bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Genesis 9
Genesis 9
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 10 →
1
Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ace, nati kwa iwo, Mubalane, mucuruke, mudzaze dziko lapansi.
2
Kuopsya kwanu, ndi kucititsa mantha kwanu kudzakhala pa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi pa zouluka zonse za m'mlengalenga; ndi pa zonse zokwawa pansi, ndi pa nsomba zonse za m'nyanja, zapatsidwa m'dzanja lanu.
3
Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo.
4
Koma nyama, m'mene muli moyo wace, ndiwo mwazi wace, musadye.
5
Zoonatu mwazi wanu wa miyoyo yanu ndidzafuna; pa dzanja la zinyama zonse ndidzaufuna: ndi pa dzanja la munthu, pa dzanja la mbale wace wa munthu ndidzaufuna moyo wa munthu.
6
Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wace udzakhetsedwa: cifukwa m'cifanizo ca Mulungu Iye anampanga munthu.
7
Ndi inu, mubalane, mucuruke; muswane pa dziko lapansi, nimucuruke m'menemo.
8
Ndipo Mulungu ananena kwa Nowa ndi kwa ana ace pamodzi naye, kuti,
9
Ndipo Ine, taonani, Ine ndikhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu, ndi mbeu zanu pambuyo panu;
10
ndi zamoyo zonse ziti pamodzi ndi inu, zouluka, ng'ombe, ndi zinyama zonse za dziko lapansi, pamodzi ndi inu; zonse zoturuka m'cingalawa, zinyama zonse za dziko lapansi,
11
Ndipo ndidzakhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu; zamoyo zonse sizidzamarizidwanso konse ndi madzi a cigumula; ndipo sikudzakhalanso konse cigumula cakuononga dziko lapansi.
12
Ndipo anati Mulungu, Ici ndici cizindikiro ca pangano limene ndipangana ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse ziti pamodzi ndi inu, ku mibadwo mibadwo;
13
ndiika Uta-wa-Leza wanga m'mtambomo, ndipo udzakhala cizindikiro ca pangano lopangana ndi Ine ndi dziko lapansi.
14
Ndipo padzakhala popimba ndi mtambo Ine dziko lapansi, utawo udzaoneka m'mtambomo;
15
ndipo ndidzakumbukira pangano langa limene liri ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo; ndipo madzi sadzakhalanso konse cigumula cakuononga zamoyo zonse.
16
Ndipo utawo udzakhala m'mtambo; ndipo ndidzauyang'anira kuti ndikumbukire pangano lacikhalire liri ndi Mulungu ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo pa dziko lapansi.
17
Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Ici ndici cizindikiro ca pangano ndalikhazikitsa popaogana ndi Ine ndi zamoyo zonse za pa dziko lapansi.
18
Ndi ana amuna a Nowa amene anaturuka m'cingalawa ndiwo Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti: Hamu ndiye atate wace wa Kanani.
19
Amenewa ndiwo ana amuna atatu a Nowa: ndiwo anafalikira dziko lonse lapansi.
20
Ndipo anayamba Nowa kukhala munthu wakulima nthaka, ndipo analima munda wamphesa:
21
namwa vinyo wace, naledzera; ndipo anali wamarisece m'kati mwa bema wace.
22
Ndipo Hamu atate wace wa Kanani, anauona umarisece wa atate wace, nauza abale ace awiri amene anali kunja.
23
Semu ndi Yafeti ndipo anatenga copfunda, naciika pa mapewa ao a onse awiri, nayenda cambuyo, napfunditsa umarisece wa atate wao: nkhope zao zinali cambuyo, osaona umarisece wa atate ao.
24
Nowa ndipo anauka kwa kuledzera kwace, nadziwa cimene anamcitira iye mwana wace wamng'ono.
25
Ndipo anati, Wotembereredwa ndi Kanani: Adzakhala kwa abale ace kapolo wa akapolo:
26
Ndipo anati: Ayamikike Yehova, Mulungu wa Semu; Kanani akhale kapolo wace.
27
Mulungu akuze Yafeti, Akhale iye m'mahema a Semu; Kanani akhale kapolo wace.
28
Ndipo Nowa anakhala ndi moyo cigumula citapita, zaka mazana atatu kudza makumi asanu.
29
Ndipo masiku onse a Nowa anali mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu: ndipo anamwalira.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
Recommended Reading
Commentary
Genesis Commentaries
→
Devotional
Genesis Devotional Guide
→
Get This Bible
BL Study Bible
→