bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Genesis 26
Genesis 26
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 27 →
1
Ndipo panali njala padzikopo, yoyenjezeka ndi njala yoyamba ija imene inali masiku a Abrahamu, ndipo Isake ananka kwa Abimeleke mfumu ya Afilisti ku Gerari.
2
Ndipo Yehova anamuonekera iye nati, Usatsikire ku Aigupto, khala m'dziko m'mene ndidzakuuza iwe;
3
khala mlendo m'dziko muno, ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndipo ndidzadalitsa iwe cifukwa kuti ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako maiko onse awa, ndipo ndidzalimbikitsa cilumbiriro ndinacilumbirira kwa Abrahamu atate wako;
4
ndipo ndidzacurukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, ndipo ndidzapatsa mbeu zako maiko onsewa; m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa;
5
cifukwa kuti Abrahamu anamvera mau anga, nasunga cilangizo canga, ndi maweruziro anga, ndi malemba anga ndi malamulo anga.
6
Ndipo Isake anakhala m'Gerari;
7
ndipo anthu a kumeneko anamfunsa iye za mkazi wace; ndipo iye anati, diye mlongowanga: cifukwa kuti anaopa kunena, Mkazi wanga; anati, anthu a kumeneko angandiphe ine cifukwa ca Rebeka; popeza anali wokongola pakumuona.
8
Ndipo panali atakhala komwe masiku ambiri, Abimeleke mfumu ya Afilisti, anayang'ana kunja kwa zenera, napenya, taona, Isake analinkuseka ndi Rebeka mkazi wace.
9
Ndipo Abimeleke anamuitana Isake nati, Taona, uyo ndi mkazi wako ndithu: kodi bwanji unati, Ndiye mlongo wanga? Ndipo Isake anati kwa iye, Cifukwa ndinati, Ndingafe cifukwa ca iye.
10
Ndipo Abimeleke anati, Nciani cimeneci waticitira ife? panatsala pang'ono ena a anthu akadagona naye mkazi wako, ndipo ukadaticimwitsa ife:
11
Ndipo Abimeleke anauza anthu ace, nati, Ali yense amene akhudza mwamuna uyo kapena mkazi wace, zoonatu adzaphedwa.
12
Ndipo Isake anabzala m'dzikomo, nalandira za makumi khumi caka cimeneco; ndipo Yehova anamdalitsa iye.
13
Ndipo anakula munthuyo, nakulakula kufikira kuti anakhala wamkurukuru:
14
ndipo anali ndi cuma ca nkhosa, ndi cuma ca zoweta, ndi banja lalikuru: ndipo Afilisti anamcitira iye nsanje.
15
Ndipo zitsime zonse anakumba anyamata a atate wace Afilisti anazitseka, nazikwirira ndi dothi.
16
Ndipo Abimeleke anati kwa Isake, Ucoke kwa ife cifukwa kuti iwe uti wamkuru wopambana ife.
17
Ndipo Isake anacoka kumeneko, namanga hema wace m'cigwa ca Gerari, nakhala kumeneko.
18
Ndipo Isake anafukulanso zitsime za madzi, anazikumba masiku a Abrahamu atate wace; cifukwa kuti Afilisti anazitseka atafa Abrahamu: ndipo anazicha maina monga maina omwe anazicha atate wace.
19
Ndipo anyamata a Isake anakumba m'cigwa, napeza kumeneko citsime ca madzi otumphuka.
20
Ndipo abusa a Gerari anakangana ndi abusa a Isake kuti, Madzi ndi athu; ndipo anacha dzina la citsimeco Eseke: cifukwa anakangana nave.
21
Ndipo anakumbanso citsime cina, ndipo anakangana naconso; nacha dzina lace Sitina.
22
Ndipo anacoka kumeneko nakumba citsime cina; koma sanakangana naco cimeneco; ndipo anacha dzina lace Rehoboti; ndipo anati, Cifukwa kuti tsopano Yehova anatipatsa ife malo, ndipo tidzabalana m'dziko muno.
23
Ndipo anacoka kumeneko nakwera kunka ku Beereseba,
24
Ndipo Yehova anamuonekera iye usiku womwewo, nati, Ine dine Mulungu wa Abrahamu atate wako; usaope, cifukwa kuti Ine ndiri ndi iwe, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kucurukitsa mbeu zako, cifukwa ca Abrahamu kapolo wanga.
25
Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, naitana dzina la Yehova, namanga hema wace kumeneko: ndi pamenepo anyamata a Isake anakumba citsime.
26
Ndipo ananka kwa iye Abimeleke kucokera ku Gerari, ndi Ahuzati bwenzi lace, ndi Fikoli, kazembe wa nkhondo yace.
27
Ndipo Isake anati kwa iwo, Mwandidzera cifukwa ciani, inu akundida ine, ndi kundicotsa kwanu?
28
Ndipo iwo anati, Kuona tinaona kuti Yehova ali ndi iwe; ndipo tinati, Tilumbiriranetu tonse awiri, ife ndi iwe, ticite pangano ndi iwe;
29
kuti usaticitire ife zoipa, pakuti sitidakhudza iwe, sitidakucirira kanthu koma kabwino ndiko, ndipo takulola umuke ndi mtendere; ndiwe tsopano wodalitsidwa ndi Yehova.
30
Ndipo anakonzera iwo madyerero, ndipo anadya namwa.
31
Ndipo analawira m'mamawa nalumbirirana wina ndi mnzace; ndipo Isake anawalola amuke, ndipo anauka kucokera kwa iye m'mtendere.
32
Ndipo panali tsiku lomwelo anyamata ace a Isake anadza namuuza iye za citsime cimene anakumba, nati kwa iye, Tapeza madzi.
33
Ndipo anacha dzina lace Seba, cifukwa cace dzina la mudziwo ndi Beereseba kufikira lero lino.
34
Pamene Esau anali wa zaka makumi anai, anakwatira Yuditi mwana wamkazi wa Beeri Mhiti, ndi Basemati mwana wamkazi wa Elone Mhiti:
35
ndipo iwo anapweteka mtima wa Isake ndi wa Rebeka.
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 27 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50