bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Acts 11
Acts 11
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 12 →
1
Koma atumwi ndi abale akukhala m'Yudeya anamva kuti amitundunso adalandira mau a Mulungu.
2
Ndipo pamene Petro adakwera kudza ku Yerusalemu, iwo akumdulidwe anatsutsana naye,
3
nanena kuti, Munalowa kwa anthu osadulidwa, ndi kudya nao.
4
Koma Petro anayamba kuwafotokozera chilongosolere, nanena,
5
Ndinali ine m'mudzi wa Yopa ndi kupemphera; ndipo m'kukomoka ndinaona masomphenya, chotengera chilikutsika, ngati chinsalu chachikulu chogwiridwa pangodya zake zinai; ndi kutsika kumwamba, ndipo chinadza pali ine;
6
chimenecho ndidachipenyetsetsa ndinachilingirira, ndipo ndinaona nyama za miyendo inai za padziko ndi zilombo, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga.
7
Ndipo ndinamvanso mau akunena ndi ine, Tauka Petro; ipha, nudye.
8
Koma ndinati, Iaitu, Ambuye; pakuti kanthu wamba, kapena konyansa sikanalowe m'kamwa mwanga ndi kale lonse.
9
Koma mau anayankha nthawi yachiwiri otuluka m'mwamba, Chimene Mulungu anachiyeretsa, usachiyesera chinthu wamba.
10
Ndipo ichi chinachitika katatu; ndipo zinakwezekanso zonse kumwamba.
11
Ndipo taonani, pomwepo amuna atatu anaima pa khomo la nyumba m'mene munali ife, anatumidwa kwa ine ochokera ku Kesareya.
12
Ndipo Mzimu anandiuza ndinke nao, wosasiyanitsa konse. Ndipo abale awa asanu ndi mmodzi anandiperekezanso anamuka nane; ndipo tinalowa m'nyumba ya munthuyo;
13
ndipo anatiuza ife kuti adaona mngelo wakuimirira m'nyumba yake, ndi kuti, Tumiza anthu ku Yopa, akaitane Simoni, wonenedwanso Petro;
14
amene adzalankhula nawe mau, amene udzapulumutsidwa nao iwe ndi apabanja ako onse.
15
Ndipo m'mene ndinayamba kulankhula, Mzimu Woyera anawagwera, monga anatero ndi ife poyamba paja.
16
Ndipo ndinakumbuka mau a Ambuye, kuti ananena, Yohanetu anabatiza ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.
17
Ngati tsono Mulungu anawapatsa iwo mphatso yomweyi yonga ya kwa ife, pamene tinakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, ndine yani kuti ndingathe kuletsa Mulungu?
18
Ndipo pamene anamva izi, anakhala duu, nalemekeza Mulungu, ndi kunena, Potero Mulungu anapatsa kwa amitundunso kutembenukira mtima kumoyo.
19
Pamenepo iwotu, akubalalika chifukwa cha chisautsocho chidadza pa Stefano, anafikira ku Fenisiya, ndi Kipro, ndi Antiokeya, osalankhula mau kwa wina yense koma kwa Ayuda okha.
20
Koma panali ena mwa iwo, amuna a ku Kipro, ndi Kirene, amenewo, m'mene adafika ku Antiokeya, analankhula ndi Agriki, ndi kulalikira Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu.
21
Ndipo dzanja la Ambuye linali nao; ndi unyinji wakukhulupirira unatembenukira kwa Ambuye.
22
Ndipo mbiri yao inamveka m'makutu a Mpingo wakukhala m'Yerusalemu; ndipo anatuma Barnabasi apite kufikira ku Antiokeya;
23
ameneyo, m'mene anafika, naona chisomo cha Mulungu, anakondwa; ndipo anawadandaulira onse, kuti atsimikize mtima kukhalabe ndi Ambuye;
24
chifukwa anali munthu wabwino, ndi wodzala ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro: ndipo khamu lalikulu lidaonjezeka kwa Ambuye.
25
Ndipo anatuluka kunka ku Tariso kufunafuna Saulo;
26
ndipo m'mene anampeza, anadza naye ku Antiokeya. Ndipo kunali, kuti chaka chonse anasonkhana pamodzi mu Mpingo, naphunzitsa anthu aunyinji; ndipo ophunzira anayamba kutchedwa Akhristu ku Antiokeya.
27
Koma masiku awa aneneri anatsika ku Yerusalemu kudza ku Antiokeya.
28
Ndipo ananyamuka mmodzi wa iwo, dzina lake Agabu, nalosa mwa Mzimu, kuti padzakhala njala yaikulu pa dziko lonse lokhalamo anthu; ndiyo idadza masiku a Klaudio.
29
Ndipo ophunzira, yense monga anakhoza, anatsimikiza mtima kutumiza zothandiza abale akukhala m'Yudeya;
30
ichonso anachita, natumiza kwa akulu mwa dzanja la Barnabasi ndi Saulo.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28