bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Corinthians 10
1 Corinthians 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 11 →
1
Abale, ndifuna kuti mudziŵe zimene zidaŵachitikira makolo athu akale aja. Onse adayenda mu mthunzi wa mtambo, ndipo onse adaoloka Nyanja Yofiira.
2
Motero mumtambomo ndi m'nyanjamo onsewo adachita ngati kubatizidwa ndi kukhala amodzi ndi Mose.
3
Onse ankadya chakudya chauzimu chimodzimodzi.
4
Onse ankamwanso chakumwa chauzimu chimodzimodzi, pakuti analikumwa m'thanthwe lauzimu limene linkaŵatsatira. Thanthwelo linali Khristu yemwe.
5
Komabe ambirimbiri mwa iwo Mulungu sadakondwere nawo, kotero kuti adafera m'chipululu.
6
Tsono zimene zidachitikazi ndi zitsanzo zotichenjeza ife, kuti tisamasirira zoipa monga adaachitira iwowo.
7
Tisakhale opembedza mafano, monga analiri ena mwa iwo. Paja Malembo akuti, “Anthu adakhala pansi kuti adye ndi kumwa, kenaka nkuimirira kuti azivina.”
8
Tisachite dama monga momwe adaachitira ena mwa iwo: paja pa tsiku limodzi adafa anthu zikwi makumi aŵiri ndi zitatu.
9
Tisapute Ambuye monga momwe adaaŵaputira ena mwa iwo: paja anthuwo adaphedwa ndi njoka.
10
Musadandaule monga momwe adaadandaulira ena mwa iwo: paja adaphedwa ndi mngelo wodzetsa imfa.
11
Zonsezi zidaŵagwera makolo athuwo kuti zikhale zoŵachenjeza. Ndipo zidalembedwa kuti tipezepo phunziro ifeyo, amene tikuyandikira nthaŵi ya kutha kwa zonse.
12
Tsono amene akuganiza kuti waimirira molimba, achenjere kuti angagwe.
13
Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.
14
Tsono okondedwa anga, pewani kupembedza mafano.
15
Ndikulankhula nanu ngati anthu anzeru. Muweruze nokha zimene ndikunenazi.
16
Nanga chikho chimene timachidalitsa mothokoza Mulungu, kodi suja timaphatikizana ndi magazi a Khristu tikamweramo? Nanga mkate umene timaunyema, kodi suja timaphatikizana ndi thupi la Khristu tikaudya?
17
Popeza kuti mkate ndi umodzi wokha, ife tonse, ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, chifukwa tonse timagaŵana mkate umodzi womwewo.
18
Onani zimene amachita Ayuda. Nanga amene amadyako zoperekedwa nsembe, kodi suja amachita nao miyambo ya pa guwa lansembelo?
19
Tsono tanthauzo la zimene ndikunenazi nchiyani? Kodi ndiye kuti nsembe yoperekedwa kwa fano nkanthu? Kapena kuti fanolo nkanthu?
20
Iyai, koma kuti zimene anthu akunja amapereka nsembe, amapereka kwa Satana, osati kwa Mulungu. Sindifuna kuti inu muyanjane ndi Satana.
21
Simungathe kumwera m'chikho cha Ambuye nkumweranso m'chikho cha Satana. Simungathe kudyera pa tebulo la Ambuye nkudyeranso pa tebulo la Satana.
22
Kodi tichite kuŵaputa dala Ambuye? Kodi mphamvu zathu nkupambana zao?
23
Zinthu zonse nzololedwa, koma si zonse zili ndi phindu. Zonse nzololedwa, koma si zonse zimathandiza.
24
Munthu asamangodzifunira yekha zabwino, koma makamaka azifunira anzake zabwino.
25
Mungathe kudya nyama iliyonse imene amagulitsa pa msika, osafunsa mafunso okhudzana ndi m'mene mtima wanu umamvera.
26
Paja Malembo akuti, “Dziko lapansi ndi zonse zam'menemo ndi za Chauta.”
27
Mkunja akakuitanani kuti mukadye naye, inuyo nkuvomera kupitako, mukadye chilichonse chimene akakupatseni. Musakafunse mafunso okhudzana ndi m'mene mtima wanu umamvera.
28
Koma wina akakuuzani kuti, “Nyama iyi idaperekedwa kwa mafano,” apo ndiye musadye nyamayo. Chifukwa cha amene wakuuzayo, usadye nyamayo, kuwopa kuti mtima ungavutike.
29
Osati kuti iweyo ungavutike mu mtima ai, koma iye uja amene wakuuzayo. Pamenepo udzati, “Kodi ufulu wanga utsekerezedwe chifukwa munthu wina mtima wake ukumuvuta?
30
Ngati ine ndikuthokoza Mulungu chifukwa cha chakudya changa, nanga munthu angandinyoze bwanji chifukwa cha chakudya chimene ndikuchilandira mothokoza Mulungu?”
31
Tsono, kaya mulikudya, kaya mulikumwa, kaya mukuchita chilichonse, muzichita zonse kuti mulemekeze Mulungu.
32
Moyo wanu ukhale wosaphunthwitsa Ayuda, kapena anthu a mitundu ina, kapenanso Mpingo wa Mulungu.
33
Muzichita monga momwe ndimachitira ine. Ndimayesa kukondweretsa anthu onse pa zonse. Sindifunafuna zokomera ineyo, koma ndimafunafuna zokomera anthu onse, kuti apulumuke.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16