bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Genesis 4
Genesis 4
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 5 →
1
Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wace Hava: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.
2
Ndipo anabalanso mphwace Abele. Abele anakhala mbusa wa nkhosa, koma Kaini anali wakulima nthaka.
3
Ndipo panali atapita masiku, Kaini anatenga zipatso za nthaka, nsembe ya kwa Yehova.
4
Ndiponso Abele anatenga iyenso mwana woyamba wa nkhosa zace ndi mafuta omwe. Yehova ndipo anayang'anira Abele ndi nsembe yace:
5
koma sanayang'anira Kaini ndi nsembe yace. Kaini ndipo anakwiya kwambiri, niigwa nkhope yace.
6
Ndipo Yehova anati kwa Kaini, Ukwiyiranji? Yagweranji nkhope yako?
7
Ukacita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kucita zabwino, ucimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwace, ndipo iwe udzamlamulira iye.
8
Kaini ndipo ananena ndi Abele mphwace. Ndipo panali pamene anali kumunda, Kaini anamuukira Abele mphwace, namupha,
9
Yehova ndipo anati kwa Kaini, Ali kuti Abele mphwako? Ndipo anati, Sindidziwai: kodi ndine woyang'anira mphwanga?
10
Ndipo anati, Wacita ciani? Mau a mwazi wa mphwako andipfuulira Ine kunthaka.
11
Tsopano ndiwe wotembereredwa kunthaka, Imene inatsegula pakamwa pace kulandira pa dzanja lako mwazi wa mphwako:
12
pamene udzalima panthaka siidzaperekanso kwa iwe mphamvu yace: udzakhala wothawathawa ndi woyendayenda pa dziko lapansi.
13
Ndipo Kaini anati kwa Yehova, Kulangidwa kwanga nkwakukuru kosapiririka.
14
Taonani, mwandiingitsa ine lero lomwe padziko; ndi pankhope panu ndidzabisika; ndipo ndidzakhala wothawathawa ndi woyendayenda pa dziko lapansi; ndipo kudzatero kuti onse akundipeza adzandipha.
15
Ndipo Yehova anati kwa iye, Cifukwa cace ali yense amene adzapha Kaini kudzabwezedwa kwa iye kasanu ndi kawiri. Ndipo Yehova anaika icizindikiro pa Kaini, kuti asamuphe ali yense akampeza.
16
Ndipo Kaini anaturuka pamaso pa Yehova, ndipo anakhalam'dziko la Nodi, kum'mawa kwace kwa Edene.
17
Ndipo Kaini anamdziwa mkazi wace; ndipo anatenga pakati, nabala Enoke: ndipo anamanga mudzi, naucha dzina lace la mudziwo monga dzina la mwana wace, Enoke.
18
Kwa Enoke ndipo kunabadwa Irade; Irade ndipo anabala Mehuyaeli; Mehuyaeli ndipo anabala Metusaeli; Metusaeli ndipo anabala Lameke.
19
Ndipo Lameke anadzitengera yekha akazi awiri: dzina lace la wina ndi Ada, dzina lace la mnzace ndi Zila.
20
Ndipo Ada anabala Yabala; iye ndiye atate wao wa iwo okhala m'mahema, akuweta ng'ombe,
21
Ndi dzina la mphwace ndilo Yubala; iye ndiye atate wao wa iwo oyimba zeze ndi citoliro.
22
Ndipo Zila, iyenso anabala Tubala-Kaini, mwini wakuphunzitsa amisiri onse a mkuwa ndi a citsulo; mlongo wace wa Tubala-Kaini ndi Nama.
23
Lameke ndipo anati kwa akazi ace: Tamvani mau anga, Ada ndi Zila; Inu akazi a Lameke, mverani kunena kwanga: Ndapha munthu wakundilasa ine, Ndapha mnyamata wakundiphweteka ine,
24
Ngati Kaini adzabwezeredwa kasanu ndi kawiri, Koma Lameke makumi asanu ndi awiri.
25
Ndipo Adamu anadziwanso mkazi wace; ndipo anabala mwana wamwamuna, namucha dzina lace Seti: Cifukwa, nati iye, Mulungu wandilowezera ine mbeu yina m'malo mwa Abele amene Kaini anamupha,
26
Ndiponso kwa Seti, kwa iye kunabadwamwana wamwamuna: anamucha dzina lace Enosi: pomwepo anthu anayamba kuchula dzina la Yehova.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50