bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Amos 6
Amos 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 7 →
1
Tsoka kwa inu amene mumakhala mosatekeseka ku Ziyoni, ndiponso kwa inu amene mumakhala mosavutika ku Samariya. Tsoka kwa inu anthu otchuka pakati pa Aisraele, inu amene anthu onse amafika kwanu.
2
Pitani ku mzinda wa Kaline mukaone. Mupitenso ku Hamati mzinda wotchuka uja, tsono mutsikire ku Gati kwa Afilisti. Kodi Aisraelenu mukupambana anthu a mafumu ameneŵa? Kodi kapena dziko lao nlalikulu kupambana lanu?
3
Inu simulabadako zoti kudzafika tsiku lachilango, zochita zanu zimafulumizitsa nthaŵi yachiwawayo.
4
Tsoka kwa inu amene mumagona pa mabedi oŵakongoletsa ndi minyanga yanjovu, inu amene mumangoti lamzi pa mipando yanu, nkumachita phwando la nyama ya anaankhosa osakhwima ndi ya anaang'ombe onenepa.
5
Ntchito nkumangoimba azeze ngati Davide, ndi kumangopeka nyimbo zoimbira pa zing'wenyeng'wenye.
6
Tsoka kwa inu amene mumamwera vinyo m'zipanda zodzaza, inu amene mumadzola mafuta abwino kwambiri, koma simumva chisoni ndi kuwonongeka kwa dziko la Yosefe.
7
Nchifukwa chake mudzatsogola ndinu kupita ku ukapolo, ndipo maphwando ndi zikondwerero zidzakutherani.
8
Ambuye Chauta alumbira m'dzina lao kuti, “Ndikunyansidwa ndi zimene ana a Yakobe akunyadira, ndikudana nazo nyumba zao zazikulu. Ndithu ndidzapereka kwa adani ao likulu lao ndi zonse zam'menemo.”
9
Anthu khumi akadzakhala akubisala m'nyumba imodzi, nawonso adzafabe.
10
Mbale wake wa wina mwa akufawo, woyenera kusamala za maliro, adzafika kudzatulutsa mtembo m'nyumbamo. Tsono adzafunsa wina amene watsalakobe m'nyumbamo kuti, “Kodi uli ndi winanso wamoyo m'menemo?” Iyeyo adzayankha kuti, “Ai mulibiretu.” Ndipo mbaleyo adzati, “Khala chete, iwe! Tisayerekeze kutchula dzina la Chauta.”
11
Zoonadi, Chauta akadzangolamula, nyumba zikuluzikulu zidzagamukagamuka, ndipo nyumba zing'onozing'ono ndiye zidzangosanduka zibuma zokhazokha.
12
Kodi pa thanthwe akavalo nkuthamangapo? Kodi panyanja wina nkulimapo ndi ng'ombe? Komabe chilungamo mwachisandutsa chivumulo, ndipo zaungwiro mwazisandutsa zoŵaŵa.
13
Mukunyadira kuti mudagonjetsa mzinda wa Lodebara, mukunena kuti, “Kodi suja tidapambana mzinda wa Karinaimu ndi mphamvu zathu zokha?”
14
Koma Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse akuti, “Ndidzakuputirani anthu a mtundu wina kuti adzakuthireni nkhondo, inu Aisraele. Adzakuzunzani kuyambira ku Mpata wa Hamati kumpoto mpaka ku mfuleni wa Araba kumwera.”
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9