bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Genesis 25
Genesis 25
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 26 →
1
Ndipo Abrahamu anatenga mkazi wina dzina lace Ketura.
2
Ndipo anambalira iye Zimerani ndi Yokesani ndi Medani, ndi Midyani, ndi Yisebaki, ndi Sua.
3
Ndipo Yokesani anabala Seba, ndi Dedani. Ana a Dedani ndi Aasuri, ndi Aletusi, ndi Aleumi.
4
Ana a Midyani: Efa, ndi Efere, ndi Hanoki, ndi Abida, ndi Elida. Onse amenewa ndi ana a Ketura.
5
Ndipo Abrahamu amwali anampatsa Isake zonse anali nazo.
6
Koma kwa ana a akazi ace ang'ono amene Abrahamu anali nao Abrahamu anapatsa mphatso, nawacotsa iwo kwa Isake mwana wace, akali ndi moyo, kuti anke kum'mawa, ku dziko la kum'mawa.
7
Masiku a zaka za moyo wace wa Abrahamu amene anakhala ndi moyo ndiwo zaka zana limodzi, kudza makumi asanu ndi limodzi, kudza khumi ndi zisanu.
8
Ndipo Abrahamu anamwalira, nafa m'ukalamba wace wabwino, nkhalamba ya zaka zambiri; natengedwa akhale ndi a mtundu wace.
9
Ndipo ana ace Isake ndi Ismayeli anamuika iye m'phanga la Makipela, m'munda wa Efroni mwana wace wa Zohari Mhiti, umene uli patsogolo pa Mamre;
10
munda umene anagula Abrahamu kwa ana a Heti: pamenepo anamuika Abrahamu ndi Sara mkazi wace.
11
Ndipo panali atafa Abrahamu, Mulungu anamdalitsa Isake mwana wace; ndipo Isake anakhala pa Beere-lahai-roi.
12
Mibadwo ya Ismayeli mwana wamwamuna wace wa Abrahamu, amene Hagara M-aigupto mdzakazi wa Sara anambalira Abrahamu ndi iyi:
13
ndipo maina a ana a Ismayeli, maina ao m'mibadwo yao ndi awa: woyamba wa Ismayeli ndi Nebayoti; ndi Kedara, ndi Abideele, ndi Mibisamu,
14
ndi Misima, ndi Duma; ndi Masa;
15
ndi Hadada, ndi Tema, ndi Yeturi, ndi Nafisi, ndi Kedema;
16
ana a Ismayeli ndi awa: maina ao m'midzi yao, m'misasa yao ndi awa: akaronga khumi ndi awiri m'mitundu yao.
17
Zaka za moyo wa Ismayeli ndi izi: zaka zana limodzi kudza makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri: ndipo iye anamwalira, natengedwa akhale ndi a mtundu wace.
18
Ndipo anakhala iwo kuyambira ku Havila kufikira ku Suri, ndiko kum'mawa kwace kwa Aigupto, pakunka ku Asuri: ndipo iye anakhala pamaso pa abale ace onse.
19
Mibadwo ya Isake mwana wace wa Abrahamu ndi iyi: Abrahamu anabala Isake:
20
ndipo Isake anali wa zaka makumi anai pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Msuriya wa ku Padanaramu, mlongo wace wa Labani Msuriya.
21
Ndipo Isake anampembedzera mkazi wace kwa Yehova popeza anali wouma: ndipo Yehova analola kupembedza kwace, ndipo Rebeka mkazi wace anatenga pakati,
22
Ndipo ana analimbana m'kati mwace: ndipo iye anati, Ngati cotero, ine ndikhala ndi moyo bwanji? ndipo ananka kukafunsa kwa Yehova.
23
Yehova ndipo anati kwa iye, Mitundu iwiri iri m'mimba mwako, Magulu awiri a anthu adzaturuka m'mimba mwako; Gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzace; Wamkuru adzakhala kapolo wa wamng'ono.
24
Atatha masiku ace akubala, taonani, amapasa anali m'mimba mwace.
25
Ndipo woyamba anabadwa wofiira, monse mwace monga maraya aubweya; ndipo anamucha dzina lace Esau.
26
Pambuyo pace ndipo anabadwa mphwace ndipo dzanja lace linagwira citende ca Esau, ndi dzina lace linachedwa Yakobo: ndipo Isake anali wa zaka makumi asanu ndi limodzi pamene mkazi wace anabala iwo.
27
Ndipo anakula anyamatawo; ndipo Esau anali munthu wakudziwa zakusaka nyama, munthu wa m'thengo; ndipo Yakobo anali munthu wofatsa, wakukhala m'mahema.
28
Ndipo Isake anakonda Esau, cifukwa anadya nyama yace ya m'thengo; koma Rebeka anakonda Yakobo,
29
Ndipo Yakobo anaphika mphodza: ndipo Esau anacokera kuthengo, nalefuka:
30
ndipo Esau anati kwa Yakobo, Undipatse ndidye cofiiraco; cifukwa ndalefuka: cifukwa cace anamucha dzina lace Edomu.
31
Ndipo Yakobo anati, Tigulane lero ukulu wako.
32
Ndipo Esau anati, Taona, ine ndifuna kufa: ukuluwo ndidzapindulanii nao?
33
Ndipo anati Yakobo, Undilumbirire ine lero lomwe, ndipo analumbirira iye; nagulana ndi Yakobo ukulu wace.
34
Ndipo Yakobo anampatsa Esau mkate ndi mphodza zophika; ndipo iye anadya, namwa, nanyamuka, napita; comweco Esau ananyoza ukulu wace.
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 26 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
Recommended Reading
Commentary
Genesis Commentaries
→
Devotional
Genesis Devotional Guide
→
Get This Bible
BL Study Bible
→