisano wa liŵiro amadziletsa pa zonse. Iwowo amachita zimenezi kuti akalandire mphotho ya nkhata yamaluŵa yotha kufota. Koma mphotho imene ife tidzalandira, ndi yosafota.
26
Nchifukwa chake ndimathamanga monga munthu wodziŵa kumene walinga. Ndiponso ndikamachita mpikisano womenyana, sindichita ngati munthu amene angomenya mophonya.
27
Ndimazunza thupi langa ndi kuligonjetsa, kuti likhale ngati kapolo wondimvera. Ndimachita zimenezi kuwopa kuti ine ndemwe, amene ndidaitana ena ku mpikisano, ndingapezeke wosayenera kuchita nao mpikisanowo.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16