bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Amos 4
Amos 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 5 →
1
Mverani mau aŵa akazi inu okhala ku Samariya amene mukungonenepa ngati ng'ombe za m'dera la Basani, inu amene mumavutitsa osauka ndi kuzunza osoŵa. Ntchito nkumangolamula amuna anu kuti, “Tipatseni zoziziritsa kukhosi.”
2
Ambuye Chauta, ndi kuyera kwao kuja, alumbira kuti, “Pali Ine ndemwe, masiku a chilango chanu akudza ndithu! Nthaŵiyo anthu adzakuguguzani ndi ngoŵe. Adzakukokani ndi mbedza nonse mpaka wotsiriza.
3
Mudzatulukira m'ming'alu ya malinga, aliyense payekhapayekha ndipo adzakutayani ku phiri la Halimoni.” Akuterotu Chauta.
4
“Bwerani ku malo oyera ku Betele, mudzachimwireko. Bweranazoni nsembe zanu m'maŵa mulimonse, bweranazoni zopereka zanu zachikhumi pa masiku atatu aliwonse.
5
Mupereke buledi wanu kuti muthokoze Mulungu. Munene poyera ndi kulengeza zopereka zanu zaufulu, pakuti nzimene mumakonda kuchita, inu Aisraele.” Akutero Chauta.
6
“Ndine amene ndidakusendetsani milomo m'mizinda yanu yonse. Ndine amene ndidagwetsa njala konse kumene munkakhala. Komabe simudabwerere kwa Ine.” Akutero Chauta.
7
“Ndinenso amene ndidamanga mvula patangotsala miyezi itatu kuti mukolole. Ndine amene ndinkagwetsa mvula pa mudzi wina, koma pa mudzi wina ai. Mvula inkagwa pa munda wina, koma munda wina nkumakhala gwa, chifukwa chosoŵa mvula.
8
Motero midzi iŵiri kapena itatu inkapita ku mudzi umodzi kuti ikamwe madzi, koma osaŵakwanira. Komabe simudabwerere kwa Ine.” Akutero Chauta.
9
“Ndidaumitsa mbeu zanu ndi matenda ndiponso ndi chinoni. Chidafotetsa mbeu za m'minda yanu yonse ndi yamphesa yomwe. Dzombe lidaononga mikuyu yanu ndi mitengo ya olivi, komabe simudabwerere kwa Ine.” Akutero Chauta.
10
“Ndidakugwetserani miliri yonga ya ku Ejipito ija. Ndidaphetsa achinyamata anu ku nkhondo, ndidapereka akavalo anu kwa adani. Ndidakununkhitsani fungo la mitembo lochokera ku misasa yanu yankhondo. Komabe simudabwerere kwa Ine.” Akutero Chauta.
11
“Ndidaononga ena mwa inu, monga momwe ndidaonongera Sodomu ndi Gomora. Otsaliranu munali ngati zikuni zofumula pa moto. Komabe simudabwerere kwa Ine.” Akutero Chauta.
12
“Tsono inu Aisraele ndidzakuteroni. Ndipo chifukwa choti ndidzakuchitani zimenezi, inu Aisraele, konzekani kuti mukumane ndi Mulungu wanu.”
13
Tsono tamvani, Iyeyo ndiye amene amaumba mapiri ndi kupanga mphepo, ndiye amene amaululira munthu za m'maganizo mwake, ndiye amene amasandutsa usana kuti ukhale usiku, ndiye amene amayenda pa zitunda za dziko lapansi. Dzina lake ndi Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9