bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Genesis 12
Genesis 12
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 13 →
1
Ndipo Yehova anati kwa Abramu, Turuka iwe m'dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi ku nyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe;
2
ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukuru, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;
3
ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi,
4
Ndipo anamuka Abramu monga Yehova ananena kwa iye, ndipo Loti anamuka pamodzi naye: ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi awiri kudza zisanu, pamene anaturuka m'Harana.
5
Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wace, ndi Loti mwana wa mphwace, ndi cuma cao cimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala m'Harana; naturuka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani.
6
Ndipo Abramu anapitira m'dziko kufikira ku malo a Sekemu, kufikira ku mtengo wathundu wa ku More. Akanani anali m'dzikomo nthawi yomweyo.
7
Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye.
8
Ndipo iye anacoka kumeneko kunka ku phiri la kum'mawa kwa Beteli, namanga hema wace; Beteli anali kumadzulo, ndi Ai anali kum'mawa: kumeneko ndipo anammangira Yehova guwa la nsembe, naitanira dzina la Yehova.
9
Ndipo Abramu anayenda ulendo wace, nayendayenda kunka kumwela.
10
Ndipo munali njala m'dzikomo, ndipo anatsikira Abramo ku Aigupto kukakhala kumeneko, cifukwa kuti njala inali yaikuru m'dziko m'menemo.
11
Ndipo panali pamene anayandikira kulowa m'Aigupto, anati kwa Sarai mkazi wace, Taonani, ndidziwa kuti ndiwe mkazi wokongola maonekedwe ako;
12
ndipo padzakhala pamene adzakuona iwe Aaigupto, adzati, Uyu ndi mkazi wace: ndipo adzandipha ine, koma iwe adzakuleka ndi moyo.
13
Uzikanenatu, kuti iwe ndiwe mlongo wanga: kuti cidzakhala cabwino ndi ine, cifukwa ca iwe, ndi kuti moyo wanga usungike ndi iwe.
14
Ndipo panali pamene Abramu analowa m'Aigupto, Aaigupto anaona kuti mkazi anali wokongola kwambiri.
15
Ndipo akaronga ace a Farao anamuona iye, namyamikira iye kwa Farao; ndipo anamuka ndi mkazi kunyumba kwace kwa Farao.
16
Ndipo anamcitira Abramu bwino cifukwa ca iyeyo; ndipo anali nazo nkhosa, ndi ng'ombe, ndi aburu, ndi akapolo, ndi adzakazi, ndi aburu akazi, ndi ngamila.
17
Koma Yehova anabvutitsa Farao ndi banja lace ndi nthenda zazikuru cifukwa ca Sarai mkazi wace wa Abramu,
18
Ndipo Farao anaitana Abramu, nati, Nanga nciani ici wandicitira ine? cifukwa canji sunandiuza ine kuti ndiye mkazi wako?
19
Cifukwa canji unati, Ndiye mlongo wanga? Kotero ndinamtenga iye akhale mkazi wanga; tsopano suyu mkazi wako; mtenge nucoke.
20
Ndipo Farao analamulira anthu ace za iye; ndipo anamperekeza iye m'njira ndi mkazi wace ndi zonse anali nazo.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
Recommended Reading
Commentary
Genesis Commentaries
→
Devotional
Genesis Devotional Guide
→
Get This Bible
BL Study Bible
→