bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Amos 8
Amos 8
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 9 →
1
Zinanso zimene Ambuye Chauta adandiwonetsa m'masomphenya ndi izi: Panali dengu la zipatso zakupsa.
2
Chauta adandifunsa kuti, “Kodi iwe Amosi, nchiyani ukuwonachi?” Ine ndidayankha kuti, “Dengu la zipatso zakupsa.” Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Nthaŵi ya chimalizo yaŵakwanira anthu anga Aisraele, sindidzaŵakhululukiranso.
3
Nyimbo za m'Nyumba ya Mulungu zidzasanduka kulira pa tsiku limenelo. Mitembo ya anthu idzachuluka, ndipo adzaiponya ponseponse. Kudzangoti zii!” Akuterotu Ambuye Chauta.
4
Amosi adati, “Imvani izi, inu amene mumapondereza osoŵa, amene mufuna kuwononga anthu osauka am'dzikomu.
5
Inu mumadzifunsa kuti, ‘Kodi chikondwerero cha kukhala kwa mwezi chidzatha liti, kuti tigulitse dzinthu? Kodi tsiku lopumula la Sabata litha liti kuti tigulitsenso tirigu, kutinso tipeze mpata wochepetsera miyeso ndi kukweza mitengo, ndiponso kuti tichenjeretse anthu ndi masikelo onama,
6
kuti osauka tiŵagule ndi siliva, amphaŵi tiŵagule ndi nkhwaŵiro, kutinso tigulitse ndi mungu womwe wa tirigu?’ ”
7
Chauta, Mulungu amene ana a Yakobe amamnyadira walumbira kuti, “Ndithudi, sindidzaiŵala zochita zao zonse.
8
Chifukwa cha zonsezi dziko lapansi lidzagwedezeka, ndipo onse okhala m'menemo adzamva chisoni! Dziko lonse lapansi lidzagwedezeka ngati Nailo, lidzafufuma ndi kuteranso ngati mtsinje wa Nailo wa ku Ejipito.”
9
Ambuye Chauta akunena kuti, “Pa tsiku limenelo ndidzadetsa dzuŵa masana, ndidzagwetsa mdima pa dziko lapansi dzuŵa lili nye.
10
Zikondwerero zanu ndidzazisandutsa kulira, nyimbo zanu ndidzazisandutsa zamaliro. Ndidzakuvekani chiguduli nonsenu pathupi panu, ndipo mitu yanu yonse idzachita dazi. Mudzakhala ngati anakubala olira mwana wao mmodzi yekha. Tsiku limenelo lidzakhaladi loŵaŵa mpaka kutha kwake.”
11
Ambuye Chauta akunena kuti, “Nthaŵi ikubwera pamene ndidzagwetsa njala m'dzikomo. Siidzakhala njala ya buledi, kapena ludzu la madzi ai, koma njala yosoŵa mau a Chauta.
12
Anthu azidzangoyenda uku ndi uku kuchoka ku nyanja ina kunka ku nyanja inanso, azidzangoti piringupiringu kuchoka chakumpoto kunka chakuvuma. Azidzafunafuna mau a Chauta, koma osaŵapeza.
13
“Pa tsiku limenelo ngakhale anamwali abiriŵiri ndi anyamata asee adzakomoka ndi ludzu.
14
Onse amene amalumbira m'dzina la Asima, mulungu wa Samariya, nkumanena kuti, ‘Pali mulungu wa ku Dani!’ Kapena kuti, ‘Pali njira yopatulika ya ku Beereseba!’ Onsewo adzagwa osadzukanso.”
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9