bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Genesis 20
Genesis 20
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 21 →
1
Abrahamu ndipo anacoka kumeneko kunka ku dziko la kumwera, ndipo anakhala pakati pa Kedesi ndi Suri, ndipo anakhala ngati mlendo m'Gerari.
2
Ndipo Abrahamu anati za Sara mkazi wace, Iye ndiye mlongo wanga: ndipo Abimeleke mfumu ya Gerari anatumiza namtenga Sara.
3
Koma Mulungu anadza kwa Abimeleke m'kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, cifukwa ca mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.
4
Koma Abimeleke sanayandikire naye; ndipo anati, Ambuye, kodi mudzaphanso mtundu wolungama?
5
Kodi iye sanati kwa ine, Ndiye mlongo wanga: ndipo mkazi iye yekha anati, iye ndiye mlongo wanga: ndi mtima wanga wangwiro ndi manja anga osacimwa ndacita ine ici.
6
Ndipo Mulungu anati kwa iye m'kulota, lode ndidziwa ine, kuti wacita ico ndi mtima wangwiro, ndipo lnenso ndinakuletsa iwe kuti usandicimwire ine: cifukwa cace sindinakuloleza iwe kuti umkhudze mkaziyo.
7
Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wace; cifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao.
8
Ndipo Abimeleke analawira m'mamawa, naitana anyamata ace onse, nanena zonse rimenezo m'makutu mwao, ndipo anthu anaopa kwambiri.
9
Ndipo Abimeleke anaitana Abrahamu, nati kwa iye, Waticitira ife ciani iwe? Ndakucimwiranji iwe kuti waufikitsa pa ine ndi pa ufumu wanga ucimo waukuru? Wandicitira ine zosayenera kuzicita.
10
Ndipo Abimeleke anati kwa Abrahamu, Unaona ciani iwe kuti wacita ici?
11
Ndipo Abrahamu anati, Cifukwa ndinati, Pompano palibe ndithu kumuopa Mulungu, ndipo adzandipha ine cifukwa ca mkazi wanga.
12
Koma ndiye mlongo wanga ndithu, mwana wa atate wanga, koma si mwana wa amai wanga: ndipo anakhala ndi ine mkazi wanga.
13
Ndipo panali pamene Mulungu anandiyendetsa ine kunyumba kwa atate wanga, ndinati kwa mkaziyo, Ici ndico cokoma mtima udzandicitire ine, konse kumene tidzafika ife, uzinena za ine, iye ndiye mlongo wanga.
14
Ndipo Abimeleke anatenga nkhosa ndi ng'ombe nd akapolo ndi adzakazi nampatsa Abrahamu, nambwezera iye Sara mkazi wace.
15
Ndipo Abimeleke anati, Taona dziko langa liri pamaso pako; kumene kuli kwabwino pamaso pako takhala kumeneko.
16
Kwa Sara ndipo anati, Taona, ndapatsa mlongo wako ndalama za siliva mazana khumi; taona, izo ndizo zoyeretsa maso za kwa onse amene ali ndi iwe: ndi pamaso pa onse ukhale wolungama.
17
Ndipo Abrahamu anapemphera Mulungu, ndipo Mulungu anaciritsa Abimeleke, ndi mkazi wace, ndi adzakazi ace; ndipo anabala ana.
18
Pakuti Yehova anatseketsa mimba yonse ya a m'nyumba ya Abimeleke, cifukwa ca Sara mkazi wace wa Abrahamu.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
Recommended Reading
Commentary
Genesis Commentaries
→
Devotional
Genesis Devotional Guide
→
Get This Bible
BL Study Bible
→