bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Amos 5
Amos 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 6 →
1
Inu banja la Israele imvani mau aŵa, amene ndikukuuzani mwadandaulo:
2
“Namwali Israele wagwa chonse osati nkudzukanso ai. Wagwa ndi kuiŵalika pa dziko lake, popanda wina womdzutsa.”
3
Zimene akunena Ambuye Chauta ndi izi: “Mzinda umene udapita ku nkhondo ndi anthu chikwi udzatsala ndi anthu zana limodzi chabe. Ndipo umene udapita ku nkhondo ndi anthu zana limodzi, udzatsala ndi anthu khumi okha a m'banja la Israele.”
4
Mau a Chauta ouza banja la Israele ndi aŵa: “Muchite zimene Ine ndifuna, kuti mukhalebe ndi moyo,
5
koma musasonkhane ku Betele, ndipo musakaloŵe ku Giligala, kapena kuwolokera ku Beereseba. Ndithu a ku Giligala adzatengedwa kupita ku ukapolo, ndipo Betele adzaonongekeratu.”
6
Muchite zimene Chauta afuna, kuti mukhalebe ndi moyo. Mukapanda kutero, adzatentha banja la Yosefe ngati moto, ndipo motowo udzapsereza a ku Betele popanda wina wouzimitsa.
7
Tsoka kwa inu amene mumasandutsa chilungamo kuti chikhale choipa, inu amene mumanyoza zolungama.
8
Iye uja ndiye amene adalenga nyenyezi za Akamwiniatsatana ndiponso Nsangwe, ndiye amene amasandutsa mdima kuti ukhale m'maŵa nasandutsa usana kuti ukhale usiku. Ndiye amene amaitana madzi am'nyanja ndi kuŵathira pa dziko lapansi. Dzina lake ndi Chauta.
9
Ndiyenso amene amakantha olamulira ankhanza, ndiye amene amagumula malinga ao.
10
Inu mumadana ndi muweruzi wodzudzula zosalungama, mumanyansidwa ndi wokamba zoona pa bwalo lamilandu.
11
Mumapondereza anthu osauka ndi kuŵabera pa msonkho. Nchifukwa chake ngakhale mwamanga nyumba za miyala yosema, simudzakhalamo. Ngakhale mwalima minda yabwino ya mphesa, simudzamumwa vinyo wake.
12
Ine ndikudziŵa kuchuluka kwa zolakwa zanu ndi kukula kwa machimo anu. Inu mumazunza anthu ochita chilungamo, mumalandira ziphuphu ndiponso mumapotoza milandu ya anthu osauka.
13
Nchifukwa chake pa nthaŵi yotere munthu wanzeru salankhulapo kanthu, chifukwa ndi nthaŵi yoipa.
14
Muike mtima pa zabwino osati pa zoipa, kuti mukhalebe ndi moyo. Apo Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, adzakhala nanu monga mwaneneramo.
15
Muzidana ndi zoipa, muzikonda zabwino. Mukhazikitse chilungamo m'mabwalo a milandu. Mwina mwake Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, adzakukomerani mtima inu anthu otsala a m'banja la Yosefe.
16
Nchifukwa chake zimene akunena Chauta, Ambuye, Mulungu Wamphamvuzonse, ndi izi: “M'mabwalo monse mudzakhala kulira, ndipo m'miseu monse anthu azidzangoti, ‘Mayo! Mayo!’ Ngakhale anthu wamba adzaŵaitana kuti adzalire, adzaitananso anthu odziŵa kubuma maliro kuti adzalire.
17
M'minda yonse ya mphesa mudzakhala kulira kokhakokha, pakuti ndidzakulanganidi nonsenu.” Akuterotu Chauta.
18
Tsoka kwa inu amene mumalilakalaka tsiku la Chauta! Kodi tsiku limenelo lidzakupinduliraninji inuyo? Kudzakhalatu mdima, osati kuŵala ai.
19
Kudzakhala monga m'mene kumachitira munthu akamathaŵa mkango, ndipo akumana ndi chimbalangondo, kapena monga munthu woti wakaloŵa m'nyumba, atsamira chipupa ndi dzanja lake, njoka nkumuluma.
20
Kodi suja tsiku la Chauta ndi mdima wokhawokha osati kuŵala, kodi suja lili ngati usiku wabii wopanda mpoti mbee pomwe!
21
Chauta akuti, “Masiku anu achikondwerero ndimadana nawo ndipo ndimaŵanyoza. Misonkhano yanu yachipembedzo siindikondwetsa konse.
22
Ngakhale mudzapereke nsembe zanu zopsereza ndiponso zaufa, Ine sindidzazivomera. Nsembe zanu zachiyanjano zophera ng'ombe zonenepa sindidzaziyang'ana nkomwe.
23
Musandisokose nazo nyimbo zanu zachipembedzo, sindingathe kupirira kulira kwa azeze anu.
24
Koma kuweruza kwanu kwangwiro kuziyenda kosalekeza ngati madzi, kulungama kwanu kukhale ngati mtsinje wosaphwa.
25
“Kodi inu anthu a ku Israele, zaka makumi anai zimene mudakhala m'chipululu, mudanditsirirako nsembe ndi kundipatsa mitulo?
26
Ndipotu muzidzanyamula Sakuti, mfumu yanu, ndi nyenyezi ija Kaiwani, mulungu wanu, mafano amene mudadzipangira.
27
Pakuti ndidzakupititsani ku ukapolo, kutali kupitirira mzinda wa Damasiko.” Akutero Chauta, amene dzina lake ndi Mulungu Wamphamvuzonse.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9