bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Genesis 32
Genesis 32
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 33 →
1
Ndipo Yakobo anankabe ulendo wace, ndipo amithenga a Mulungu anakomana naye.
2
Pamene Yakobo anawaona anati, Ili ndi khamu la Mulungu: ndipo anacha pamenepo dzina lace Mahanaimu.
3
Ndipo Yakobo anatumiza amithenga patsogolo pace kwa Esau mkuru wace, ku dziko la Seiri, ku dera la ku Edomu.
4
Ndipo anauza iwo kuti, Mukanene cotere kwa mbuyanga Esau: Atero Yakobo kapolo wako, ndakhala pamodzi naye Labani, ndipo ndakhalabe kufikira tsopano line:
5
ndipo ndiri nazo ng'ombe ndi aburu, ndi zoweta ndi akapolo ndi adzakazi, ndipo ndatumiza kukuuza mbuyanga kuti ndipeze ufulu pamaso pako.
6
Ndipo amithenga anabwera kwa Yakobo kuti, Tidafika kwa mbale wanu Esau, ndipo iyenso alinkudza kukomana nanu, ndipo ali nao anthu mazana anai.
7
Ndipo Yakobo anaopa kwambiri, nabvutidwa; ndipo anagawa anthu anali nao ndi nkhosa ndi zoweta, ndi ngamila, zikhale makamu awiri;
8
ndipo anati, Akafika Esau pa khamu limodzi nalikantha, linalo lotsala lidzapulumuka.
9
Ndipo Yakobo anati, Mulungu wa atate wanga Abrahamu, Mulungu wa atate wanga Isake, Yehova, amene munati kwa ine, Bwera ku dziko lako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakucitira iwe bwino:
10
sindiyenera zazing'ono za zifundo zonse, ndi zoona zonse, zimene mwamcitira kapolo wanu: cifukwa ndi ndodo yanga ndinaoloka pa Yordano uyu; ndipo tsopano ndiri makamu awiri.
11
Mundipulumutsetu ine m'dzanja la mkuru wanga, m'dzanja la Esau; cifukwa ine ndimuopa iye, kapena adzadza kudzandikantha ine, ndi amai pamodzi ndi ana.
12
Ndipo Inu munati. Ndidzakucitira iwe bwino ndithu, ndidzakuyesa mbeu yako monga mcenga wa pa nyanja yaikuru, umene sungathe kuwerengeka cifukwa ca unyinji wace.
13
Ndipo anagona komweko usiku womwewo, natengako zimene anali nazo, mphatso yakupatsa Esau mkuru wace:
14
mbuzi zazikazi mazana awiri, atonde makumi awiri, nkhosa zazikazi mazana awiri, ndi zazimuna makumi awiri,
15
ngamila zamkaka makumi atatu ndi ana ao, ng'ombe zazikazi makumi anai, zazimuna khumi, aburu akazi makumi awiri ndi ana khumi.
16
Ndipo anazipereka zimenezo m'manja a anyamata ace, gulu pa lokha gulu pa lokha: ndipo anati kwa anyamata ace, Taolokani patsogolo panga, tacitani danga pakati pa magulu, tina ndi lina.
17
Ndipo anauza wotsogolera kuti, Pamene akomana nawe mkuru wanga Esau ndi kufunsa iwe kuti, Ndiwe yani, umuka kuti? za yani zimenezi patsogolo pako?
18
pomwepo uziti, Za kapolo wanu Yakobo; ndizo mphatso yotumizidwa kwa mbuyanga Esau; taonani ali pambuyo pathu.
19
Ndipo anauzanso waciwiri ndi wacitatu, ndi onse anatsata magulu, kuti, Muzinena kwa Esau cotero, pamene mukomana naye:
20
ndiponso muziti, Ndiponso, taonani, kapolo wanu Yakobo ali pambuyo pathu, Pakuti anati, Ndidzampembedzera iye ndi mphatso imene ipita patsogolo panga, pambuyo pace ndidzaona nkhope yace; kapena adzandilandira ine.
21
Momwemo naolotsa mphatso patsogolo pace: ndipo iye yekha anagona usiku womwewo pacigono.
22
Ndipo anauka usiku womwewo, natenga akazi ace awiri, ndi adzakazi ace awiri, ndi ana ace amuna khumi ndi mmodzi, naoloka pa doko la Yaboki.
23
Ndipo anawatenga iwo nawaolotsa pamtsinje, naziolotsa zonseanalinazo.
24
Ndipo anatsala Yakobo yekha; ndipo analimbana naye munthu kufikira mbandakuca.
25
Ndipo pamene anaona kuti sanamlaka, anakhudza nsukunyu ya ncafu yace; ndipo nsukunyu ya ncafu yace ya Yakobo inaguluka, pakulimbana naye.
26
Ndipo iye anati Ndileke ndimuke, cifukwa kulinkuca. Ndipo Yakobo anati, Sindidzakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa ine.
27
Ndipo iye anati kwa Yakobo, Dzina lako ndani? Nati iye, Yakobo.
28
Ndipo anati, Dzina lako silidzachedwanso Yakobo, koma Israyeli, cifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.
29
Yakobo ndipo anafunsa iye, nati, Undiuze ine dzina lako. Ndipo iye anati, Undifunsa dzina cifukwa ninji? Ndipo anamdalitsa iye pamenepo.
30
Ndipo anacha dzina la malo amenewo, Penieli: cifukwa ndaonana ndi Mulungu nkhope ndi nkhope, ndipo wapulumuka moyo wanga,
31
Ndipo kudamcera iye pamene analoloka pa Penieli, ndipo iye anatsimphina ndi ncafu yace.
32
Cifukwa cace ana a Israyeli samadya ntsempha ya thako iri pa nsukunyu ya ncafu kufikira lero: cifukwa anakhudza nsukunyu ya ncafu ya Yakobo pa ntsempha ya thako.
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 33 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50