bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Amos 9
Amos 9
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
1
Tsono ndidaona Chauta ataima pambali pa guwa. Adati, “Gwetsani makapotolosi a Nyumba ya Mulungu, kuti maziko ake agwedezeke. Muŵagwetsere pamitu pa anthu. Onse otsalira Ine ndidzaŵapha pa nkhondo. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathaŵe. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzapulumukepo.
2
“Ngakhale akakumbe pansi mpaka ku malo a anthu akufa, dzanja langa lidzaŵadukhululako kumeneko. Ngakhale akakwere mpaka kumwamba, ndidzaŵatsakamutsako.
3
Ngakhale akabisale pamwamba pa phiri la Karimele, ndidzaŵaunguza nkuŵagwira. Ngakhale akabisale pansi pa nyanja yaikulu, ndidzalamula chilombo cham'nyanjamo kuti chiŵalume.
4
Ngakhale adani ao aŵakusire ku ukapolo, komweko ndidzalamula kuti aphedwe pa nkhondo. Ndidzaŵayang'anitsitsa kuti ziŵagwere zoipa osati zabwino.”
5
Ambuye Chauta Wamphamvuzonse, akakhudza dziko, limanyenyeka, ndipo zonse zokhala m'menemo zimalira. Apo dziko lonse limafufuma ngati mtsinje wa Nailo ndipo limateranso ngati mtsinje wa Nailo wa ku Ejipito.
6
Ndiwo amene amamanga malo ao okhalamo kumwamba, naika thambo ngati denga la dziko lapansi, amaitana madzi akunyanja naŵakhuthulira pa dziko lapansi. Iwowo dzina lao ndi Chauta.
7
“Kwa Ine, Aisraelenu muli ngati Aetiopiya.” Akuterotu Chauta. “Kodi sindine uja ndidatulutsa Aisraele ku Ejipito? Kodi sindine uja ndidatulutsa Afilisti ku Kafitori ndi Asiriya ku Kiri?
8
Ine, Ambuye Chauta, maso anga ali pa dziko lochimwalo, ndipo ndidzalifafaniza pa dziko lapansi. Komabe banja la Yakobe lokha sindidzaliwononga kotheratu.” Akuterotu Chauta.
9
“Ai, ndidzalamula, ndipo ndidzagwedeza Aisraele uku ndi uku pakati pa mitundu yonse ya anthu monga momwe amagwedezera sefa uku ndi uku, popanda kamwala nkamodzi komwe kogwa pansi.
10
Adzafera pa nkhondo anthu anga onse ochimwa, iwo amene amati, ‘Chilango sichidzatifika, kapena kutipambana.’ ”
11
Chauta akuti, “Nthaŵi imeneyo ndidzakwezanso ufumu wa Davide umene udagwa ngati nyumba. Ndidzakonzanso makoma ake ogumuka ndi kumanganso mabwinja ake. Ndidzaubwezeranso mwake mwakale.
12
Nthaŵi imeneyo Aisraele otsala adzagonjetsa zimene zatsala za ku Edomu, pamodzi ndi maiko onse amene amadziŵika ndi dzina langa.” Akuterotu Chauta, amene adzachitedi zimene wanenazi.
13
Chauta akunena kuti, “Nthaŵi ikubwera pamene mlimi adzabzola wokolola, ndipo woponda mphesa adzabzola wobzala mbeu. M'mapiri mudzatuluka vinyo wokoma, azidzachita kuyenderera pa zitunda zonse.
14
“Ndidzaŵabwezeranso pabwino anthu anga Aisraele. Adzamanganso mizinda yamabwinja ndi kumakhalamo. Adzalima minda ya mphesa ndipo adzamwa vinyo wake. Adzalima minda ndipo adzadya zipatso zake.
15
Ndidzaŵakhazikanso m'dziko mwao, ndipo palibe amene adzaŵachotsemo m'dziko limene ndidzaŵapatsalo.” Akuterotu Chauta, Mulungu wanu.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9