bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Corinthians 5
1 Corinthians 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 6 →
1
Mbiri yawanda ponseponse yonena kuti pakati panu pali dama. Ndipo damalo ndi la mtundu wakuti ndi anthu akunja omwe sachita. Ndamva ndithu kuti munthu wina akukhala ndi mkazi wa bambo wake.
2
Ndipo inu mukudzitukumulabe! Kwenikweni mukadayenera kumva chisoni, ndi kumchotsa pakati panu munthu amene adachita zimeneziyo.
3
Kunena za ine, ngakhale sindili nanu pamodzi, komabe mtima wanga uli nanu ndithu. Mwakuti ndamuweruza kale munthu amene adachita zimeneziyo, monga ngati ndili nanu pamodzi.
4
Tsono mutasonkhana m'dzina la Ambuye Yesu, inenso m'maganizo ndili nanu pomwepo, ndi mphamvu ya Ambuye athu Yesu,
5
munthuyo mumpereke kwa Satana, kuti thupi lake liwonongedwe, ndipo pakutero mzimu wake udzapulumutsidwe pa tsiku la Ambuye.
6
Pamenepo palibe choti inu nkunyadira ai. Kodi simuŵadziŵa mau aja akuti, “Chofufumitsira buledi chapang'ono chimafufumitsa mkate wonse?”
7
Muchotse chofufumitsira chakalechi cha uchimo, kuti mukhale oyera mtima ndithu, ngati buledi watsopano wosafufumitsa, monga momwe muliri ndithu, pakuti Khristu, Mwanawankhosa wathu wa Paska, adaphedwa kale ngati nsembe.
8
Tiyeni tsono, tichite chikondwererocho, osati ndi chofufumitsira chakale chija cha uchimo ndi cha kuipa mtima, koma ndi buledi wosafufumitsa, wa kuyera mtima ndi wa choona.
9
M'kalata imene ndidaakulemberani, ndidaakuuzani kuti musamayanjane nawo anthu adama.
10
Sindiye kuti muziŵapewa anthu onse apansipano amene ali adama, aumbombo, achifwamba, kapena opembedza mafano ai. Kuti mutero kukadafunika kuti mungochokamo m'dziko lino lapansi.
11
Koma ndidaakulemberani kuti musamayanjane ndi munthu amene amati ndi mkhristu, pamene chikhalirecho ndi munthu wadama, kapena waumbombo, wopembedza mafano, waugogodi, chidakwa, kapena wachifwamba. Munthu wotere musamadye naye nkomwe.
12
Nanga kuweruza anthu amene adakali kunja, ndi ntchito yanga ngati? Si koma amene ali mu mpingo ndiwo muyenera kuŵaweruza?
13
Ndi Mulungu amene amaweruza anthu akunjawo. Paja mau a Mulungu akuti, “Munthu woipayo mumchotse pakati panu.”
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16