bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Genesis 34
Genesis 34
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 35 →
1
Ndipo Dina mwana wamkazi wa Leya, amene anambalira Yakobo, ananka kukaona akazi a kumeneko.
2
Pamene anamuona iye Sekemu, mwana wace wamwamuna wa Hamori Mhivi, karonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa,
3
Ndipo mtima wace unakhumba Dina mwana wace wamkazi wa Yakobo, ndipo anamkonda namwaliyo, nanena momkopa namwaliyo.
4
Ndipo anati Sekemu kwa atate wace Hamori kuti, Munditengere ine mkazi uyo akhale mkazi wanga.
5
Ndipo anamva Yakobo kuti anamuipitsa Dina, mwana wace wamkazi; ana ace amuna anali ndi zoweta zace kudambo: ndipo Yakobo anakhala cete mpaka anafika iwo.
6
Ndipo Hamori atate wace wa Sekemu anaturuka kunka kwa Yakobo kukanena ndi iye.
7
Ndipo pakumva ico ana ace amuna a Yakobo anabwera pocokera kudambo: amunawo ndipo anaphwetekwa mtima, nakwiya kwambiri, cifukwa iyeyo anacita copusa coipira Israyeli pakugona ndi mwana wamkazi wa Yakobo; ndico cosayenera kucita.
8
Ndipo Hamori ananena ndi iwo, kuti, Mtima wa Sekemu mwana wanga umkhumba mwana wako wamkazi: umpatsetu kuti akhale mkazi wace.
9
Mukwatirane ndi ife: tipatseni ife ana anu akazi, ndiponso dzitengereni ana athu akazi.
10
Ndipo mudzakhala pamodzi ndi ife, dziko lidzakhala pamaso panu; khalani m'menemo ndi kucita malonda, ndi kukhala nazo zanuzanu m'menemo.
11
Ndipo Sekemu anati kwa atate wace wa mkazi ndi kwa abale ace, Tipeze ufulu pamaso panu, cimene mudzanena kwa ine ndidzapereka.
12
Mundipemphe ine za mitulo ndi zaulere zambirimbiri, ndipo ndidzapereka monga mudzanena kwa ine; koma mundipatse ine namwaliyo akhale mkazi wanga.
13
Ndipo ana ace amuna a Yakobo anayankha Sekemu ndi Hamori atate wace monyenga, nanena, popeza anamuipitsa Dina mlongo wao,
14
nati kwa iwo, Sitingathe kucita ici, kupereka mlongo wathu kwa mwamuna wosadulidwa; cifukwa kumeneko ndiko kuticepetsa ife.
15
Koma apa pokha tidzakubvomerezani: ngati mudzakhala onga ife ndi kudulidwa amuna onse;
16
pamenepo tidzakupatsani inu ana athu akazi, ndipo tidzadzitengera ana anu akazi, ndipo tidzakhala pamodzi ndi inu, ndi kukhala mtundu umodzi.
17
Koma mukapanda kutimvera ndi kusadulidwa, pamenepo tidzatenga mwana wathu wamkazi, ndi kumuka naye.
18
Mau ao ndipo anakomera Hamori ndi Sekemu mwana wace wa Hamori.
19
Ndipo mnyamatayo sanacedwa kucicita popeza anakondwera ndi mwana wace wamkazi wa Yakobo; ndipo iye anali wolemekezedwa woposa onse a pa banja la atate wace.
20
Ndipo Hamori ndi Sekemu mwana wace anafika ku cipata ca mudzi wao, nalankhulana ndi anthu a mudzi wao, kuti,
21
Anthu amenewa ali amtendere pamodzi ndi ife; cifukwa cace akhale m'dzikomo, acite malonda m'menemo: pakuti taonani dzikololirilalikurulokwaniraiwo; tidzitengere ana ao akazi akhale akazi athu, tiwapatse amenewa ana athu akazi.
22
Anthuwo adzatiloleza ife tikhale nao anthu amodzi, pokhapo amuna onse a mwa ife adzadulidwa, monga iwo adulidwa.
23
Kodi ng'ombe zao ndi cuma cao ndi zoweta zao sizidzakhala zathu? Pokhapo tibvomerezana nao ndipo adzakhala pamodzi ndi ife.
24
Ndipo onse amene anaturuka pa cipata ca mudzi wao anamvera Hamori ndi mwana wace Sekemu, nadulidwa amuna onse akuturuka pa cipata ca mudzi wao.
25
Ndipo panali tsiku lacitatu pamene anamva kuwawa, ana amuna awiri a Yakobo, Simeoni ndi Levi, abale ace a Dina, anatenga wina lupanga lace wina lace, nalimbika mtima nalowa m'mudzi napha amuna onse.
26
Ndipo anapha Hamori ndi Sekemu mwana wace ndi lupanga, naturutsa Dina m'nyumba ya Sekemu nacoka naye.
27
Ndipo ana amuna a Yakobo anadzakwa ophedwa nafunkhamudzi cifukwa anamuipitsa mlongo wao.
28
Ndipo analanda nkhosa zao ndi zoweta zao ndi aburu ao, ndi za m'mudzi, ndi za m'munda;
29
ndi cuma cao conse ndi ana ao ndi akazi ao anawagwira, nafunkha zonse za m'nyumba.
30
Ndipo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, Mwaodisautsa ndi kundinunkhitsa ine mwa anthu okhala m'dzikomu, mwa Akanani ndi mwa Aperezi; ndipo ine ndine wa anthu owerengeka, adzandisonkhanira ine ndi kundikantha: ndipo ndidzapasulidwa ine ndi a pa nyumba yanga.
31
Ndipo iwo anati, Kodi iye ayenera kusandutsamloogo wathu wadama?
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 35 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
Recommended Reading
Commentary
Genesis Commentaries
→
Devotional
Genesis Devotional Guide
→
Get This Bible
BL Study Bible
→