bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Genesis 7
Genesis 7
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 8 →
1
Ndipo anati Yehova kwa Nowa, Talowani, iwe ndi a ku nyumba ako onse m'cingalawamo; cifukwa ndakuona iwe kuti uli wolungama pamaso panga m'mbadwo uno.
2
Nyama zonse zodyedwa udzitengereko wekha zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yamphongo ndi yaikazi yace; ndi nyama zosadyedwa ziwiri ziwiri yamphongo ndi yaikazi yace.
3
Ndiposo mbalame za kumlengalenga zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yaimuna ndi yaikazi, kuti mbeu ikhale ndi moyo pa dziko lonse lapansi.
4
Pakuti akapita masiku asanu ndi awiri Ine ndidzabvumbitsa mvula pa dziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku; ndi zinthu zamoyo zonse zomwe ndazipanga ndidzaziononga pa dziko lapansi,
5
Ndipo anacita Nowa monga mwa zonse anamlamulira iye Yehova.
6
Ndipo Nowa anali wa zaka mazana asanu ndi limodzi, pamene cigumula ca madzi cinali pa dziko lapansi.
7
Ndipo analowa Nowa ndi ana ace ndi mkazi wace ndi akazi a ana ace m'cingalawamo, cifukwa ca madzi a cigumula.
8
Nyama zodyedwa ndi nyama zosadyedwa, ndi mbalame, ndi zonse zokwawa pansi,
9
zinalowa ziwiri ziwiri kwa Nowa m'cingalawamo, yamphongo ndi yaikazi, monga momwe Mulungu anamlamulira Nowa.
10
Ndipo panali pamene anapita masiku asanu ndi awiri, madzi a cigumula anali pa dziko lapansi.
11
Caka ca mazana asanu ndi limodzi ca moyo wa Nowa, mwezi waciwiri, tsiku la khumi ndi asanu ndi awiri la mwezi, tsiku lomwelo akasupe onse a madzi akuru anasefuka, ndi mazenera a kumwamba anatseguka.
12
Ndipo mvula inali pa dziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku.
13
Tsiku lomwelo analowa m'cingalawamo Nowa, ndi Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti, ana a Nowa, ndi mkazi wace wa Nowa, ndi akazi atatu a ana ace pamodzi nao:
14
iwo, ndi zamoyo zonse monga mwa mitundu yao, ndi zinyama zonse monga mwa mitundu yao, zokwawa zonse zokwawa pa dziko lapansi monga mwa mitundu yao, ndi zouluka zonse monga mwa mitundu yao, ndi mbalame zonse za mitundu mitundu.
15
Ndipo zinalowa kwa Nowa m'cingalawamo ziwiri ziwiri zamoyo zonse, m'mene muli mpweya wa moyo.
16
Zimene zinalowazo, zinalowa yamphongo ndi yaikazi zamoyo zonse, monga momwe Mulungu anamlamulira iye: ndipo Yehova anamtsekera iye.
17
Ndipo cigumula cinali pa dziko lapansi masiku makumi anai: ndipo madzi anacuruka natukula cingalawa, ndipo cinakwera pamwamba pa dziko lapansi.
18
Ndipo madzi anapambana, nacuruka ndithu pa dziko lapansi, ndipo cingalawa cinayandama pamadzi.
19
Ndipo madzi anapambana ndithu pa dziko lapansi; anamizidwa mapiri atari onse amene anali pansi pa thambo lonse.
20
Madzi anapambana ndithu nakwera mikono khumi ndi isanu: namizidwa mapiri,
21
Ndipo zinafa zamoyo zonse zoyenda pa dziko lapansi, zouluka, ndi nyama, ndi zamoyo, ndi zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi, ndi anthu onse:
22
zonse zimene m'mphuno zao munali mpweya wa maimu wa moyo, zonse zinali pamtunda, zinafa.
23
Ndipo zinaonongedwa zamoyo zimene zonse zinali pa dziko lapansi, anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndipo zinaonongedwa pa dzikolapansi: anatsala Nowayekha ndi amene anali pamodzi naye m'cingalawa.
24
Ndipo anapambana madzi pa dziko lapansi masiku zana kudza makumi asanu.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50