bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Amos 7
Amos 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 8 →
1
Izi ndizo zimene Ambuye Chauta adandiwonetsa m'masomphenya: Chauta ankapanga dzombe pa nthaŵi yoti mfumu inali itamweta kale udzu, ndipo udzuwo unkaphukanso kachiŵiri.
2
Pamene ndidaona kuti dzombelo ladya zomera zonse zam'dzikomo, ndidati, “Inu Ambuye Chauta, ndapota nanu, khululukani. Kodi anthu a Yakobeŵa angalimbike bwanji? Iwoŵa ndi ofooka kwambiri.”
3
Apo Chauta adakhululuka, ndipo adati, “Zimenezi sizidzachitika konse.”
4
Zina ndi izi zimene Ambuye Chauta adandiwonetsa m'masomphenya: Ambuye Chauta ankaitana malaŵi a moto kuti alange anthu. Motowo udapsereza phompho lalikulu, nuyamba kuwononga minda yonse ya pa dziko lapansi.
5
Tsono ine ndidati, “Inu Ambuye Chauta, ndapota nanu, basi lekani. Kodi anthu a Yakobeŵa angalimbike bwanji? Iwoŵa ndi ofooka kwambiri.”
6
Apo Chauta adakhululuka, ndipo adati, “Zimenezinso sizidzachitika konse.”
7
Zina ndi izi zimene Chauta adandiwonetsa m'masomphenya: Ndidaona Iye ataima pamwamba pa khoma lomangamanga, m'manja mwake ali ndi chingwe choongolera khoma.
8
Tsono Chautayo adandifunsa kuti, “Kodi iwe Amosi, nchiyani ukuwonachi?” Ine ndidayankha kuti, “Chingwe choongolera khoma.” Apo Chauta adati, “Ndikuika chingwe chimenechi pakati pa anthu anga Aisraele kuti kuwoneke kukhota kwao, choncho sindidzaŵalekereranso ai.
9
Akachisi a ana a Isaki adzasanduka bwinja, malo achipembedzo a Aisraele adzaonongedwa. Ndipo ndidzagwetsa banja la mfumu Yerobowamu pa nkhondo.”
10
Ku Betele kunali wansembe wina dzina lake Amaziya. Iyeyo adatumiza mthenga kwa Yerobowamu, mfumu ya ku Israele kuti, “Amosi akukuutsirani chiwembu pakati pa anthu a ku Israele. Anthu sangathe kuvomera zonse zimene iye akunenazo.
11
“Amosiyo akunena kuti, ‘Yerobowamu adzafa pa nkhondo, ndipo Aisraele adzatengedwa kunka ku ukapolo, kutali ndi dziko lao.’ ”
12
Tsono Amaziya adauza Amosi kuti, “Mlosi iwe, choka kuno! Thaŵira ku dziko la Yuda! Uzikalosa kumeneko, ndipo anthu akumeneko azikakudyetsa.
13
Koma usakalosenso ku Betele poti kumeneko ndi malo opatulika a mfumu, ndiponso ndi Nyumba ya Mulungu ya m'dziko lino.”
14
Amosi adayankha Amaziya kuti, “Ine sindine mneneri konse, kapenanso wa m'gulu la aneneri. Inetu ndine woŵeta nkhosa, ndiponso wolima nkhuyu.
15
Chauta adachita kukanditenga, kundileketsa ntchito yoŵeta nkhosa, nandiwuza kuti, ‘Pita, ukalalikire anthu anga, Aisraele.’
16
“Nchifukwa chake tsono imva mau amene Chauta akunena. Iweyo ukundiwuza kuti ndisalose zotsutsa Israele, ndisalalike zotsutsa banja la Isaki.
17
Tsono zimene akunena Chauta ndi izi: ‘Mkazi wako adzasanduka mkazi wadama mumzindamu. Ndipo ana ako aamuna ndi aakazi adzaphedwa pa nkhondo. Dziko lako adzaligaŵagaŵa kugaŵira anthu ena. Iweyo ukafera ku dziko lachikunja. Ndipo Aisraele adzatengedwa kunka ku ukapolo kutali ndi dziko lao.’ ”
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9