bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Amos 1
Amos 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 2 →
1
Naŵa mau a Amosi amene ankaŵeta nkhosa ku Tekowa. Zimenezi, zodzachitikira Aisraele, Chauta adamuululira pa nthaŵi ya Uziya, mfumu ya ku Yuda, ndi pa nthaŵi ya Yerobowamu, mwana wa Yowasi, mfumu ya ku Israele, kutatsala zaka ziŵiri kuti chivomezi chija chichitike.
2
Amosi adati, “Chauta akukhuluma ku Ziyoni, mau ake akumveka ngati bingu ku Yerusalemu. Nchifukwa chake mabusa akuuma, msipu wa pa phiri la Karimele ukufota.”
3
Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa anthu a ku Damasiko akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo ankazunza anthu a ku Giliyadi mwankhanza.
4
Tsono Ine ndidzaponya moto pa nyumba ya Hazaele, ndipo motowo udzatentha malinga a Benihadadi.
5
Ndidzathyola mpiringidzo woteteza mzinda wa Damasiko. Ndidzaonongeratu mfumu yolamulira ku Chigwa cha Aveni, ndiponso iye amene akugwira ndodo yaufumu ku Betedeni. Anthu a ku Siriya adzatengedwa ukapolo kupita nawo ku dziko la Kiri.” Akuterotu Chauta.
6
Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa anthu a ku Gaza akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo adatenga mtundu wathunthu wa anthu kunka nawo ku ukapolo, ndipo adaupereka ku Edomu.
7
Tsono Ine ndidzaponya moto pa makoma ozinga Gaza, udzatentha malinga ake.
8
Ndidzaonongeratu onse okhala ku Asidodi, kudzanso iye amene akugwira ndodo yaufumu ku Asikeloni. Ndidzakantha mzinda wa Ekeroni ndi dzanja langa, ndipo Afilisti onse otsalira adzaonongeka.” Akuterotu Ambuye Chauta.
9
Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa anthu a ku Tiro akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo adapereka mtundu wathunthu wa anthu ku Edomu, osasunga chipangano chaubale chija.
10
Ndiye Ine ndidzaponya moto pa makoma ozinga Tiro, ndipo motowo udzatentha malinga ake.”
11
Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa anthu a ku Edomu akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo adathamangitsa abale ao lupanga lili kumanja, popanda nchifundo chomwe. Ndiponso anali ndi ukali wosatonthozeka, ndi mkwiyo wosapozeka.
12
Ndiye Ine ndidzaponya moto pa mzinda wa Temani, ndipo motowo udzapsereza ndi malinga a ku Bozira omwe.”
13
Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa Aamoni akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo pofuna kufutuza malire ao, adatumbula akazi apakati ku Giliyadi,
14
Ndiye Ine ndidzaponya moto pa makoma a ku Raba, ndipo motowo udzapsereza malinga ake. Padzakhala kufuula kwakukulu pa tsiku lankhondolo, kumenyana kudzakhala kwafumbi ngati mkuntho wa kamvulumvulu.
15
Tsono mfumu yao idzatengedwa kunka ku ukapolo, iyoyo pamodzi ndi nduna zake.” Akuterotu Chauta.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
Recommended Reading
Commentary
Amos Commentaries
→
Devotional
Amos Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→