bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Amos 2
Amos 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 3 →
1
Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa Amowabu akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo adanyoza mafupa a mfumu ya ku Edomu poŵatentha mpaka kuŵasandutsa phulusa.
2
Nchifukwa chake Ineyo ndidzaponya moto ku Mowabu, ndipo motowo udzapsereza malinga a ku Keriyoti. Anthu a ku Mowabu adzafera pakati pa phokoso la nkhondo, asilikali akufuula ndi kuliza malipenga.
3
Ndidzaŵaphera wolamulira wao, Ndidzaphanso nduna zake pamodzi naye.” Akuterotu Chauta.
4
Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa anthu a ku Yuda akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo anyoza malamulo a Ine Chauta, ndipo sadatsate malangizo anga. Milungu yabodza imene makolo ao ankaipembedza yaŵasokeretsa.
5
Nchifukwa chake Ineyo ndidzaponya moto ku Yuda, ndipo motowo udzapsereza malinga a Yerusalemu.”
6
Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa anthu a ku Israele akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo amagulitsa anthu achilungamo ndi siliva, amagulitsa anthu osauka ndi nsapato.
7
Anthu osauka iwo amaŵadyera masuku pa mutu, anthu ozunzika iwo safuna kuŵayang'ana. Bambo ndi mwana amakagona ndi mdzakazi mmodzimmodzi, mwakuti amanyoza dzina langa loyera.
8
Anthuwo amagona pambali pa malo aliwonse opembedzerapo, pa zovala zimene adalandira kwa osauka ngati chikole. M'nyumba ya Mulungu amamweramo zakumwa za anthu amene adaŵalipitsa pa mlandu.
9
“Komabe ndine amene ndidaononga Aamori pamene Aisraele ankafika, ngakhale iwo aja anali ataliatali ngati mikungudza, ngakhale anali amphamvu ngati mitengo ya thundu. Ndidaŵaonongeratu zipatso zao m'mwamba ndiponso mizu yao pansi.
10
Inu Aisraele, ndine ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito. Ndine ndidakutsogolerani m'chipululu zaka makumi anai, kuti mukalande dziko la Aamori lija.
11
Ndipo ndine ndidasankha ena mwa ana anu kuti akhale aneneri, nkusankha ena mwa anyamata anu kuti akhale Anaziri. Kodi si choncho, inu anthu a ku Israele?” Akuterotu Chauta.
12
“Koma Inu mudaŵamwetsa vinyo Anaziri aja, ndipo mudaŵalamula aneneriwo kuti, ‘Musalose.’
13
“Mverani, ndidzakukanikizani pansi kwanuko, ndipo mudzalira ngati ngolo yodzaza ndi katundu wopitirira muyeso.
14
Waliŵiro sadzatha kuthaŵa, wanyonga sadzakhalanso ndi mphamvu. Wankhondo sadzapulumutsa moyo wake.
15
Munthu wamauta sadzalimbika. Wothamanga sadzapulumuka, ndipo wokwera pa kavalo sadzapulumutsa moyo wake.
16
Pa tsiku limenelo ngakhale wolimba mtima pakati pa anthu a mphamvu, adzathaŵa ali maliseche.” Akuterotu Chauta.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9