bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Amos 3
Amos 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 4 →
1
Imvani mau amene Chauta adalankhula, mau okudzudzulani inu Aisraele, ndiye kuti banja lonse limene Iye adalitulutsa ku dziko la Ejipito. Adanena kuti,
2
“Ine ndidasankha ndi kusamala inu nokha pakati pa mitundu yonse ya pa dziko lapansi. Tsono ndidzakulangani koposa chifukwa cha machimo anu onse.”
3
“Kodi anthu aŵiri nkuyendera pamodzi, osapangana?
4
Kodi mkango umabangula m'nkhalango, usanagwire nyama? Kodi msona wa mkango umakhuluma m'phanga mwake, usanagwire kanthu?
5
Kodi mbalame nkukatera pa msampha pansi, popanda nyambo yake? Nanga msamphawo kodi nkufwamphuka pansipo, usanakole kanthu?
6
Kodi lipenga lankhondo nkulira mu mzinda, anthu osachita mantha? Nanga tsoka likagwera mzinda, kodi si Chauta amene amachita zimenezo?
7
Zoonadi, Ambuye Chauta sachita kanthu osadziŵitsa atumiki ao, aneneri, zimene akonzekera.
8
Mkango ukabangula, kodi sachita mantha ndani? Ambuye Chauta akalankhula, kodi ndani sadzalalika?”
9
“Ulengeze kwa anthu okhala m'malinga a ku Asidodi, ndiponso kwa okhala m'malinga a ku Ejipito, uŵauze kuti akasonkhane ku mapiri a ku Samariya, akaone zachipwirikiti ndi zachifwamba zimene zikuchitika pakati pa anthu ake.”
10
“Sadziŵa kuchita zolungama amene amadzaza malinga ao ndi zinthu zozipeza mwankhondo ndi mwakuba.” Akuterotu Chauta.
11
Nchifukwa chake Ambuye Chauta mau ao ndi aŵa: “Adani adzalizinga dzikolo, malinga ake adzaŵagwetsa, ndipo adzafunkha zonse zam'menemo.”
12
Zimene akunena Chauta ndi izi: “Monga mbusa amangotolako miyendo iŵiri kapena nsonga ya khutu la nkhosa yake ikajiwa ndi mkango, ndimo m'mene adzapulumukire Aisraele okhala ku Samariya, ngati zidutswa chabe za bedi.
13
“Mverani, muŵaimbe mlandu am'banja la Yakobe,” akutero Ambuye Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse.
14
“Pa tsiku limene ndidzalange Israele chifukwa cha zolakwa zake, maguwa a ku Betele ndidzaŵagumula, ndipo nyanga za guwa zidzathyoka nkugwa pansi.
15
Ndidzagwetseratu nyumba za nthaŵi yachisanu ndi za nthaŵi yamafundi. Nyumba zaminyanga zidzaonongeka, ndithu nyumba zazikulu zidzaphwasuka.” Akuterotu Chauta.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9