bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Genesis 48
Genesis 48
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 47
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 49 →
1
Ndipo panali zitapita izi, anthu anati kwa Yosefe, Taonani, atate wanu wadwala: ndipo iye anatenga ana ace amuna awiri, Manase ndi Efraimu, apite naye.
2
Ndipo anthu anamuuza Yakobo nati, Taonani, mwana wanu Yosefe alinkudza kwa inu; ndipo Yakobo anadzilimbitsa, nakhala tsonga pakama.
3
Ndipo Yakobo anati kwa Yosefe, a Mulungu Wamphamvuyonse anaonekera kwa ine pa Luzi m'dziko la Kanani nandidalitsa ine, nati kwa ine,
4
Taona, ndidzakubalitsa iwe, ndidzakucurukitsa iwe, ndidzakusandutsa iwe khamu la anthu a mitundu; ndipo ndidzapatsa mbeu yako ya pambuyo pako dziko ili likhale laolao cikhalire.
5
Tsopano ana ako amuna awiri, amene anakubadwira iwe m'dziko la Aigupto, ndisanadze kwa iwe ku Aigupto, ndiwo anga; Efraimu ndi Manase, monga Rubeni ndi Simeoni, ndiwo anga.
6
Koma obala iwe udzawabala pambuyo pao, ndiwo ako; awaphe dzina la abale ao m'colowa cao.
7
Tsono ine, pamene ndinacokera ku Padani, Rakele anamwalira pambali panga m'dziko la Kanani m'njira, itatsala nthawi yaing'ono tisadafike ku Efrati; ndipo ndidamuika iye pamenepo pa njira ya ku Efrati (ndiwo Betelehemu).
8
Ndipo Israyeli anayang'ana ana amuna a Yosefe, nati, Ndani awa?
9
Ndipo Yosefe anati kwa atate wace, Amenewa ndi ana anga, amene Mulungu wandipatsa ine pano. Ndipo iye anati, Udze naotu kwa ine, ndipo ndidzawadalitsa.
10
Koma maso a Israyeli anali akhungu m'ukalamba wace, ndipo sanathei kuona. Ndipo anadza nao pafupi; ndipo anapsompsona iwo, nawafungatira.
11
Ndipo Israyeli anati kwa Yosefe, Sindinaganizira kuti ndione nkhope yako: ndipo, taona, Mulungu wandionetsa ine mbeu zako zomwe.
12
Ndipo Yosefe anaturutsa iwo pakati pa maondo ace, nawerama ndi nkhope yace pansi.
13
Ndipo Yosefe anatenga iwo onse awiri, Efraimu m'dzanja lace lamanja ku dzanja lamanzere la Yakobo, ndi Manase m'dzanja lace lamanzere ku dzanja lamanja la Israyeli, nadza nao pafupi ndi iye.
14
Ndipo Israyeli anatambalitsa dzanja lace lamanja, naliika pa mutu wa Efraimu, amene ndiye wamng'ono, ndi dzanja lace lamanzere pa mutu wa Manase anapingasitsa manja ace dala; cifukwa Manase anali woyamba.
15
Ndipo anadalitsa Yosefe, nati, Mulungu, pamaso pace anayenda makolo anga Abrahamu ndi Isake, Mulungu amene anandidyetsa ine nthawi zonse za moyo wanga kufikira lero,
16
mthenga amene anandiombola ine ku zoipa zonse, adalitse anyamatawa; dzina langa lichulidwe pa iwo, ndi dzina la makolo anga Abrahamu ndi Isake; iwo akule, nakhale khamu pakati pa dziko lapansi.
17
Ndipo pamene Yosefe anaona kuti atate wace anaika dzanja lace lamanja pa mutu wa Efraimu, kudamuipira iye; ndipo anatukula dzanja la atate wace, kulicotsa pa mutu wa Efraimu ndi kuliika pa muta wa Manase.
18
Ndipo Yosefe anati kwa atate wace, Msatero atate wanga, cifukwa uyu ndi woyamba; ikani dzanja lanu lamanja pa mutu wace.
19
Koma anakana atate wace, nati, Ndidziwa mwananga, ndidziwa; Iyenso adzakhala mtundu wa anthu, iyenso adzakula; koma mphwace adzakhala wamkuru ndi iye, ndipo mbeu zace zidzakhala mitundu yambirimbiri.
20
Ndipo anadalitsa iwo tsiku lomwelo, nati, Mwa iwe Israyeli adzadalitsa, kuti, Mulungu akuyese iwe monga Efraimu ndi monga Manase; ndipo anaika Efraimu woyamba wa Manase.
21
Ndipo Israyeli anati kwa Yosefe, Taona, ndirinkufa ine; Mulungu adzakhala ndi iwe, adzakubwezanso iwe ku dziko la makolo ako.
22
Ndipo ine ndakupatsa iwe gawo limodzi loposa la abale ako, limene ndinalanda m'dzanja la Aamori ndi lupanga langa ndi uta wanga.
← Chapter 47
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 49 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
Recommended Reading
Commentary
Genesis Commentaries
→
Devotional
Genesis Devotional Guide
→
Get This Bible
BL Study Bible
→